Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

MFUNDO ZOTHANDIZA MABANJA | BANJA

Muziona Moyenera Zinthu Zimene Zimakukwiyitsani

Muziona Moyenera Zinthu Zimene Zimakukwiyitsani
  •   Mumakonda kungochita zimene mwaganiza osakonzekera koma mnzanu amakonda kukonzekera chilichonse.

  •   Mumakonda kukhala phee ndipo ndinu wamanyazi koma mnzanu ndi womasuka ndipo amakonda kucheza pagulu.

 Kodi mwamuna kapena mkazi wanu amachita zinthu zimene zimakukwiyitsani? Kuganizira kwambiri zinthuzi kungasokoneze banja lanu. Paja Baibulo limanena kuti: “Amene amangokhalira kulankhula za nkhani inayake amalekanitsa mabwenzi apamtima.”​—Miyambo 17:9.

 Musalole kuti zinthu zimene zimakukwiyitsani zichititse kuti inu ndi mwamuna kapena mkazi wanu musamagwirizane. M’malomwake, muziyesetsa kuona zinthuzo moyenera.

Zimene zili m’nkhaniyi

 Kuona moyenera zinthu zimene zimakukwiyitsani

 Mwina zinthu zimene mnzanu amachita zomwe zimakukwiyitsani ndi mbali ina chabe ya khalidwe limene mumalikonda. Taganizirani zitsanzo zitatu izi:

 “Nthawi zambiri mwamuna wanga amachedwa kumaliza zinthu komanso kukonzekera akafuna kupita kwinakwake. Koma khalidwe lomweli limamuthandiza kuti azindilezera mtima. Nthawi zina, ndimakwiya iye akachedwa koma pa nthawi imodzimodziyo khalidweli ndi limodzi mwa makhalidwe ake omwe ndimawakonda.”​—Chelsea.

 “Mkazi wanga akamakonzekera zinthu amaganizira chinthu china chilichonse. Iye amafuna kuti zinthu zonse zikhale pamalo ake ndipo nthawi zina zimenezi zimandikwiyitsa. Koma khalidwe limeneli limamuthandizanso kuti nthawi zonse akhale wokonzeka.” ​—Christopher.

 Nthawi zina, ndimaona kuti mwamuna wanga amachita mphwayi ndipo zimandikwiyitsa. Komabe ndimaona kuti sapanikizika ndipo zimenezi n’zomwe zinandichititsa kuyamba kumukonda. Ndimasangalala kwambiri kuti zinthu zikavuta mtima wake umakhalabe m’malo.” ​—Danielle.

 Mogwirizana ndi zimene Chelsea, Christopher ndi Danielle ananena, nthawi zambiri zinthu zimene mnzanu amachita zomwe zimakukwiyitsani zimangokhala mbali ina ya khalidwe labwino limene ali nalo. Choncho ngati atasiya zimene zimakuvutitsanizo, ndiye kuti anasiyenso zinthu zabwino zimene amachitazo. Zimenezi n’zofanana ndi mmene zilili ndi ndalama yachitsulo. Simungathe kungotaya mbali imodzi chabe popanda kutayanso mbali inayo.

 Koma n’zoona kuti makhalidwe ena sakhala ndi mbali ina yabwino. Mwachitsanzo, Baibulo limanena kuti anthu ena ‘amakonda kukwiya.’ (Miyambo 29:22) Ngati munthu ali ndi vutoli, ayenera kuchita zonse zimene angathe kuti asiye “kuwawidwa mtima konse kwa njiru, kupsa mtima, mkwiyo, kulalata ndiponso mawu achipongwe.” a​—Aefeso 4:31.

 Koma ngati mnzanu ali ndi khalidwe lina lomwe si loipa kwambiri kungoti simusangalala nalo, muzitsatira malangizo a m’Baibulo akuti: “Pitirizani kulolerana . . . ngati wina ali ndi chifukwa chodandaulira za mnzake.”​—Akolose 3:13.

 Kuwonjezera pamenepa, muziyesetsa kuona mbali ina yabwino ya khalidwe lomwelo. Mwina mbali imeneyo ndi yomwe inachititsa kuti mukopeke ndi mwamuna kapena mkazi wanu. Mwamuna wina dzina lake Joseph anati, “Kuganizira kwambiri zinthu zimene zimakukwiyitsani kuli ngati kungoona mbali yakuthwa ya dayamondi osaona kuwala kwake kokongola.”

 Mafunso othandiza pokambirana

 Aliyense aganizire kaye payekha mmene angayankhire mafunso otsatirawa. Kenako mungakambirane limodzi mayankho anu.

  •   Kodi mnzanu ali ndi khalidwe limene mukuona kuti likusokoneza banja lanu? Ngati zili choncho, kodi ndi khalidwe liti?

  •   Kodi khalidweli ndi loipadi kapena limangokutopetsani?

  •   Nanga kodi khalidweli lili ndi mbali ina yabwino? Ngati zili choncho, kodi mbaliyo ndi yotani, nanga n’chifukwa chiyani mumaikonda?