Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Kodi “Makiyi a Ufumu” N’chiyani?

Kodi “Makiyi a Ufumu” N’chiyani?

Yankho la m’Baibulo

 Nthawi zina mawu akuti “Makiyi a Ufumu,” m’Mabaibulo ena amatchedwanso “Makiyi olowera mu ufumu.” Mawuwa amatanthauza udindo wothandiza anthu kuti ‘akalowe mu ufumu wa Mulungu.’ (Mateyu 16:19;The New American Bible; Machitidwe 14:22) a Yesu anapatsa Petulo “makiyi a ufumu wakumwamba.” Zimenezi zikutanthauza kuti Petulo anapatsidwa udindo wotsegulira anthu okhulupirika mwayi wolandira mzimu woyera wa Mulungu kuti anthuwo adzathe kulowa mu Ufumu wakumwamba.

Kodi makiyiwa anawagwiritsa ntchito kwa anthu ati?

 Petulo anagwiritsa ntchito udindo umene Mulungu anamupatsa potsegulira magulu atatu a anthu mwayi wolowa mu Ufumu.

  1.   Ayuda komanso anthu otembenukira kuchiyuda. Yesu atangophedwa ndi kuukitsidwa, Petulo analimbikitsa gulu la Ayuda kuti liyambe kukhulupirira kuti Yesu ndi amene anasankhidwa ndi Mulungu kuti adzalamulire mu Ufumu. Anafotokozanso zimene Ayudawo angachite kuti apulumutsidwe. Zimenezi zinakhala ngati watsegulira anthuwo njira yoti alowe mu Ufumu ndipo anthu masauzande “analandira mawu akewo.”​—Machitidwe 2:38-41.

  2.   Asamariya. Patapita nthawi Petulo anatumizidwa kukalalikira ku Samariya b limodzi ndi mtumwi Yohane. Ali kumeneko, anagwiritsa ntchito kiyi wina wa Ufumu pamene anapempherera anthuwo “kuti alandire mzimu woyera.” (Machitidwe 8:14-17) Zimenezi zinachititsa kuti Asamariya akhale ndi mwayi wolowa mu Ufumu.

  3.   Anthu a mitundu ina. Patadutsa zaka zitatu ndi hafu kuchokera pamene Yesu anaphedwa, Mulungu anaulula kwa Petulo kuti anthu a mitundu ina analinso ndi mwayi wolowa mu Ufumu. Petulo atauzidwa zimenezi, anagwiritsa ntchito kiyi mmodzi pa makiyi omwe anapatsidwa, polalikira kwa anthu a mitundu ina. Zimenezinso zinatsegulira anthuwo mwayi wolandira mzimu woyera, kukhala Akhristu komanso kukhala ndi chiyembekezo cholowa mu Ufumu.​—Machitidwe 10:30-35, 44, 45.

Kodi ‘kulowa mu Ufumu’ kumatanthauza chiyani?

 Anthu amene ‘amalowa mu Ufumu,’ adzalamulira limodzi ndi Yesu kumwamba. Baibulo linaneneratu kuti anthuwa adzakhala “m’mipando yachifumu” ndipo “adzakhala mafumu olamulira dziko lapansi.”​—Luka 22:29, 30; Chivumbulutso 5:9, 10.

Maganizo olakwika okhudza makiyi a Ufumu

 Maganizo olakwika: Petulo ndi amene ankasankha anthu oti alowe mu ufumu.

 Zoona zake: Baibulo limanena kuti Khristu Yesu ndi “amene anaikidwiratu kudzaweruza amoyo ndi akufa” osati Petulo. (2 Timoteyo 4:1, 8; Yohane 5:22) Ndipo Petuloyo ananena kuti Yesu “ndi Amene Mulungu anamuika kukhala woweruza anthu amoyo ndi akufa.”—Machitidwe 10:34, 42.

 Maganizo olakwika: Mulungu, Yesu komanso angelo, ankadikira kuti Petulo adzasankhe nthawi yogwiritsa ntchito makiyi a Ufumu.

 Zoona zake: Ponena za makiyi a Ufumu, Yesu anauza Petulo kuti: “Chilichonse chimene udzamanga padziko lapansi chidzakhala chitamangidwa kumwamba, ndipo chilichonse chimene udzamasula padziko lapansi chidzakhala chitamasulidwa kumwamba.” (Mateyu 16:19) Anthu ena amaganiza kuti mawu amenewa akutanthauza kuti Petulo ndi amene ankasankha zinthu zoti zichitike kumwamba. Komabe mawu amenewa m’chigiriki choyambirira amasonyeza kuti Petulo ankatsatira zinthu zomwe zinali zitakonzedwa kale kumwamba.

 Malo ena m’Baibulo amasonyeza kuti pamene Petulo ankagwiritsa ntchito makiyi a Ufumu, ankamvera malangizo ochokera kumwamba. Mwachitsanzo pa nthawi ina pamene ankagwiritsa ntchito kiyi wachitatu anatsatira malangizo amene Mulungu anamupatsa.​—Machitidwe 10:19, 20.

a Nthawi zina Baibulo limagwiritsa ntchito mawu akuti “kiyi” ponena za udindo kapena ntchito ina yapadera.​—Yesaya 22:20-22; Chivumbulutso 3:7, 8

b Asamariya anali m’chipembedzo chomwe chinali chosiyana ndi Chiyuda komabe chinali ndi ziphunzitso ndi miyambo ina yochokera m’Chilamulo cha Mose.