Kodi Munthu Angasonyeze Bwanji Kuti ‘Amalemekeza Bambo Ake ndi Mayi Ake’?
Yankho la m’Baibulo
Lamulo lonena za kulemekeza bambo ako ndi mayi ako limapezeka nthawi zambiri m’Baibulo. (Ekisodo 20:12; Deuteronomo 5:16; Mateyu 15:4; Aefeso 6:2, 3) Kuti munthu atsatire lamuloli afunika kuchita zinthu 4 zofunika kwambiri.
Muziwayamikira. Mungasonyeze kuti mukulemekeza bambo anu ndi mayi anu powayamikira chifukwa cha zinthu zonse zimene akuchitirani. Mungasonyeze kuti mumawayamikira potsatira malangizo awo. (Miyambo 7:1, 2; 23:26) Baibulo limati muyenera kuona makolo anu monga “ulemerero” wanu, kapena kuti kumawanyadira.—Miyambo 17:6.
Muziwamvera. Ngati mudakali wamng’ono, mungasonyeze kuti mumalemekeza bambo anu ndi mayi anu ngati mumazindikira udindo umene Mulungu anawapatsa woti azikuuzani zochita. Lemba la Akolose 3:20 limauza ana kuti: “Muzimvera makolo anu pa zinthu zonse, pakuti kuchita zimenezi kumakondweretsa Ambuye.” Ngakhale Yesu ankamvera makolo ake pamene anali mwana.—Luka 2:51.
Muziwalemekeza. (Levitiko 19:3; Aheberi 12:9) Nthawi zambiri kulemekeza makolo anu kumaphatikizapo zimene mumayankhula komanso mmene mumaziyankhulira. N’zoona kuti nthawi zina makolo amachita zinthu zimene zingachititse kuti muzivutika kuwalemekeza. Komabe, ana angalemekeze makolo awo popewa kulankhula komanso kuchita zinthu mopanda ulemu. (Miyambo 30:17) Baibulo limanena kuti kunena zinthu zonyoza makolo ndi tchimo lalikulu kwambiri.—Mateyu 15:4.
Muziwasamalira. Pamene makolo anu akalamba, angafunike kumawathandiza. Mungasonyeze kuti mumawalemekeza ngati mungayesetse kuchita zonse zomwe mungathe kuti akhale ndi zinthu zofunika pamoyo. (1 Timoteyo 5:4, 8) Mwachitsanzo, Yesu atatsala pang’ono kufa anauza munthu wina kuti azisamalira mayi ake.—Yohane 19:25-27.
Maganizo olakwika pa nkhani yolemekeza makolo
Maganizo olakwika: Kuti munthu asonyeze kuti amalemekeza bambo ake ndi mayi ake, ayenera kuwalola kuti aziyendetsa zinthu m’banja lake.
Zoona zake: Baibulo limaphunzitsa kuti mgwirizano wa mwamuna ndi mkazi okwatirana ndi wofunika kwambiri kuposa mgwirizano wawo ndi abale awo. Lemba la Genesis 2:24 limati: “Mwamuna adzasiya bambo ake ndi mayi ake, n’kudziphatika kwa mkazi wake.” (Mateyu 19:4, 5) N’zoona kuti mwamuna ndi mkazi wake akhoza kupindula ndi malangizo ochokera kwa makolo awo kapena apongozi awo. (Miyambo 23:22) Komabe, mwamuna ndi mkazi sangalakwitse ngati atasankha kuti achibale awo asamalowerere kwambiri nkhani za m’banja mwawo.—Mateyu 19:6.
Maganizo olakwika: Ulamuliro wa bambo kapena mayi umaposa wa wina aliyense.
Zoona zake: Ngakhale kuti Mulungu anapereka ulamuliro kwa makolo m’banja, ulamuliro wawo uli ndi malire ndipo suposa ulamuliro wa Mulungu. Mwachitsanzo, pamene khoti lalikulu linalamula ophunzira a Yesu kuti asamvere Mulungu, iwo anayankha kuti: “Ife tiyenera kumvera Mulungu monga wolamulira, osati anthu.” (Machitidwe 5:27-29) Mofanana ndi zimenezi, ana amamvera makolo awo “mwa Ambuye,” zomwe zikutanthauza kuti ayenera kuwamvera m’zinthu zonse zimene sizikusemphana ndi malamulo a Mulungu.—Aefeso 6:1.
Maganizo olakwika: Munthu amayenera kutsatira zimene bambo ndi mayi ake amakhulupirira ku chipembedzo chawo kuti asonyeze kuti amawalemekeza.
Zoona zake: Baibulo limatilimbikitsa kufufuza zinthu zimene tikuphunzitsidwa kuti tione ngati ndi zoona. (Machitidwe 17:11; 1 Yohane 4:1) Munthu amene amachita zimenezi akhoza kusankha kukhulupirira zinthu zosiyana ndi zimene makolo ake amakhulupirira. Baibulo limatchula za atumiki osiyanasiyana okhulupirika a Mulungu amene sanatsatire chipembedzo cha makolo awo, monga Abulahamu, Rute, ndi mtumwi Paulo.—Yoswa 24:2, 14, 15; Rute 1:15, 16; Agalatiya 1:14-16, 22-24.
Maganizo olakwika: Munthu angasonyeze kuti amalemekeza bambo ndi mayi ake ngati akuchita nawo miyambo ya chikhalidwe monga kulambira makolo omwe anamwalira kale.
Zoona zake: Baibulo limati: “Yehova Mulungu wako ndi amene uyenera kumulambira, ndipo uyenera kutumikira iye yekha basi.” (Luka 4:8) Mulungu sasangalala ndi munthu amene amalambira anthu akufa. Kuonjezera pamenepo, Baibulo limati “akufa sadziwa chilichonse.” Iwo samadziwa chilichonse ngakhale anthu aziwapatsa ulemu winawake, ndipo sangathandize kapena kuvulaza anthu amoyo.—Mlaliki 9:5, 10; Yesaya 8:19.