Kodi Chizindikiro cha “Masiku Otsiriza” Kapena Kuti Nthawi “ya Mapeto” N’chiyani?
Yankho la m’Baibulo
Baibulo linatchula zochitika komanso makhalidwe omwe anthu adzakhale nawo monga chizindikiro cha “mapeto a nthawi ino” kapena cha “mathedwe a nthawi ya pansi pano.” (Mateyu 24:3; Buku Lopatulika Ndilo Mau a Mulungu) Baibulo limanenanso za nthawi imeneyi kuti, “masiku otsiriza” kapena kuti nthawi ya “mapeto.”—2 Timoteyo 3:1; Danieli 8:19.
Kodi m’Baibulo muli maulosi ati onena za “masiku otsiriza”?
Baibulo linaneneratu zinthu zambiri zomwe zidzachitikire limodzi pokwaniritsa “chizindikiro” chotithandiza kudziwa kuti tikukhala m’masiku otsiriza. (Luka 21:7) Tiyeni tikambirane zitsanzo izi:
Nkhondo zapadziko lonse. Yesu ananeneratu kuti: “Mtundu udzaukirana ndi mtundu wina, ndipo ufumu udzaukirana ndi ufumu wina.” (Mateyu 24:7) Mofanana ndi ulosiwu, lemba la Chivumbulutso 6:4 linaneneratu za wokwera pahatchi wina amene akuimira nkhondo zomwe ‘zidzachotsa mtendere padziko lapansi.’
Njala. Yesu ananeneratu kuti: “Kudzakhala njala.” (Mateyu 24:7) Buku la Chivumbulutso linaneneratunso za wokwera pahatchi wina amene akadzafika, madera ambiri padzikoli padzakhala njala yaikulu.—Chivumbulutso 6:5, 6.
Zivomezi zamphamvu. Yesu ananena kuti kudzakhala “zivomezi m’malo osiyanasiyana.” (Mateyu 24:7; Luka 21:11) Zivomezi zimenezi zikamadzachitika, zidzachititsa mavuto ambiri komanso anthu ambiri adzafa kuposa momwe zakhala zikukhalira m’mbuyo monsemu.
Matenda. Mogwirizana ndi zomwe Yesu ananena, kudzakhala miliri kapena kuti matenda osiyanasiyana.—Luka 21:11.
Kuphwanya malamulo. Ngakhale kuti anthu akhala akuphwanya malamulo kwazaka zambiri. Yesu ananeneratu kuti m’masiku otsiriza, padzakhala “kuwonjezeka kwa kusamvera malamulo.”—Mateyu 24:12.
Kuwononga dziko. Lemba la Chivumbulutso 11:18, linaneneratu kuti anthu adzakhala “akuwononga dziko lapansi.” Anthu adzachita zimenezi m’njira zambiri monga pochita zachiwawa ndi zachinyengo. Komanso adzachita zimenezi powononga chilengedwe.
Kuchepa kwa makhalidwe abwino. Pa 2 Timoteyo 3:1-4, Baibulo linaneneratu kuti anthu adzakhala “osayamika, osakhulupirika, . . . . osafuna kugwirizana ndi anzawo, onenera anzawo zoipa, osadziletsa, oopsa, osakonda zabwino, achiwembu, osamva za ena, odzitukumula ndiponso onyada.” Makhalidwe a anthuwa adzafika poipa kwambiri moti Baibulo limati idzakhala “nthawi yapadera komanso yovuta.”,
Kusagwirizana m’banja. Pa 2 Timoteyo 3:2, 3, Baibulo linaneneratu kuti anthu ambiri adzakhala “osakonda achibale awo.” Linaneneratunso kuti ana adzakhala “osamvera makolo.”
Kusakonda Mulungu. Yesu ananeneratu kuti: “Chikondi cha anthu ambiri chidzazirala.”(Mateyu 24:12) Pamenepa, Yesu ankatanthauza kuti ambiri adzasiya kukonda Mulungu. Nalonso lemba la 2 Timoteyo 3:4 linanena za anthu amenewa kuti adzakhala “okonda zosangalatsa, m’malo mokonda Mulungu.”
Chinyengo cha anthu a zipembedzo. Pa 2 Timoteyo 3:5, Baibulo linaneneratu kuti anthu adzaoneka ngati kuti amapembedza Mulungu, koma sadzafuna kutsatira mfundo zake.
Kumvetsa bwino maulosi a m’Baibulo. Buku la Danieli linaneneratu kuti “nthawi yamapeto,” anthu ambiri adzamvetsa bwino choonadi cha m’Baibulo komanso maulosi.—Danieli 12:4.
Ntchito yolalikira padziko lonse. Yesu ananeneratu kuti: “Uthenga wabwino uwu wa Ufumu udzalalikidwa padziko lonse lapansi kumene kuli anthu.”—Mateyu 24:14.
Anthu onyoza adzachuluka. Yesu ananeneratu kuti ambiri adzanyalanyaza umboni woonekera bwino wotsimikiza kuti mapeto akufika. (Mateyu 24:37-39) Kuwonjezera pamenepa, lemba la 2 Petulo 3:3, 4 linaneneratu kuti adzaona kuti zizindikirozo zilibe phindu lililonse.
Kukwaniritsidwa kwa maulosi onse. Yesu ananena kuti masiku otsiriza adzadziwika ndi kukwaniritsidwa kwa maulosi onsewa pa nthawi imodzi, osati ndi maulosi ochepa chabe kapena ndi ambiri a maulosiwa.—Mateyu 24:33.
Kodi tikukhala mu “masiku otsiriza”?
Inde. Zomwe zikuchitika padzikoli komanso tikawerengetsa bwino nthawi mogwirizana ndi zomwe Baibulo linaneneratu, zimasonyeza kuti masiku otsiriza anayamba mu 1914, chaka chomwe Nkhondo Yoyamba Padziko Lonse inayamba. Onerani vidiyoyi yomwe ikusonyeza kuti zomwe zikuchitika padzikoli, ndi umboni woti tikukhaladi m’masiku otsiriza.
Ufumu wa Mulungu unayamba kulamulira kumwamba mu 1914. Ndipo chinthu choyamba chomwe Ufumuyu unachita, ndi kuthamangitsa Satana Mdyerekezi limodzi ziwanda zake kuchoka kumwamba moti sakanathanso kusokoneza zinthu kumwambako. (Chivumbulutso 12:7-12) Zoti Satana akusokoneza kwambiri anthu, zikuonekera m’makhalidwe ndi zochita za anthu zomwe zikuchititsa masiku otsirizawa kukhala “nthawi yapadera komanso yovuta.”—2 Timoteyo 3:1.
Anthu ambiri amada nkhawa akaona mmene zinthu zikuyendera m’nthawi yovutayi. Amada nkhawa akaona kuti anthu sakugwirizananso ngati kale. Moti ena amaona kuti mwina nthawi ina padzikoli sipadzapezeka munthu aliyense, chifukwa anthu akhoza kudzaphana okhaokha.
Komabe, pali anthu ena omwe ngakhale kuti nawonso amakhala ndi nkhawa ndi mmene zinthu zikuyendera panopo, amaona kuti zinthu zidzakhala bwino kwambiri m’tsogolo. Iwo amakhulupirira kuti Ufumu wa Mulungu udzachotsa mavuto onse omwe ali padzikoli. (Danieli 2:44; Chivumbulutso 21:3, 4) Amayembekezera moleza mtima kuti Mulungu adzakwaniritsa zomwe analonjeza ndipo amalimbikitsidwa ndi mawu omwe Yesu ananena akuti: “Amene adzapirire mpaka pa mapeto, ndiye amene adzapulumuke.”—Mateyu 24:13; Mika 7:7.