Kodi Baibulo Limati Chiyani pa Nkhani ya Kubwezera?
Yankho la m’Baibulo
Munthu akhoza kuona kuti kubwezera n’koyenera, koma kuchita zimenezi n’kosemphana ndi malangizo a m’Baibulo akuti: “Usanene kuti: ‘Ndim’chitira zimene iye anandichitira. Aliyense ndizim’bwezera mogwirizana ndi zimene anachita.’” (Miyambo 24:29) M’Baibulo muli malangizo omwe athandiza anthu ambiri kuthetsa mtima wofuna kubwezera.
Zimene zili m’nkhani iyi
N’chifukwa chiyani si bwino kubwezera?
Ngati munthu wakukhumudwitsani kapena kukupwetekani, mwachibadwa mungadandaule n’kumafuna kuti munthuyo alangidwe. Koma kubwezera si kogwirizana ndi zimene Baibulo limaphunzitsa. N’chifukwa chiyani tikutero?
Mulungu sasangalala anthu akamabwezera. M’Baibulo, Yehova a Mulungu ananena kuti: “Kubwezera ndi kwanga, ndidzawabwezera ndine.” (Aroma 12:19) Baibulo limalimbikitsa anthu amene alakwiridwa kuti aziyesetsa kuthetsa mavuto mwamtendere m’malo mobwezera. (Aroma 12:18) Koma kodi tingatani ngati palibe njira zothetsera mavutowo mwamtendere kapena tayesetsa ndipo zalephereka? Malemba amanena kuti tiyenera kudalira Yehova kuti athane ndi zinthu zopanda chilungamo zimene zatichitikira.—Salimo 42:10, 11.
Kodi Mulungu amalanga anthu?
Panopa, Mulungu amalola kuti akuluakulu a boma azipereka chilango. (Aroma 13:1-4) Koma pa nthawi yake, adzalanga anthu onse amene achitira nkhanza anzawo ndipo adzathetseratu mavuto onse.—Yesaya 11:4.
Kodi ndingathetse bwanji mtima wofuna kubwezera?
Musamachite zinthu mopupuluma. (Miyambo 17:27) Nthawi zambiri, anthu amene amachita zinthu chifukwa chokwiya, amanong’oneza bondo pambuyo pake. Koma amene amaganiza kaye asanachite zinthu ndi amene amasankha bwino zochita.—Miyambo 29:11.
Muziyesetsa kudziwa bwino nkhani yonse. (Miyambo 18:13) Munthu amene walakwiridwa angachite bwino kudzifunsa kuti, ‘Kodi pali zinthu zimene sindikuzidziwa zomwe zachititsa munthuyo kuchita zimene wachita? Kodi wapanikizika ndi zinazake? Kapena kodi anachita zinthuzo mosazindikira?’ Nthawi zina, tingaone kuti munthu watilakwira mwadala pamene munthuyo anangochita zinthuzo mosadziwa.
Maganizo olakwika okhudza kubwezera
Maganizo olakwika: Baibulo limalola kuti tizibwezera chifukwa limanena kuti “diso kulipira diso.”—Levitiko 24:20.
Zoona zake: Lamulo lakuti “diso kulipira diso” limene linaperekedwa kwa Aisiraeli linkaletsa kuti anthu azibwezera okha. Koma linkathandiza oweruza kuti azisankha njira yoyenera yoti alange munthu. b—Deuteronomo 19:15-21.
Maganizo olakwika: Popeza Baibulo limanena kuti tisamabwezere, sitingadziteteze tikamachitiridwa nkhanza.
Zoona zake: Ndi zoyenera kuti munthu adziteteze kapena kupempha thandizo kwa anthu oyenera akachitiridwa nkhanza. Koma Baibulo limanena kuti tiyenera kumapewa kulimbana ndi ena ngati zingatheke.—Miyambo 17:14.
a Yehova ndi dzina la Mulungu ndipo limapezeka m’Baibulo.
b Kuti mudziwe zambiri zokhudza lamuloli, onani nkhani yakuti “Kodi Lamulo Lakuti ‘Diso Kulipira Diso’ Linkatanthauza Chiyani?”