Kodi Ndingatani Kuti Anthu Ena Asamandichitire Zachipongwe?
Yankho la m’Baibulo
Mfundo zotsatirazi, zomwe n’zogwirizana ndi zimene Baibulo limanena, zingakuthandizeni:
Muziganizira za ntchito basi. Muzichita zinthu mosangalala komanso mwaulemu ndi anzanu amene mumagwira nawo ntchito. Komabe, musamachite zinthu momasuka kwambiri chifukwa zimenezi zingachititse anthu ena kuganiza kuti ndinu wophweka pa nkhani ya zibwenzi kapena zogonana.—Mateyu 10:16; Akolose 4:6.
Muzivala modzilemekeza. Kuvala mosadzilemekeza kumachititsa anthu ena kukuganizirani zinthu zolakwika. Baibulo limatilimbikitsa kuti tizivala “mwaulemu ndi mwanzeru.”—1 Timoteyo 2:9.
Muzisankha mwanzeru anthu ocheza nawo. Ngati mumacheza ndi anthu amene amakonda kukopana ndi ena kuti azigonana nawo, ndiye kuti inunso anthu azikuchitirani zomwezo.—Miyambo 13:20.
Muzipewa nkhani zopusa. Muzichokapo ngati anthu amene mukucheza nawo ayamba kukambirana nkhani zokhudza “khalidwe lochititsa manyazi, nkhani zopusa kapena nthabwala zotukwana, zomwe ndi zinthu zosayenera.”—Aefeso 5:4.
Muzipewa malo komanso zinthu zimene zingakuikeni m’mavuto. Mwachitsanzo, chenjerani ngati munthu wina wakupemphani kuti mutsalire kuntchito popanda chifukwa chomveka nthawi yowerukira itakwana.—Miyambo 22:3.
Muzikana molimba mtima komanso mosapita m’mbali. Munthu wina akamachita zinthu zosonyeza kuti akufuna mugone naye, muuzeni mosabisa chichewa kuti simungalole zimene akufunazo. (1 Akorinto 14:9) Mwachitsanzo, mungamuuze kuti: “Zimene mukuchitazi sizindisangalatsa ndipo mukundisowetsa mtendere. Musiyiretu zimenezi.” Mukhozanso kumulembera kalata munthuyo n’kufotokoza zimene iye akuchita, mmene zikukukhudzirani ndiponso zimene mukufuna kuti iye achite. Muuzeni momveka bwino kuti mumatsatira mfundo za m’Baibulo zokhudza kukhala ndi makhalidwe abwino.—1 Atesalonika 4:3-5.
Uzani ena kuti akuthandizeni. Ngati munthuyo akupitirizabe kukuvutitsani, uzani munthu wina amene mumamukhulupirira kuti akuthandizeni. Mukhoza kuuza wachibale wanu, mnzanu wakuntchito kapena munthu wina amene amadziwa kuthandiza anthu amene akukumana ndi vuto ngati lanulo. (Miyambo 27:9) Anthu ambiri amene amachitiridwa zachipongwe aona kuti pemphero ndi lothandiza kwambiri. Kaya simunapempherepo m’moyo wanu, musakayikire zoti Yehova, “Mulungu amene amatitonthoza m’njira iliyonse,” angakuthandizeni.—2 Akorinto 1:3.
Anthu mamiliyoni ambiri amasowa mtendere kuntchito chifukwa chochitiridwa zachipongwe kapena kuvutitsidwa kuti agone nawo, koma Baibulo lingathandize anthu oterewa.