Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

MFUNDO ZOTHANDIZA MABANJA

Kodi Ndingatani Ngati Nditamva Kuti Mwana Wanga Amavutitsidwa ndi Anzake?

Kodi Ndingatani Ngati Nditamva Kuti Mwana Wanga Amavutitsidwa ndi Anzake?

 Kodi mungatani ngati mwana wanu atakuuzani kuti mnzake wakusukulu amamuvutitsa? Kodi mungauze aphunzitsi ake kuti amulange mwana wovutitsayo? Kapena mungam’phunzitse mwana wanuyo mmene angamabwezerere? Musanasankhe zoyenera kuchita, ganizirani mfundo zotsatirazi.

 Zimene ndiyenera kudziwa zokhudza anthu ovutitsa anzawo

 Kodi kuvutitsa ena n’kutani? Ngati nthawi zonse munthu amakonda kumenya kapena kuchitira munthu wina zankhanza mwadala, ndiye kuti akumuvutitsa. Choncho si kuopsezedwa kulikonse kapena kunyozedwa kulikonse komwe tinganene kuti ndi kuvutitsidwa.

 Kodi kudziwa zoona n’kofunika bwanji? Anthu ena amaona kuti avutitsidwa akachitiridwa zilizonse zokhumudwitsa, ngakhale zitakhala zazing’ono. Choncho ngati mumalowerera nkhani zing’onozing’ono za ana, mosadziwa mungakhale mukuphunzitsa mwana wanuyo kuona kuti sangakwanitse kuthetsa mikangano payekha. Komatu luso lotha kuthetsa mikangano mwamtendere lingamuthandize panopa komanso akadzakula.

 Lemba lothandiza: “Usamafulumire kukwiya.”​—Mlaliki 7:9.

 Mfundo yofunika kwambiri: Ngakhale kuti mukhoza kulowerera pa nkhani zina zofunika, pena mukhoza kumusiya mwanayo kuti aphunzire kupirira komanso kuti adziwe zimene angamachite akasemphana maganizo ndi anthu ena.—Akolose 3:13.

 Nanga bwanji ngati mwana wanu atakuuzani kuti nthawi zonse anzake akumamuchitira nkhanza mwadala?

 Kodi ndingamuthandize bwanji?

  •   Muzimvetsera moleza mtima zimene mwana wanu akukuuzani. Muziyesetsa kudziwa (1) zomwe zikumuchitikira komanso (2) chifukwa chake anzake amamuvutitsa. Musafulumire kusankha zochita musanamvetse nkhani yonse. Dzifunseni kuti, ‘Kodi ndikudziwa zonse zokhudza nkhaniyi?’ Kuti mumvetse nkhani yonse, muyenera kufunsa aphunzitsi a mwana wanuyo kapena kholo la mwana wovutitsayo.

     Lemba lothandiza: “Munthu aliyense woyankhira nkhani asanaimvetsetse n’ngopusa, ndipo amachita manyazi.”​—Miyambo 18:13.

  •   Ngati mwana wanu amavutitsidwa, muthandizeni kudziwa kuti zimene amayankha kapena kuchita akamavutitsidwa zingathetse vutolo kapena kuliwonjezera. Mwachitsanzo, Baibulo limanena kuti: “Kuyankha modekha kumabweza mkwiyo, koma mawu opweteka amayambitsa mkwiyo.” (Miyambo 15:1) Apa mfundo ndi yoti, kubwezera kumachititsa kuti zinthu ziipe kwambiri, ndipo kungachititse kuti anzakewo azimuvutitsa kwambiri.

     Lemba lothandiza: “Osabwezera choipa pa choipa kapena chipongwe pa chipongwe.”​—1 Petulo 3:9.

  •   Mufotokozereni mwana wanuyo kuti kusabwezera si kutanthauza kuti ndi wofooka. M’malomwake, zimasonyeza kuti ali ndi mphamvu chifukwa wakwanitsa kuugwira mtima moti sanachite zimene winayo amafuna. Zimakhala ngati wagonjetsa munthuyo popanda kulimbana naye.

     Mfundoyi ndi yofunikanso kwambiri ngati mwana wanu amavutitsidwa pa intaneti. Mwana wanu akamabwezera mawu onyoza omwe anthu omuvutitsa akumutumizira pa intaneti, zingachititse kuti omuvutitsawo apitirizebe. Ndipo mwana wanuyo akhoza kumaonekanso ngati wovutitsa anzake. Popewa zimenezi, nthawi zambiri ndi bwino kungokhala chete osayankha chilichonse. Kutsatira njira imeneyi kungachititse kuti anthuwo agwe ulesi n’kusiya kumuvutitsa mwana wanuyo.

     Lemba lothandiza: “Popanda nkhuni moto umazima.”​—Miyambo 26:20.

  •   Nthawi zina, n’zotheka mwana wanuyo kupewa anthu omwe angamuvutitse komanso malo amene n’zosavuta kuvutitsidwa ndi ena. Mwachitsanzo, ngati atadziwa kumene anthu ovutitsawo amapezeka, angachite bwino kudutsa njira ina.

     Lemba lothandiza: “Wochenjera ndi amene amati akaona tsoka amabisala, koma anthu osadziwa zinthu amangopitabe ndipo amalangidwa.”​—Miyambo 22:3.

Mukhoza kukambirana ndi aphunzitsi a mwana wanuyo kapena kholo la mwana wovutitsayo

 TAYESANI KUCHITA IZI: Thandizani mwana wanu kuti aganizire ubwino ndi kuipa komwe kungakhalepo ngati atachita zotsatirazi. Mwachitsanzo:

  •  Kodi chingachitike n’chiyani ngati atamangonyalanyaza omuvutitsawo?

  •  Nanga bwanji ngati atauza omuvutitsawo kuti amusiye?

  •  Bwanji ngati atakanena kwa aphunzitsi ake?

  •  Kodi angathe “kudziteteza” kwa omuvutitsawo pongochita zinthu mwanthabwala?

 Kaya mwana wanu amavutitsidwa pamasom’pamaso kapena pa intaneti, dziwani kuti kuvutitsidwa ndi nkhani yaikulu. Choncho muziyesetsa kukambirana naye njira yabwino yomwe ingamuthandize. Ndipo muzimutsimikizira kuti mupitiriza kumuthandiza mpaka vutolo litatha.

 Lemba lothandiza: “Bwenzi lenileni limakukonda nthawi zonse, ndipo bwenzilo ndi m’bale amene anabadwira kuti akuthandize pakagwa mavuto.”​—Miyambo 17:17.