Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Kodi Chipulumutso N’chiyani?

Kodi Chipulumutso N’chiyani?

Yankho la m’Baibulo

 Nthawi zina Baibulo limagwiritsa ntchito mawu oti “kupulumutsa” ndiponso “chipulumutso” ponena za kuthandiza munthu amene moyo wake uli pa ngozi. (Ekisodo 14:13, 14; Machitidwe 27:20) Koma nthawi zambiri mawuwa amagwiritsidwa ntchito ponena za kumasulidwa ku uchimo. (Mateyu 1:21) Popeza uchimo umabweretsa imfa, anthu amene apulumutsidwa ku uchimowu amayembekezera kudzakhala ndi moyo wosatha.—Yohane 3:16, 17. a

Kodi munthu ayenera kuchita chiyani kuti adzapulumuke?

 Kuti munthu adzapulumuke, ayenera kukhulupirira Yesu ndiponso kusonyeza chikhulupirirocho pomvera malamulo ake.—Machitidwe 4:10, 12; Aroma 10:9, 10; Aheberi 5:9.

 Baibulo limasonyeza kuti munthu ayenera kukhala womvera kuti asonyeze kuti chikhulupiriro chake si chakufa. (Yakobo 2:24, 26) Komabe izi sizikutanthauza kuti zochita za munthu zingachititse kuti akhale woyenerera kupulumuka. Tikutero chifukwa chakuti chipulumutso ndi ‘mphatso yochokera kwa Mulungu,’ yomwe amapereka chifukwa cha “kukoma mtima kwakukulu” kapena kuti “chisomo” chake.—Aefeso 2:8, 9; Buku Lopatulika Ndilo Mau a Mulungu.

Kodi n’zotheka kuti munthu ataye mwayi wake wodzapulumuka?

 Inde. Munthu amene wagwera m’madzi ndipo wina wamuvuula kuti asamire, akhoza kugweranso m’madzimo atapanda kusamala. N’chimodzimodzinso ndi munthu amene wapulumutsidwa ku uchimo koma sakupitiriza kukhala ndi chikhulupiriro. Iye akhoza kutaya mwayi wake wodzapulumuka. N’chifukwa chake Baibulo limalimbikitsa Akhristu amene apulumutsidwa ku uchimo kuti ‘azimenya mwamphamvu nkhondo yachikhulupiriro.’ (Yuda 3) Limanenanso kuti: “Pitirizani kukonza chipulumutso chanu, mwamantha ndi kunjenjemera.”—Afilipi 2:12.

Kodi Mpulumutsi wathu ndi Mulungu kapena Yesu?

 Baibulo limasonyeza kuti chipulumutso chimachokera kwa Mulungu ndipo limanena kuti iye ndi “Mpulumutsi” wathu. (1 Samueli 10:19; Yesaya 43:11; Tito 2:10; Yuda 25) Kale Mulungu anagwiritsa ntchito anthu osiyanasiyana kuti apulumutse Aisiraeli ndipo Baibulo limanena kuti iwonso anali ‘apulumutsi.’ (Nehemiya 9:27; Oweruza 3:9, 15; 2 Mafumu 13:5) b Mulungu amapulumutsa anthu ku uchimo pogwiritsa ntchito nsembe ya dipo ya Yesu Khristu. Choncho Baibulo limanenanso kuti Yesu ndi “Mpulumutsi” wathu.—Machitidwe 5:31; Tito 1:4. c

Kodi aliyense adzapulumuka?

 Ayi, anthu ena sadzapulumuka. (2 Atesalonika 1:9) Yesu atafunsidwa kuti, “Kodi amene akupulumuka ndi owerengeka okha?” iye anayankha kuti: “Yesetsani mwamphamvu kulowa pakhomo lopapatiza. Chifukwa ambiri ndikukuuzani, adzafunitsitsa kulowamo koma sadzatha.”—Luka 13:23, 24.

Maganizo olakwika amene anthu ena ali nawo pa nkhani ya chipulumutso

 Maganizo olakwika: Lemba la 1 Akorinto 15:22 limasonyeza kuti anthu onse adzapulumuka chifukwa limati: “Mwa Khristu onse adzapatsidwa moyo.”

 Zoona zake: Nkhani ya palembali ndi yokhudza kuuka kwa akufa. (1 Akorinto 15:12, 13, 20, 21, 35) Choncho mawu akuti “mwa Khristu onse adzapatsidwa moyo” akutanthauza kuti anthu adzaukitsidwa kapena kulandira moyo kudzera mwa Yesu Khristu.—Yohane 11:25.

 Maganizo olakwika: Lemba la Tito 2:11 limaphunzitsa kuti anthu onse adzapulumuka chifukwa limanena kuti Mulungu ‘akupulumutsa anthu onse.’—Buku Lopatulika Ndilo Mau a Mulungu.

 Zoona zake: Mawu achigiriki a m’lembali omwe anawamasulira kuti anthu “onse” angatanthauzenso kuti “osiyanasiyana.” d Choncho lemba la Tito 2:11 limatanthauza kuti Mulungu akupulumutsa anthu osiyanasiyana kapena kuti ochokera “m’dziko lililonse, fuko lililonse, mtundu uliwonse, ndi chinenero chilichonse.”—Chivumbulutso 7:9, 10.

 Maganizo olakwika: Lemba la 2 Petulo 3:9 limasonyeza kuti anthu onse adzapulumuka chifukwa limanena kuti Mulungu “safuna kuti wina aliyense adzawonongedwe.”

 Zoona zake: Mulungu amafuna kuti anthu onse adzapulumuke koma sawakakamiza kuti azitsatira zimene iye amafuna kuti adzapulumuke. Pa ‘tsiku lake lachiweruzo adzawononga anthu osamuopa.’—2 Petulo 3:7.

a Nthawi zina Baibulo limanena kuti munthu ‘wapulumutsidwa’ ngakhale kuti kwenikweni adzapulumutsidwa ku uchimo ndi imfa m’tsogolo.​—Aefeso 2:5; Aroma 13:11.

b M’malembawa, Mabaibulo ena amagwiritsa ntchito mawu akuti “mthandizi,” “mtsogoleri” kapena “munthu” chabe m’malo monena kuti “mpulumutsi.” Koma mawu achiheberi oyambirira omwe anagwiritsidwa ntchito m’malembawa ndi ofanana ndi mawu amene amagwiritsidwa ntchito ponena kuti Yehova Mulungu ndi Mpulumutsi.—Salimo 7:10.

c Dzina lakuti Yesu limachokera ku mawu ena achiheberi akuti Yehoh·shuʹaʽ, omwe amatanthauza kuti “Yehova Ndiye Chipulumutso.”

d Onani buku lakuti, Vine’s Complete Expository Dictionary of Old and New Testament Words. Mawu achigiriki omwe anamasuliridwa kuti “onse” ndi ofanana ndi amene anamasuliridwa kuti “zamtundu uliwonse” palemba la Mateyu 5:11. Palembali Yesu anauza otsatira ake kuti anthu adzakunenerani “zoipa zamtundu uliwonse.”—Baibulo la International Standard Version.