MFUNDO ZOTHANDIZA MABANJA | MABANJA
Kodi Mungatani Kuti Musamachitirane Nsanje M’banja?
Banja silingayende bwino ngati mwamuna ndi mkazi wake amakayikirana. Ndiye kodi mungatani kuti musamachitirane nsanje pa zifukwa zosamveka?
Zimene zili munkhaniyi
N’chiyani chimachititsa kuti anthu azikayikirana popanda zifukwa zenizeni?
Zomwe mungachite ngati mwamuna kapena mkazi wanu ndi wansanje
Kodi nsanje ndi chiyani?
Mawu akuti “nsanje,” ali ndi matanthauzo ambiri. Koma munkhaniyi, tikambirana mmene munthu amamvera mumtima chifukwa choganiza kuti munthu wina akufuna mwamuna kapena mkazi wake, kapenanso ngati akuganiza kuti mwamuna kapena mkazi wake akudyerera maso munthu wina. Zimenezi zikayamba kuchitika, timaona kuti banja lathu lili pangozi. Ngati zimenezi ndi zomwe zikuchitikadi, ndi pomveka kuchita nsanje ndipo si zolakwika kumva choncho. Paja banja ndi anthu awiri. Choncho mwamuna ndi mkazi wake ayenera kuchita chilichonse chotheka kuti ateteze banja lawo.
Mfundo ya m’Baibulo: “Moti sakhalanso kuti ndi awiri, koma thupi limodzi. Choncho chimene Mulungu wachimanga pamodzi, munthu asachilekanitse.”—Mateyu 19:6.
“Nsanje ili ngati chipangizo chokuchenjezani ngati pali chinachake chomwe chingasokoneze banja lanu, n’cholinga choti muchitepo kanthu zisanafike poipa.”—Benjamin.
Ngati munthu wina atamakayikira mwamuna kapena mkazi wake popanda zifukwa zenizeni, imeneyi ingakhale nsanje yosathandiza. Mukakhala ndi chikondi chenicheni mumapewa nsanje ya mtundu umenewu. (1 Akorinto 13:4, 7) Dr. Robert L. Leahy analemba kuti: “Zinthu zomwe anthu amachita chifukwa cha nsanje pomwe alibe umboni uliwonse wogwirika, ndi zimene zingasokoneze mgwirizano womwe akufuna kutetezawo.” a
N’chiyani chimachititsa kuti anthu azikayikirana popanda zifukwa zenizeni?
Munthu akhoza kukhala ndi nsanjeyi ngati mwamuna kapena mkazi wake wakale, ankamuzembera ndi munthu wina. Apo ayi, ngati banja la makolo ake linasokonekera chifukwa choti wina anali wosakhulupirika, ndipo nayenso akuopa kuti zikhoza kuchitikira banja lake.
“Ndili mwana, bambo anga ankawazembera mayi anga. Choncho kuyambira kale zimandivuta kukhulupirira munthu. Zinandisokoneza kwambiri maganizo moti nthawi zina zimafika posokoneza banja lathu.”—Melissa.
Chinanso chomwe chimayambitsa vutoli: Ngati umaopa kuti mwamuna kapena mkazi wako akhoza kukopekanso ndi anthu ena, n’zosavuta kuyamba kukayikira aliyense kuti akhoza kukusokonezera banja. Moti nthawi zina utha kumaganiza kuti ngati atapeza mpata, akhoza kukusiya n’kutengana ndi munthu wina.
“Mwamuna wanga anapemphedwa ndi mnzake kuti akagwirizire ukwati wake monga mnzake wamkwati. Kusonyeza kuti nthawi zina ankafunika kumakavina ndi mnzake wa mkwatibwi. Sizinandisangalatse, mpaka ndinamuletsa.”—Naomi.
Maukwati amachitika m’njira zosiyanasiyana potengera madera. Koma Akhristu amafunika kuyendera mfundo za m’Baibulo. Koma kodi zinalidi zomveka kuti Naomi akanize mwamuna wake kukagwirizira ukwati wa mnzake? Panopa amaona kuti anangochita nsanje pa zifukwa zosamveka. Iye anafotokoza kuti, “Ndinkangoopa. Ndinkaganiza kuti mwamuna wanga amandiyerekezera ndi akazi ena. Koma ndinalibe nazo umboni, zinali za m’mutu mwanga basi.”
Kaya nsanjeyi ibwere pa zifukwa zotani, koma ngati munthu akuchitira nsanje mwamuna kapena mkazi wake popanda zifukwa zomveka, amayamba kukayikira mnzakeyo kapenanso kumuimba mlandu kuti akumuzembera. Pamapeto pake zimatha kusokoneza banja lawo komanso thanzi lawo.
Mfundo ya m’Baibulo: “Nsanje ili ngati khansa.”—Miyambo 14:30, Baibulo la Easy-to-Read Version.
Mungatani ngati mukuchita nsanje?
Muzikhulupirira kwambiri mwamuna kapena mkazi wanu. M’malo mokhalira kufufuza kuti mupeze ngati mwamuna kapena mkazi wanu ndi wosakhulupirika, muziganizira kwambiri zimene amachita kuti muzimukhulupirira.
“Ndimaganizira makhalidwe abwino a mwamuna wanga. Akamamvetsera pomwe anthu akulankhula naye, chimakhala chifukwa choti amawadera nkhawa, osati chifukwa choti ali ndi maganizo olakwika. Ndimafunika kudzikumbutsa kuti ngati banja la makolo anga linali la mavuto, sizikutanthauza kuti banja langanso lizikumana ndi zomwezo.”—Melissa.
Mfundo ya m’Baibulo: “Chikondi . . . chimakhulupirira zinthu zonse.”—1 Akorinto 13:4, 7.
Muzisamala ndi zimene mumaganiza. Dr. Leahy yemwe tamutchula poyamba paja analembanso kuti: “Nthawi zambiri timaona kuti zomwe tikuganiza ndi zoona. Chifukwa choti tikukhulupirira zomwe tikuganizazo, timangoona ngati ndi umboni wa nkhaniyo. Koma kungokhulupirira kuti zinazake ndi zoona sikuchititsa kuti nkhaniyo ikhaledi yoona. Mmene tikumvera mumtima si umboni wokwanira wotsimikizira kuti nkhaniyo ndi yoona.” b
“Kuthamangira kuganiza kuti pakuchitika zinazake zolakwika tikangoona zinthu zimene zatikayikitsa, kutha kuyambitsa mavuto m’banja lathu.”—Nadine
Mfundo ya m’Baibulo: “Anthu onse adziwe kuti ndinu ololera.”—Afilipi 4:5
Kambiranani zimene zikukudetsani nkhawa. Kaya mukuchita nsanje pa zifukwa zotani, fotokozerani mwamuna kapena mkazi wanu nkhawa imene muli nayo. Zimenezi zingakuthandizeni kuti mukambirane mmene muzichitira zinthu, kuti aliyense azikhala womasuka komanso kuti asamadere nkhawa chilichonse. Ndiponso onetsetsani kuti zimene mwagwirizanazo zisakuchititseni kuti muzichita zinthu mopanikizika.
“Muzikambirana nkhanizi muli ndi maganizo akuti mnzanuyo alibe cholinga chilichonse chofuna kukupweteketsani mtima ndiponso kuti nayenso akufuna kuchita zoyenera. Muziona kuti mnzanuyo ali ndi zolinga zabwino. Mwina inuyo mumakhumudwa msanga kapenanso kuyembekezera kuti azichita zinazake zomwe sangakwanitse. Mwinanso n’kutheka kuti mwamuna kapena mkazi wanuyo sadziwa n’komwe kuti mumayembekezera kuti azikuchitirani zinazake.”—Ciara
Mfundo ya m’Baibulo: “Aliyense asamangofuna zopindulitsa iyeyo basi, koma zopindulitsanso ena.”—1 Akorinto 10:24.