Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Kodi Zinyama Zimapita Kumwamba?

Kodi Zinyama Zimapita Kumwamba?

Yankho la m’Baibulo

 Baibulo limaphunzitsa kuti pa zolengedwa zonse zomwe zili padziko lapansi, ndi anthu ochepa okha omwe adzapite kumwamba. (Chivumbulutso 14:1, 3) Anthuwo adzapita kumwamba kuti akalamulire limodzi ndi Yesu monga mafumu komanso ansembe. (Luka 22:28-30; Chivumbulutso 5:9, 10) Koma anthu ambiri adzaukitsidwa kuti akhale ndi moyo m’paradaiso padziko lapansi.—Salimo 37:11, 29.

 Baibulo silimanena kuti ziweto kapena agalu zidzapita kumwamba. Tikutero chifukwa choti zinyama sizingakwanitse kutsatira mfundo za m’Baibulo zozithandiza kuyenerera ‘kuitanidwa kumwamba.’ (Aheberi 3:1) Mfundozi zikuphatikizapo kuphunzira, kukhala ndi chikhulupiriro komanso kumvera malamulo a Mulungu. (Mateyu 19:17; Yohane 3:16; 17:3) Choncho anthu okha ndi amene anapatsidwa chiyembekezo chodzakhala ndi moyo wosatha.—Genesis 2:16, 17; 3:22, 23.

 Kuti zolengedwa zapadziko zipite kumwamba, zimafunika ziukitsidwe kaye. (1 Akorinto 15:42) M’Baibulo muli nkhani za anthu angapo omwe anaukitsidwa kwa akufa. (1 Mafumu 17:17-24; 2 Mafumu 4:32-37; 13:20, 21; Luka 7:11-15; 8:41, 42, 49-56; Yohane 11:38-44; Machitidwe 9:36-42; 20:7-12) Koma onsewa anali anthu, osati zinyama.

 Kodi zinyama zili ndi mzimu?

 Ayi. Baibulo limanena kuti nyama komanso anthu ndi zamoyo. (Numeri 31:28) Munthu woyamba Adamu atalengedwa, sanapatsidwe mzimu koma ‘anakhala wamoyo.’ (Genesis 2:7) Moyo unapangidwa ndi zinthu ziwiri, “fumbi lapansi” komanso “mpweya wa moyo.”

 Kodi moyo umafa?

 Inde. Baibulo limaphunzitsa kuti moyo umafa. (Levitiko 21:11; Ezekieli 18:20) Anthu komanso zinyama zikafa, zimabwerera kufumbi. (Mlaliki 3:19, 20) M’mawu ena tinganene kuti sizikhalaponso. a

 Kodi zinyama zimachimwa?

 Ayi. Kuti munthu achimwe amafunika kuganiza, kukhudzidwa ndi zinthu kapena kuchita zinazake zosemphana ndi mfundo za Mulungu. Amafunikanso kukhala woti amatha kudziwa zoyenera kusankha pa nkhani ya makhalidwe. Komatu zinyama sizingathe kuchita zimenezi. Pa nthawi yonse imene zimakhala ndi moyo, zimangochita zinthu mwachibadwa. (2 Petulo 2:12) Kenako zimafa, ngakhale kuti sizinachimwe.

 Kodi n’zoyenera kuchitira nkhanza zinyama?

 Ayi. Mulungu anapatsa mphamvu anthu zoti aziyang’anira zinyama, koma sanawapatse ufulu woti azizichitira nkhanza. (Genesis 1:28; Salimo 8:6-8) Ndipotu Mulungu amasamalira nyama ina iliyonse ngakhale mbalame zing’onozing’ono. (Yona 4:11; Mateyu 10:29) Iye analamula olambira ake kuti asamachitire nkhanza nyama.—Ekisodo 23:12; Deuteronomo 25:4; Miyambo 12:10.

a Kuti mudziwe zambiri, werengani mutu 6 m’buku lakuti Zimene Baibulo Limaphunzitsa.