Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Zokhudza Inuyo

Kodi inuyo ndi ndani? Nanga mumayendera mfundo zotani? Ngati mungadzidziwe bwino, zingakuthandizeni kuti muzisankha nokha zochita m’malo moti anthu ena azikusankhirani.

Khalidwe Langa

Kodi Ndimayendera Mfundo Ziti?

Kudziwa mfundo zimene mumayendera, zimene mumachita bwino, zimene mumalakwitsa komanso zolinga zanu kungakuthandizeni kuti muzisankha bwino zochita mukapanikizika.

Kodi Ndili pa Ubwenzi ndi Yehova?

Kudziwa yankho la funsoli kungakuthandizeni kuthana ndi mavuto amene mukukumana nawo.

N’chifukwa Chiyani Sindikuyenera Kutsanzira Khalidwe la Anthu Omwe Amaonetsedwa M’mafilimu, pa TV ndi M’magazini?​—Gawo 1: Ya Atsikana

Achinyamata ambiri amaganiza kuti akuchita zinthu m’njira yawoyawo, koma amakhala akungotsanzira zochita za ena.

N’chifukwa Chiyani Sindikuyenera Kutsanzira Khalidwe la Anthu Omwe Amaonetsedwa M’mafilimu, pa TV ndi M’magazini?​—Gawo 2: Ya Anyamata

Kodi kutsanzira makhalidwe a anthu amene amasonyezedwa m’mafilimu, pa TV ndi m’magazini kungapangitse kuti anthu asamakopeke nanu?

Kodi Ndine Munthu Wodalirika?

Achinyamata ena amapatsidwa ufulu wambiri poyerekezera ndi anzawo ena. Kodi n’chiyani chimachititsa kuti pakhale kusiyana kotereku?

N’chifukwa Chiyani Tiyenera Kupewa Kunama ndiponso Kuba?

Kodi si zoona kuti anthu achinyengo zinthu zimawayendera bwino?

N’chifukwa Chiyani Muyenera Kukhala Oona Mtima?

Kodi mumafunika kunama kuti zinthu zikuyendereni bwino? Onani chifukwa chake kuchita zinthu moona mtima n’kothandiza kwambiri.

Kodi Ndinu Woona Mtima?

Dzifufuzeni pogwiritsa ntchito mafunso atatuwa.

Kodi Ndine Wopirira?

Aliyense amakumana ndi mavuto, choncho m’pofunika kuphunzira kukhala wopirira, ngakhale mavutowo atakhala aang’ono kapena aakulu.

Zimene Mungachite Zinthu Zikasintha

Zinthu zimasintha pamoyo. Onani zimene ena achita kuti azolowere zinthu zitawasinthira.

Kodi Mumatani Wina Akakupatsani Malangizo pa Zomwe Mwalakwitsa?

Kodi zingatheke bwanji kuti malangizo owawa kwambiri akhale othandiza kwambiri?

Kodi Ndizitani Munthu Wina Akandidzudzula?

Achinyamata ena amakhala ngati tambula yagalasi yomwe sichedwa kusweka moti akangodzudzulidwa ngakhale pa zinthu zazing’ono, amakwiya kwambiri. Kodi inunso mumatero?

Kodi Ndingaphunzitse Bwanji Chikumbumtima Changa?

Chikumbumtima chanu chimasonyeza kuti ndinu munthu wotani. Chimasonyezanso mfundo zimene mumakhulupirira. Ndiye kodi chikumbumtima chanu chimasonyeza zotani zokhudza inuyo?

Kodi Ndimafuna Kuti Ndisamalakwitse Chilichonse?

Kodi mungasiyanitse bwanji pakati pa kuyesetsa kuchita bwino ndi kuyesa kuchita zinthu zosatheka?

Zomwe Zingakuthandize Kuti Usamayembekezere Kuchita Zinthu Mosalakwitsa Chilichonse

Zoti muchitezi zikuthandizani kukhala ndi maganizo oyenera a zimene anthu ena komanso inuyo mungakwanitse kuchita.

Kodi Kukhala Munthu Wotchuka pa Intaneti Kuli Ndi Phindu?

Anthu ena amalolera kuika moyo wawo pangozi n’cholinga choti akhale ndi anthu ambiri owatsatira komanso okonda zimene aposita pa intaneti. Kodi kukhala wotchuka pa intaneti n’kothandizadi?

Kodi Ndingatani Kuti Ndisiye Kukhala Moyo Wachiphamaso?

Njira 4 zomwe zingakuthandizeni kuti musiye kukhala moyo wachinyengowu.

Kodi Mungatani Kuti Musamangotengera Zochita za Anzanu?

Munthu akhoza kuyamba kuchita zoipa chifukwa chotengera zochita za anzake. Zimene muyenera kudziwa zokhudza kutengera zochita za anzanu komanso zimene mungachite pothetsa vutoli.

Moyo Wanga Wachinyamata—Kodi Ndingapewe Bwanji Kutengera Zochita za Anzanga?

Onani mmene mfundo za m’Baibulo zingakuthandizireni kuti mukwanitse kulimbana ndi vutoli.

Musamangotengera Zochita za Anzanu

Zinthu 4 zimene zingakuthandizeni kuti muzisankha nokha zochita mwanzeru.

Musamachite Mantha Potsatira Zimene Mumakhulupirira

Werengani nkhaniyi kuti mudziwe chimene chinathandiza Yeremiya kulengeza uthenga wochenjeza anthu a ku Yuda.

Kodi Ndingasankhe Bwanji Munthu Wabwino Woti Ndizimutsanzira?

Kukhala ndi munthu woti muzimutsanzira kungakuthandizeni kupewa mavuto, kukwaniritsa zolinga zanu komanso kuti zinthu zizikuyenderani bwino. Kodi inuyo muyenera kutsanzira munthu wotani?

Mmene Mungasankhire Munthu Womutsanzira

Gawoli likuthandizani kuti mudziwe amene mungamutsanzire.

Zochita Zanga

N’chifukwa Chiyani Ndikufunika Kumathandiza Ena?

Kuchitira ena zabwino kumakuthandizani m’njira ziwiri. Kodi njira zimenezi ndi zotani?

Zimene Mungachite Kuti Muthandize Ena

Mukhoza kuthandiza anthu amene mumakhala nawo pafupi. Nkhani ino ili ndi njira zitatu zimene mungatsatire pokonza mapulani oti muthandize ena.

Kodi Ndizitani Ndikalakwitsa Zinazake?

Aliyense amalakwitsa koma si onse amene amaphunzirapo kanthu.

Kodi Ndingatani Kuti Ndisamagonje Poyesedwa?

Onani zinthu zitatu zimene zingakuthandizeni kuti musamagonje mukayesedwa.

Mungatani Kuti Musamagonje Mukakumana ndi Mayesero?

Mwamuna komanso mkazi weniweni amatha kupewa mayesero. Werengani nkhaniyi kuti mudziwe zinthu 6 zimene zingakuthandizeni kusagonja mukamayesedwa komanso kuti musakhale ndi nkhawa chifukwa chodziwa kuti mwagonja.

Mmene Ndimaonekera

Kodi Ndimakonda Kuvala Zovala Zotani?

Werengani nkhaniyi kuti mudziwe zokhudza maganizo olakwika amene anthu amakhala nawo pa nkhani ya mafasho.

Zovala Zimene Ndimakonda Kuvala

Pepalali lili ndi mfundo zimene zingakuthandizeni kuti muzivala zovala zoyenera.

Zimene Achinyamata Amanena pa Nkhani ya Maonekedwe

N’chifukwa chiyani achinyamata ambiri zimawavuta kuti azisangalala ndi mmene amaonekera? N’chiyani chingawathandize pa nkhaniyi?

Moyo Wanga Wachinyamata—N’chifukwa Chiyani Ndimadandaula Kwambiri za Mmene Ndimaonekera?

Dziwani zimene mungachite kuti musamadere nkhawa kwambiri zokhudza mmene mumaonekera.

Kodi Ndimangokhalira Kuganizira za Maonekedwe Anga?

Kodi mungatani kuti muzisangalala ndi mmene mumaonekera?

Kodi Ndiyeneradi Kudandaula Ndi Mmene Ndimaonekera?

Kodi mumakhumudwa mukadziyang’anira pagalasi? Kodi ndi zinthu ziti zimene muyenera kusintha?

Kodi Palibe Vuto Ngati Nditadzilemba Pathupi Langa?

N’chiyani chingakuthandizeni kuti musankhe mwanzeru pa nkhani imeneyi?