Kodi Pali “Machimo 7 Obweretsa Imfa?”
Yankho la m’Baibulo
Baibulo silitchula mwachindunji mndandanda wa “machimo 7 obweretsa imfa.” Komabe, limaphunzitsa kuti anthu amene amachita machimo akuluakulu sadzapulumuka. Mwachitsanzo, Baibulo limati machimo akuluakulu monga dama, kupembedza mafano, kuchita zamizimu, kupsa mtima, komanso kumwa mwauchidakwa ndi “ntchito za thupi.” Komanso limati: “Anthu amene amachita zimenezi sadzalowa mu ufumu wa Mulungu.”—Agalatiya 5:19-21. a
Kodi Baibulo limatchula zinthu 7 zimene Mulungu amadana nazo?
Inde limatchula. Pa Miyambo 6:16, Baibulo la Buku Lopatulika Ndilo Mawu a Mulungu limati: “Zilipo zinthu zisanu ndi chimodzi Yehova azida; ngakhale zisanu ndi ziwiri zimnyansa.” Ngakhale zili choncho, mndandanda wa machimo womwe uli pa Miyambo 6:17-19, sukutanthauza kuti machimo onse ndi okhawa. M’malomwake, mavesiwa akungotchula magulu a zochita zomwe zikuimira zinthu zonse zolakwika, zimene zikuphatikizapo zoganiza, zolankhula, ndi zochita. b
Kodi mawu oti “tchimo lakupha” amatanthauza chiyani?
Mabaibulo ena amagwiritsa ntchito mawu amenewa pa lemba la 1 Yohane 5:16. Mwachitsanzo, Baibulo la The New American Bible limati: “Pali tchimo lobweretsa imfa.” Mawu akuti “tchimo lakupha” akhoza kumasuliridwanso kuti “tchimo lobweretsa imfa.” Kodi pali kusiyana kotani pakati pa “tchimo lobweretsa imfa” ndi “tchimo losabweretsa imfa”?—1 Yohane 5:16.
Baibulo limanena momveka bwino kuti machimo onse amabweretsa imfa. Komabe, nsembe ya dipo ya Yesu Khristu ikhoza kutipulumutsa ku uchimo ndi imfa. (Aroma 5:12; 6:23) Choncho, “tchimo lobweretsa imfa” ndi limene silingakhululukidwe ndi nsembe ya dipo ya Khristu. Munthu amene amachita tchimo la mtundu umenewu amapitirizabe kulichita ndipo zimakhala zovuta kuti asinthe maganizo kapena makhalidwe ake. Baibulo limanena kuti munthu wochita tchimo limeneli “sadzakhululukidwa.”—Mateyu 12:31; Luka 12:10.
a Sikuti machimo otchulidwa pa Agalatiya 5:19-21 ndi okhawa omwe ndi akuluakulu, chifukwa pambuyo potchula machimo amenewa, Baibulo limanenanso kuti “ndi zina zotero.” Izi zikutanthauza kuti aliyense ayenera kugwiritsa ntchito luso la kuzindikira kuti apeze makhalidwe enanso oipa omwe sanatchulidwe.
b Lemba la Miyambo 6:16 lili ndi chitsanzo cha mawu a Chiheberi omwe amatsindika kwambiri za nambala yachiwiri poisiyanitsa ndi nambala yoyamba. Kutchula zinthu m’njira imeneyi kumapezeka kawirikawiri m’Malemba.—Yobu 5:19; Miyambo 30:15, 18, 21.