Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Kodi Nkhani za M’Baibulo Zimatsutsana?

Kodi Nkhani za M’Baibulo Zimatsutsana?

Yankho la m’Baibulo

 Ayi. Nkhani zonse za m’Baibulo n’zogwirizana. Ngakhale kuti nkhani zina zingaoneke ngati zikutsutsana, koma mukhoza kuona kuti ndi zogwirizana ngati mutatsatira zina mwa mfundo izi:

  1.   Onani bwinobwino nkhani yonse. Nkhani iliyonse imene munthu angalembe, ena angaione kuti ikutsutsana ngati atangoona mbali yochepa ya nkhaniyo.

  2.   Ganizirani mmene wolemba wake anailembera. Mwachitsanzo, anthu amene anaona chinachake chikuchitika akhoza kunena molondola zimene zinachitikazo koma sangagwiritse ntchito mawu ofanana pofotokoza nkhaniyo komanso onse sanganene chilichonse chimene chinachitika.

  3.   Ganizirani mmene zinthu zinkakhalira pa nthawiyo komanso miyambo ya anthu.

  4.   Onani ngati mawu ena akugwiritsidwa ntchito mophiphiritsa kapena ayi.

  5.   Kumbukirani kuti nthawi zina anthu akhoza kunena kuti munthu wina wachita chinachake ngakhale munthuyo atakhala kuti anauza wina kuti amuchitire. a

  6.   Werengani Mabaibulo omasuliridwa molondola.

  7.   Muzipewa kugwirizanitsa maganizo a anthu ndi zimene Baibulo limanena.

 Zitsanzo zotsatirazi zikusonyeza mmene mfundo tazitchula pamwambazi zingathandizire kumvetsa nkhani za m’Baibulo zimene zingaoneke ngati zimatsutsana.

Mfundo yoyamba: Kuona nkhani yonse

  Ngati Mulungu anapuma pa tsiku la 7, n’chifukwa chiyani Baibulo lomwelo limanenanso kuti iye akugwirabe ntchito? Nkhani yonse yokhudza kulengedwa kwa zinthu, yopezeka m’buku la Genesis, imasonyeza kuti mawu akuti, “pa tsiku la 7 limenelo, [Mulungu] anayamba kupuma pa ntchito yake yonse imene anali kuchita,” amanena za kupuma pa ntchito yake yolenga dziko lapansi ndi zinthu zina. (Genesis 2:​2-4) Pamene Yesu ananena kuti Mulungu “akugwirabe ntchito mpaka pano,” sankatsutsana ndi mawu amenewa chifukwa iye ankanena za ntchito zimene Mulungu akugwira. (Yohane 5:​17) Zina mwa ntchitozo ndi kuuzira Baibulo, kutsogolera komanso kusamalira anthu.​—Salimo 20:6; 105:5; 2 Petulo 1:21.

Mfundo yachiwiri ndi yachitatu: Kuganizira zinthu zimene olemba nkhaniyo anaona komanso kuganizira mbiri yakale

  Kodi Yesu anachiritsira kuti munthu wakhungu? Buku la Luka limasonyeza kuti Yesu anachititsa munthu wakhungu pamene “anali kuyandikira ku Yeriko,” pomwe nkhani yofananayo imene ili m’buku la Mateyu imati Yesu anachititsa anthu awiri akhungu pamene “anali kutuluka mu Yeriko.” (Luka 18:​35-​43; Mateyu 20:​29-​34) Zimene Luka ndi Mateyu ananena pa nkhaniyi sikuti zikutsutsana koma zikutithandiza kumvetsa bwino nkhani yonse. Mwachitsanzo, Mateyu ankaganizira kwambiri zokhudza chiwerengero cha anthu akhunguwo pamene Luka ankaganizira kwambiri zokhudza munthu wakhungu amene analankhula ndi Yesu. Pa nkhani ya malo amene Yesu anachititsira anthuwa, akatswiri a mbiri yakale anapeza zoti m’nthawi ya Yesu, panali mizinda iwiri ya Yeriko. Panali mzinda wakale wa Yeriko womwe unamangidwa ndi Ayuda komanso mzinda watsopano wa Yeriko umene unamangidwa ndi Aroma, ndipo mizindayi inatalikirana pafupifupi kilomita imodzi ndi hafu. Yesu ayenera kuti anali pakati pa mizinda iwiri imeneyi pamene ankachiritsa anthu akhunguwo.

Mfundo ya 4: Kuganizira mawu ophiphiritsira komanso osaphiphiritsa

  Kodi dzikoli lidzawonongedwa? Palemba la Mlaliki 1:​4, Baibulo limati “dziko lapansi lidzakhalapobe mpaka kalekale” ndipo anthu ena angaone kuti zimenezi zikutsutsana ndi mawu akuti “zinthu zimene zimapanga kumwamba ndi dziko lapansi zidzatentha kwambiri n’kusungunuka.” (2 Petulo 3:​10) Komabe, m’Baibulo mawu akuti “dziko” amagwiritsidwa ntchito mophiphiritsa kutanthauza anthu, koma nthawi zina amagwiritsa ntchito mosaphiphiritsa ponena za dziko lenilenili. (Genesis 1:1; 11:​1, Buku Lopatulika Ndilo Mau a Mulungu) Mawu akuti “dziko” lidzaonongedwa omwe ali pa 2 Petulo 3:​10 sakutanthauza kuti dziko lenilenili lidzaotchedwa koma akutanthauza “chiwonongeko cha anthu osaopa Mulungu.”​—2 Petulo 3:7.

Mfundo ya 5: Kuganizira anthu amene akutchulidwa

  Ku Kaperenao, kodi ndani analankhula ndi Yesu n’kumuuza pempho la kapitawo? Lemba la Mateyu 8:​5, 6 limanena kuti kapitawo wa asilikali anapita kwa Yesu pamene lemba la Luka 7:3 limanena kuti kapitawoyo anatuma akulu a Ayuda kuti akapereke pempho lake. Tingamvetse bwino mfundo ya m’malemba amenewa, omwe akuoneka ngati akutsutsana, ngati titaganizira zoti kapitawo wa asilikaliyo ndi amene anachita chilichonse chotheka n’cholinga choti Yesu athandize kapolo wake. Choncho anatumiza akulu a Ayuda kuti akapereke pempho lakelo kwa Yesu.

Mfundo ya 6: Werengani Mabaibulo omasuliridwa molondola

  Kodi tonsefe timachimwa? Baibulo limaphunzitsa kuti tonsefe tinatengera uchimo kwa Adamu. (Aroma 5:12) Zimene Mabaibulo ena amanena zikuoneka kuti n’zotsutsana ndi mfundu imeneyi. Mabaibulo enawo amanena kuti munthu wabwino “sachimwa.” (1 Yohane 3:​6, Chipangano Chatsopano mu Chichewa cha Lero; Buku Lopatulika Ndilo Mau a Mulungu) Koma m’Chigiriki chimene chinagwiritsidwa ntchito polemba Baibulo, mawu akuti “chimwa” palemba la 1 Yohane 3:​6, amasonyeza zinthu zimene zikupitiriza kuchitika. Choncho pali kusiyana pakati pa tchimo limene tinatengera kwa Adamu, lomwe palibe angalipewe, ndi tchimo limene anthu amachita mwadala akamapitiriza kuchita zinthu zosamvera malamulo a Mulungu. N’chifukwa chake omasulira Mabaibulo ena anayesetsa kupewa kusokoneza anthu palemba limeneli. Mwachitsanzo, iwo anamasulira lembali molondola pogwiritsa ntchito mawu akuti “sakhala ndi chizolowezi chochita tchimo.”​—Baibulo la Dziko Latsopano; Phillips.

Mfundo ya 7: Kuona zimene Baibulo limanena osati maganizo a anthu

  Kodi Yesu ndi wofanana ndi Mulungu? Nthawi ina Yesu ananena kuti: “Ine ndi Atate ndife amodzi.” Zimene ananenazi zimaoneka ngati zikutsutsana ndi zimene ananenanso nthawi ina kuti, “Atate ndi wamkulu kuposa ine.” (Yohane 10:30; 14:28) Kuti timvetse molondola mavesi amenewa, tikuyenera kuona zimene Baibulo limanena pa nkhani ya Yehova ndi Yesu m’malo mogwirizanitsa mavesiwa ndi zimene ena amanena zakuti pali milungu itatu mwa Mulungu m’modzi zomwe si zochokera m’Baibulo. Baibulo limasonyeza kuti Yehova Mulungu ndi Atate wake wa Yesu komanso kuti Yesuyo amalambira Mulunguyo. (Mateyu 4:10; Maliko 15:34; Yohane 17:3; 20:17; 2 Akorinto 1:3) Choncho Yesu si wofanana ndi Mulungu.

 Pamene Yesu ananena akuti “Ine ndi Atate ndife amodzi” ankasonyeza kuti iyeyo ndi Atate wake, Yehova Mulungu, ali ndi cholinga chofanana. Kenako Yesu ananena kuti: “Atate ndi ine ndife ogwirizana.” (Yohane 10:38) Pemphero limene Yesu anapempherera ophunzira ake limasonyeza kuti iye ankafunanso kuti ophunzira ake akhale ndi cholinga chofanana ndi chake. Iye anapemphera kuti: “Ndawapatsa ulemerero umene munandipatsa, kuti iwo akhale amodzi mmene ifenso tilili amodzi. Ine wogwirizana ndi iwo, inu wogwirizana ndi ine.”​—Yohane 17:​22, 23.

a Mwachitsanzo, buku lakuti Encyclopædia Britannica limanena kuti manda otchedwa Taj Mahal anamangidwa ndi Shah Jahān yemwe anali mfumu ya ku Mughal. Komatu sikuti iyeyo ndi amene anamangadi chifukwa nkhaniyo imapitiriza kuti “anthu oposa 20,000 analembedwa ntchito kuti amange mandawo.”