Kodi Baibulo Lingandithandize Ngati Ndili ndi Nkhawa?
Yankho la m’Baibulo
Inde. Tikutero chifukwa chakuti Mulungu ndi amene angatithandize kwambiri. Pajatu Baibulo limati: “Mulungu, amene amatonthoza mtima wopsinjika, anatitonthoza ife mtima.”—2 Akorinto 7:6, Chipangano Chatsopano mu Chichewa cha Lero.
Zimene Mulungu amapereka kuti atithandize
Mphamvu. Mulungu ‘amatitonthoza’ poyankha mapemphero athu opempha mphamvu kuti tipirire osati pongochotsa mavutowo. (Afilipi 4:13) Musakayikire kuti Mulungu ndi wokonzeka kumvetsera mapemphero anu. Baibulo limati: “Yehova ali pafupi ndi anthu a mtima wosweka. Ndipo odzimvera chisoni mumtima mwawo amawapulumutsa.” (Salimo 34:18) Mulungu amamvetsa zimene mukufuna kunena ngakhale pamene mukusowa mawu oti mufotokozere mmene mukumvera mumtima.—Aroma 8:26, 27.
Zitsanzo za m’Baibulo. Munthu wina amene analemba nawo Baibulo anapemphera kuti: “Pa nthawi imene zinthu zinandivuta kwambiri ndinaitana pa inu.” Iye analimbikitsidwa atakumbukira kuti Mulungu amafunitsitsa kutikhululukira. Ananena kwa Mulungu kuti: “Mukanakhala kuti mumayang’anitsitsa zolakwa, ndani akanaima pamaso panu, inu Yehova? Inu mumakhululukiradi, kuti anthu akuopeni.”—Salimo 130:1, 3, 4.
Chiyembekezo. Masiku ano, Mulungu amatitonthoza komanso walonjeza kuti adzachotsa mavuto onse amene amatidetsa nkhawa. Zimenezi zikadzachitika, “zinthu zakale [monga nkhawa] sizidzakumbukiridwanso ndipo sizidzabweranso mumtima.”—Yesaya 65:17.
Dziwani izi: A Mboni za Yehova amadziwa kuti Mulungu amathandiza anthu amene ali ndi nkhawa koma nawonso amapita kuchipatala ngati akudwala matenda a maganizo. (Maliko 2:17) Sitilimbikitsa anthu kulandira chithandizo chinachake kuchipatala chifukwa munthu aliyense ayenera kusankha yekha pa nkhani ngati zimenezi.