Kodi Baibulo Limanena Zotani Zokhudza Danieli?
Yankho la m’Baibulo
Danieli anali mneneri wachiyuda wokhulupirika amene anakhalapo m’zaka za m’ma 600 ndi 500 B.C.E. Mulungu anamupatsa mphamvu zotha kumasulira maloto, anamuonetsa masomphenya a zimene zidzachitike m’tsogolo komanso anamuuzira kuti alembe buku la m’Baibulo lomwe limadziwika ndi dzina lake.—Danieli 1:17; 2:19
Kodi Danieli anali ndani?
Danieli anakulira ku Yuda. Mu ufumu wa Yuda munali mzinda wa Yerusalemu komanso kachisi wa Chiyuda. Mu 617 B.C.E., Nebukadinezara yemwe anali mfumu ya Babulo, analanda mzinda wa Yerusalemu ndi kugwira “akuluakulu a m’dzikolo” n’kupita nawo ku ukapolo ku Babulo. (2 Mafumu 24:15; Danieli 1:1) N’kutheka kuti pa nthawiyi Danieli anali wachinyamata ndipo anapita nawo limodzi pa ulendowo.
Danieli limodzi ndi anyamata ena (monga Sadrake, Mesake ndi Abedinego) anapita nawo kunyumba yachifumu ku Babulo kuti akalandire maphunziro apadera okhudza ntchito zaboma. Ngakhale kuti ankakakamizidwa kuti achite zinthu zosemphana ndi chikhulupiriro chawo, Danieli ndi anzake atatu aja anapitirizabe kukhala okhulupirika kwa Yehova Mulungu wawo. (Danieli 1:3-8) Ataphunzitsidwa kwa zaka zitatu, Mfumu Nebukadinezara anagoma chifukwa cha nzeru ndiponso luso la anyamatawa, ndipo ananena kuti anyamatawo anali anzeru “kuwirikiza maulendo 10 kuposa ansembe onse ochita zamatsenga ndi anthu onse olankhula ndi mizimu amene anali mu ufumu wake.” Kenako mfumuyo inasankha Danieli ndi anzake aja kuti azitumikira m’nyumba yake.—Danieli 1:18-20.
Patapita zaka zambiri mwina Danieli ali ndi zaka za m’ma 90, anaitanidwa kuti akaonekere ku nyumba ya mfumu. Belisazara, yemwe pa nthawiyi ankalamulira ku Babulo, anapempha Danieli kuti amasulire mawu omwe analembedwa modabwitsa pakhoma. Mothandizidwa ndi mzimu wa Mulungu, Danieli anamasulira kuti Babulo adzagonjetsedwa ndi Amedi ndi Aperisiya. Ndipo usiku womwewo mzindawu unagonjetsedwadi.—Danieli 5:1, 13-31.
Ufumu wa Amedi ndi Aperisiya utayamba kulamulira, Danieli anasankhidwa kukhala nduna yapamwamba ndipo Mfumu Dariyo inaganiza zomukwezabe pa udindo. (Danieli 6:1-3) Nduna zinzake zinayamba kumuchitira nsanje ndipo zinamukonzera chiwembu. Pamapeto pake Danieli anaponyedwa m’dzenje la mikango, koma Yehova anamupulumutsa. (Danieli 6:4-23) Danieli atatsala pang’ono kumwalira, mngelo wa Yehova anaonekera kwa iye kawiri konse n’kumutsimikizira kuti anali “munthu wokondedwa kwambiri.”—Danieli 10:11, 19.
Wonerani zomwe zinachitikazi mu sewero la m’Baibulo la mbali ziwiri la mutu wakuti, Danieli Anali Munthu Wachikhulupiriro Cholimba.