Kodi Baibulo Limanena Zotani pa Nkhani Yodzikonda Wekha?
Yankho la m’Baibulo
Baibulo limasonyeza kuti ndi zoyenera kuti munthu azidzikonda koma asamapitirire malire. Ndipo munthu amasonyeza kuti amadzikonda ngati amadzisamalira, kudzisungira ulemu komanso akamadziona kuti ndi wofunika. (Mateyu 10:31) Baibulo limasonyeza kuti munthu ayenera kukhala ndi malire pa nkhani yoganizira zofuna zake kuopera kuti angakhale wonyada.
Kodi munthu woyambirira kumukonda azikhala ndani?
Tiyenera kukonda kwambiri Mulungu pa moyo wathu. Ponena za lamulo lalikulu kwambiri, Baibulo limati: “Uzikonda Yehova Mulungu wako ndi mtima wako wonse.”—Maliko 12:28-30; Deuteronomo 6:5.
Baibulo limanenanso za lamulo lachiwiri kuti: “Uzikonda mnzako mmene umadzikondera wekha.”—Maliko 12:31; Levitiko 19:18.
Ngakhale kuti Baibulo silinapereke lamulo lachindunji loti munthu azidzikonda yekha, koma mawu akuti “uzikonda mnzako mmene umadzikondera wekha,” akusonyeza kuti sikolakwika ngati munthu atamadzikonda yekha komanso kudzisungira ulemu mosapitirira malire.
Kodi Yesu ankakonda ndani choyamba?
Yesu ankakonda kwambiri Mulungu. Komanso ankadziwa malire ake posonyeza kuti ankakonda anthu ena komanso posonyeza kuti ankadzikonda yekha ndipo analimbikitsa ophunzira ake kutengera zomwe iye ankachita.—Yohane 13:34, 35.
Pa zinthu zonse, Yesu ankakonda kwambiri Mulungu ndipo anadzipereka kwambiri kuti akwaniritse zimene Mulunguyo ankafuna. Nthawi ina ananena kuti: “Kuti dziko lidziwe kuti ndimakonda Atate, ndikuchita izi kutsatira lamulo limene Atatewo anandipatsa.”—Yohane 14:31.
Yesu anasonyezanso kuti ankakonda anthu. Anachita zimenezi popatsa anthuwo zomwe ankafunika ndipo anafika mpaka popereka moyo wake chifukwa cha anthuwo.—Mateyu 20:28.
Anasonyezanso kuti ankadziganizira chifukwa ankapeza nthawi yopuma, kudya komanso yosangalala ndi ophunzira ake limodzinso ndi ena omwe ankamutsatira.—Maliko 6:31, 32; Luka 5:29; Yohane 2:1, 2; 12:2.
Kodi munthu amene amaika patsogolo zofuna za ena m’malo mwa zofuna zake sakhala wosangalala kapena amadzichotsera ulemu?
Ayi. Tikutero chifukwa tinalengedwa m’chifaniziro cha Mulungu amene khalidwe lake lalikulu ndi chikondi. (Genesis 1:27; 1 Yohane 4:8) Zimenezi zikusonyeza kuti Mulungu anatilenga m’njira yoti tizitha kukonda anzathu. Ngakhale kuti timafunika kuchita zinthu modziganizira, timasangalala kwambiri tikamasonyeza kuti timakonda Mulungu kuposa chilichonse komanso tikamachitira zabwino anthu ena. Ndipotu Baibulo limanena kuti: “Kupatsa kumabweretsa chimwemwe chochuluka kuposa kulandira.”—Machitidwe 20:35.
Anthu ambiri masiku ano amanena kuti munthu amakhala wosangalala akamachita zinthu zomwe akuona kuti n’zabwino kwa iyeyo. Anthuwa anasintha mfundo yakuti “uzikonda mnzako” ndipo amanena kuti “uzidzikonda wekha.” Komabe ambiri amavomereza kuti munthu amakhala wathanzi komanso wosangalala akamatsatira mfundo ya m’Baibulo yakuti: “Aliyense asamangodzifunira zopindulitsa iye yekha basi, koma zopindulitsanso wina.”—1 Akorinto 10:24.