Kodi Anefili Anali Ndani?
Yankho la m’Baibulo
Anefili anali ana amene angelo oipa anaberekerana ndi akazi ena m’nthawi ya Nowa ndipo anali amphamvu kuposa munthu wina aliyense. a
Baibulo limafotokoza kuti “ana a Mulungu woona anayamba kuona kuti ana aakazi a anthu anali okongola.” (Genesis 6:2) ‘Ana a Mulungu’ amenewa anali angelo amene anapandukira Mulungu pamene “anasiya malo awo okhala” kumwamba, n’kudziveka matupi a anthu. Atachita zimenezi “anayamba kudzitengera okha akazi alionse amene anawasankha.”—Yuda 6; Genesis 6:2.
Ana amene anabadwawo anali ziphona zomwe zinali zosiyana kwambiri ndi ana ena onse chifukwa choti bambo awo anali angelo. (Genesis 6:4) Anefili anali ziphona zankhanza kwambiri zomwe zinadzadza dziko lonse ndi chiwawa. (Genesis 6:13) Ndipo Baibulo limafotokoza kuti anali “ziphona zakalelo, amuna otchuka.” (Genesis 6:4) Iwo anachititsa kuti anthu enanso ayambe kuchita zachiwawa komanso azikhala mwa mantha.—Genesis 6:5; Numeri 13:33. b
Maganizo olakwika okhudza Anefili
Maganizo olakwika: Padzikoli padakali Anefili masiku ano.
Zoona zake: Yehova anapangitsa kuti padziko pachitike chigumula chimene chinapha anthu onse a chiwawa m’nthawi ya Nowa. Anefili nawonso anaphedwa pamodzi ndi anthu onse oipa. Komabe, Yehova anachitira chifundo Nowa ndi banja lake ndipo ndi okhawo amene anapulumuka pa nthawiyo.—Genesis 6:9; 7:12, 13, 23; 2 Petulo 2:5.
Maganizo olakwika: Bambo awo a Anefili anali anthu.
Zoona zake: Baibulo limanena kuti bambo awo anali “ana a Mulungu woona.” (Genesis 6:2) Mawu akuti “ana a Mulungu woona” amanena za angelo. (Yobu 1:6; 2:1; 38:7) Angelowa anali ndi mphamvu zotha kusintha matupi awo n’kukhala ngati anthu. (Genesis 19:1-5; Yoswa 5:13-15) Mtumwi Petulo ananenapo za “mizimu imene inali m’ndende, imene inali yosamvera pa nthawi imene Mulungu anali kuleza mtima m’masiku a Nowa.” (1 Petulo 3:19, 20) Nayenso Yuda anafotokoza za angelo ena amene “sanasunge malo awo oyambirira koma anasiya malo awo okhala.”—Yuda 6.
Maganizo olakwika: Anefili anali angelo ochimwa.
Zoona zake: Nkhani ya pa Genesis 6:4 imasonyeza kuti Anefili sanali angelo koma kuti anali ziphona zomwe zinabadwa pambuyo poti angelo omwe anasintha matupi awo agonana ndi akazi. Angelowa ‘atayamba kudzitengera okha akazi alionse amene anawasankha,’ Yehova ananena kuti pambuyo pa zaka 120 iye awononga anthu onse oipa omwe anali padziko. (Genesis 6:1-3) Nkhaniyi imanenanso kuti “m’masiku amenewo,” angelo oipawa anapitiriza “kugona ndi ana aakazi a anthu” ndipo anabereka ana. Anawo anali “ziphona zakalelo,” omwe ndi Anefili.—Genesis 6:4.
a Dzina lakuti “Anefili” limachokera ku liwu la Chiheberi lomwe limatanthauza kuti “Ogwetsa.” Buku lina linanena kuti liwu limeneli limanena za anthu omwe “amagwera anthu ena mwachiwawa ndi kuwavulaza, ndipo amachititsa kuti enawo agwenso.”—Wilson’s Old Testament Word Studies.
b Zikuoneka kuti azondi a Chiisraeli omwe ananena mawu a pa Numeri 13:33 anaona anthu amene kukula kwawo kunawakumbutsa za nkhani yokhudza Anefili, omwe anali atamwalira zaka zambiri m’mbuyomo.—Genesis 7:21-23.