Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

MFUNDO ZOTHANDIZA MABANJA | KULERA ANA

Nkhani Yovomereza Ana Kugwiritsa Ntchito Intaneti—Mbali 1: Kodi Mwana Wanga Azigwiritsa Ntchito Intaneti?

Nkhani Yovomereza Ana Kugwiritsa Ntchito Intaneti—Mbali 1: Kodi Mwana Wanga Azigwiritsa Ntchito Intaneti?

 Kafukufuku wina anapeza kuti achinyamata 97 pa 100 alionse amagwiritsa ntchito intaneti. Kodi mwana wanunso akufuna kuyamba kugwiritsa ntchito intaneti? Ngati ndi choncho, pali mfundo zingapo zimene mukuyenera kuziganizira.

Zimene zili munkhaniyi

 Mmene mwana wanu azigwiritsira ntchito nthawi

 Buku lina linanena kuti: “Malo ochezera a pa intaneti anakonzedwa m’njira yakuti muzikopeka ndi zomwe zimaikidwa pamalowa, kuti nthawi zonse muzikonda kumangokhala pa intaneti komanso kuti muzingokhalira kuona zinthu zatsopano zomwe zabwera.”—HelpGuide.

 “Ndikangolowa pa intaneti, ndimangozindikira kuti ndatha maola ambiri ndikutsegula zinthu zosiyanasiyana, chonsecho ndimangofuna kukhalapo maminitsi ochepa. Ndipo zimakhala zovuta kuti usiye foni pansi n’kuyamba kuchita zinthu zaphindu.”—Lynne, wazaka 20.

 Dzifunseni kuti: Kodi mwana wanga angakwanitse kutsatira malamulo amene ndingaike okhudza kuchuluka kwa nthawi imene angakhale pa intaneti? Kodi akhoza kudziikira yekha malamulo n’kumawatsatira?

 Mfundo ya m’Baibulo: “Samalani kwambiri mmene mukuyendera . . . [khalani] anzeru. Muzigwiritsa ntchito bwino nthawi yanu.”—Aefeso 5:15, 16.

Kulola mwana wanu kugwiritsa ntchito intaneti musanamupatse malangizo, kuli ngati kumulola kukwera hatchi musanamuphunzitse zoyenera kuchita

 Mmene mwana wanu azionera anthu ocheza nawo

 Intaneti imapangitsa munthu kuona ngati uli ndi anzako ambiri. Koma nthawi zambiri anzakowo sakhala enieni.

 “Ndinaona kuti achinyamata ambiri amaganiza kuti ngati anthu omwe amacheza nawo pa intaneti asonyeza kuti asangalala ndi zimene aika kapena ngati ali ndi anthu ambiri amene amawatsatira, amaona kuti ndi umboni wakuti anthu ambiri amawakonda, ngakhale kuti anthuwo sakuwadziwa n’komwe.”—Patricia, wazaka 17.

 Dzifunseni kuti: Kodi mwana wanga amazindikira kuti kukhala wotchuka pa intaneti kulibe phindu lililonse? Kodi amathanso kupeza anthu ocheza nawo pamasom’pamaso?

 Mfundo ya m’Baibulo: “Bwenzi lenileni limakukonda nthawi zonse, ndipo bwenzilo ndi m’bale amene anabadwira kuti akuthandize pakagwa mavuto.”—Miyambo 17:17.

 Mmene zingakhudzire maganizo a mwana wanu

 Ochita kafukufuku anapeza kuti anthu omwe amagwiritsa ntchito kwambiri intaneti amakhala ndi mavuto monga, kusowa ocheza nawo, kuda nkhawa komanso kuvutika maganizo.

 “Umakhumudwa kwambiri ukaona zithunzi zimene anzako aponya pa intaneti zosonyeza zomwe akuchita ali ndi anthu ena iwe kulibe.”—Serena, wazaka 19.

 Dzifunseni kuti: Kodi mwana wanga ndi wokhwima maganizo moti akhoza kupewa kumangoganizira za iye yekha, kukhala ndi mtima wampikisano kapenanso kukhudzidwa kwambiri ndi zimene ena akuchita pa intaneti?

 Mfundo ya m’Baibulo: “Tisakhale odzikuza, oyambitsa mpikisano pakati pathu, ndi ochitirana kaduka.”—Agalatiya 5:26.

 Zochita za mwana wanu akamagwiritsa ntchito intaneti

 Mukamagwiritsa ntchito intaneti, zimakhala zosavuta kuti anthu ena azikuvutitsani, kukutumizirani zinthu zokhudza kugonana ndiponso zolaula. Mwana wanu akhoza kukhudzidwa ndi vutoli ngakhale zitakhala kuti si iyeyo amene akuyambitsa.

 “Ndinaona kuti nkhani za pa intaneti sizichedwa kulowera kolakwika. Nthawi zambiri pamakhala mawu otukwana komanso nyimbo zoipa.”—Linda, wazaka 23.

 Dzifunseni kuti: Kodi mwana wanga ndi wokhwima maganizo moti akhoza kumagwiritsa ntchito intaneti bwinobwino? Kodi akhoza kulimba mtima kuti apewe zinthu zoipa zimene zingabwere pa intaneti?

 Mfundo ya m’Baibulo: “Dama ndi chonyansa chamtundu uliwonse kapena umbombo zisatchulidwe n’komwe pakati panu, . . . ngakhale za khalidwe lochititsa manyazi, nkhani zopusa kapena nthabwala zotukwana.”—Aefeso 5:3, 4.

 Kodi n’koyeneradi kuti azigwiritsa ntchito intaneti?

 Si kuti munthu amafunikira kukhala ndi intaneti kuti akhale ndi moyo wosangalala. Achinyamata ambiri amatha kukhala bwinobwino popanda kugwiritsa ntchito intaneti. Zimenezi zikuphatikizapo achinyamata ena amene poyamba ankaigwiritsa ntchito koma pano anasiya.

 “Nditaona mmene mchemwali wanga anasokonekera makhalidwe chifukwa chogwiritsa ntchito intaneti, ndinaganiza zongoisiya. Kuyambira nthawi imeneyo, ndimakhala wosangalala ndipo ndikuona kuti pali zambiri zomwe ndikusangalala nazo.”—Nathan, wazaka 17.

 Mfundo yofunika kwambiri: Musanalole kuti mwana wanu azigwiritsa ntchito intaneti, tsimikizirani kuti ndi wokhwima maganizo moti akhoza kumadziletsa kuti asamatherepo nthawi yambiri, akhoza kukhala ndi anzake abwino ndiponso kupewa zinthu zoipa zomwe zimaikidwa pamalowa.

 Mfundo ya m’Baibulo: “Munthu wochenjera amaganizira za mmene akuyendera.”—Miyambo 14:15.