Kodi Maulosi Onena za Mesiya Amatsimikizira Kuti Yesu Analidi Mesiya?
Yankho la m’Baibulo
Inde. Yesu ali padzikoli anakwaniritsa maulosi ambiri onena za “Mesiya Mtsogoleri” amenenso adzakhale “Mpulumutsi wa dziko.” (Danieli 9:25; 1 Yohane 4:14) Ndipotu ngakhale atamwalira n’kuukitsidwa, Yesu anapitirizabe kukwaniritsa maulosi onena za Mesiya.—Salimo 110:1; Machitidwe 2:34-36.
Kodi dzina lakuti “Mesiya” limatanthauza chiyani?
Mawu Achiheberi akuti Ma·shiʹach kapena kuti Mesiya omwenso ndi ofanana ndi mawu Achigiriki akuti Khri·stos kapena kuti Khristu, amatanthauza kuti “Wodzozedwa.” Choncho dzina lakuti, “Yesu Khristu” limatanthauza kuti “Yesu ndi Wodzozedwa,” kapena kuti “Yesu ndi Mesiya.”
Kale, nthawi zambiri munthu akamaikidwa pa udindo winawake wapadera, ankamuthira mafuta pamutu posonyeza kuti wadzozedwa. (Levitiko 8:12; 1 Samueli 16:13) Mulungu anadzoza Yesu kuti akhale Mesiya ndipo udindo umenewu ndi waukulu kwambiri. (Machitidwe 2:36) Komabe Mulungu sanadzoze Yesu ndi mafuta enieni, koma anamudzoza ndi mzimu woyera.—Mateyu 3:16.
Kodi maulosi onena za Mesiya anakwaniritsidwa ndi anthu angapo?
Ayi. Monga mmene zimakhalira kuti chidindo cha chala sichingaimire anthu awiri, maulosi a m’Baibulo onena za Mesiya ankafunika kukwaniritsidwa pa munthu m’modzi. Ndipo Baibulo linapereka chenjezo lakuti, “kudzafika onamizira kukhala Khristu ndi aneneri onyenga, ndipo adzachita zizindikiro zamphamvu ndiponso zodabwitsa, kuti ngati n’kotheka, adzasocheretse ngakhale osankhidwawo.”—Mateyu 24:24.
Kodi Mesiya adzaonekera m’tsogolo?
Ayi. Baibulo linaneneratu kuti Mesiya adzachokera m’banja la Mfumu Davide ya ku Isiraeli. (Salimo 89:3, 4) Komabe zikuoneka kuti mipukutu yakale ya Ayuda yofotokoza za mzere wa makolo mpaka kukafika pa Davide, inasowa ndipo n’kutheka kuti mipukutuyi inawonongedwa pa nthawi imene Aroma anabwera kudzagonjetsa Yerusalemu mu 70 C.E. a Kuchokera nthawi imeneyo palibe munthu winanso akananena kuti iyeyo ndi Mesiya wochokeradi m’banja lachifumu la Davide. Ngakhale zili choncho, m’nthawi ya Yesu mipukutuyo inalipo ndipo adani ake sakanatsutsa zomwe iye ananena kuti ndi wochokera m’banja la Davide.—Mateyu 22:41-46.
Kodi m’Baibulo muli maulosi angati onena za Mesiya?
N’zovuta kutchula kuti maulosi onena za Mesiya ndi ochuluka bwanji. Ndipo njira imene wina angagwiritse ntchito powerengera kuchuluka kwa maulosi, ikhoza kusiyana ndi imene wina angagwiritsenso ntchito, ngakhale pa nkhani zimene zikuonekeratu kuti zikufotokoza za Mesiya. Mwachitsanzo, nkhani ya pa Yesaya 53:2-7, imafotokoza za maulosi osiyanasiyana onena za Mesiya. Ena akhoza kuona mavesi onsewa ngati ulosi umodzi, pamene ena akhoza kuona mfundo iliyonse ngati ulosi pawokha.
Ena a maulosi onena za Mesiya omwe anakwaniritsidwa pa Yesu
Ulosi |
Umapezeka pa |
Kukwaniritsidwa kwake |
---|---|---|
Mbewu ya Abulahamu |
||
Mbadwa ya Isaki yemwe anali mwana wa Abulahamu |
||
Adzabadwira mu mtundu wa Chiyuda |
||
Adzabadwira mumzere wa banja lachifumu la Mfumu Davide |
||
Adzabadwa kwa namwali |
||
Adzabadwira ku Betelehemu |
||
Adzapatsidwa dzina lakuti Emanueli b |
||
Adzabadwira m’banja losauka |
||
Ana aang’ono adzaphedwa iye akadzangobadwa |
||
Adzaitanidwa kuti achoke ku Iguputo |
||
Adzatchedwa Mnazareti c |
||
Mthenga adzatsogola kudzalengeza za iye |
||
Adzadzozedwa kukhala Mesiya mu 29 C.E d |
||
Mulungu adzatsimikizira kuti Yesu ndi Mwana wake |
||
Adzadzipereka kwambiri panyumba ya Mulungu |
||
Adzalengeza uthenga wabwino |
||
Adzalalikira ku Galileya ndipo anthu ambiri adzaona kuwala |
||
Adzachita zozizwitsa ngati Mose |
||
Adzalankhula Mawu ochokera kwa Mulungu ngati mmene anachitira Mose |
||
Adzachiritsa anthu ambiri |
||
Sadzakhala wodzikonda |
||
Adzachitira chifundo anthu ovutika |
||
Adzasonyeza chilungamo cha Mulungu |
||
Mlangizi wodabwitsa |
||
Adzalengeza za dzina la Yehova |
||
Adzagwiritsa ntchito mafanizo pophunzitsa |
||
Mtsogoleri |
||
Anthu ambiri sadzamukhulupirira |
||
Adzakhala mwala wopunthwitsa |
||
Anthu adzamukana |
||
Anthu adzadana naye popanda chifukwa |
||
Adzalowa mu Yerusalemu mwaulemerero atakwera pabulu |
||
Adzatamandidwa ndi ana |
||
Adzabwera m’dzina la Yehova |
||
Adzaperekedwa ndi mnzake wapamtima |
||
Adzaperekedwa ndi ndalama 30 zasiliva e |
||
Anzake adzamuthawa |
||
Anthu adzamuperekera umboni wabodza |
||
Sadzayankha chilichonse kwa anthu omuimba mlandu |
||
Adzamulavulira |
||
Adzamenyedwa m’mutu |
||
Adzakwapulidwa |
||
Sadzabwezera anthu omumenya |
||
Olamulira adzagwirizana kuti alimbane naye |
||
Adzamukhomerera manja ndi mapazi ake kumtengo |
||
Anthu adzachitira mayere zovala zake |
||
Adzakhala ngati m’modzi wa anthu ochimwa |
||
Adzanyozedwa ndi kumunenera zachipongwe |
||
Adzavutika chifukwa cha anthu ochimwa |
||
Adzakhala ngati wakanidwa ndi Mulungu |
||
Adzapatsidwa vinyo wosakaniza ndi ndulu kuti amwe |
||
Adzamva ludzu asanamwalire |
||
Adzapereka mzimu wake kwa Mulungu |
||
Adzataya moyo wake |
||
Adzapereka dipo kuti achotse uchimo |
||
Mafupa ake sadzathyoledwa |
||
Adzalasidwa |
||
Adzaikidwa m’manda pamodzi ndi anthu olemera |
||
Adzaukitsidwa kwa akufa |
||
Womupereka adzalowedwa m’malo ndi munthu wina |
||
Adzakhala kudzanja lamanja la Mulungu |
a Buku la McClintock and Strong’s Cyclopedia limanena kuti: “Sitikukayikira kuti kaundula wonena za anthu a mtundu wachiyuda komanso mabanja awo anasokonezekera pa nthawi imene Yerusalemu ankawonongedwa.”
b Dzina lakuti Emanueli ndi la Chiheberi ndipo limatanthauza kuti “Mulungu Ali Nafe.” Dzinali limafotokoza bwino za udindo wa Yesu monga Mesiya. Kubwera kwake padzikoli komanso zimene anachita, zinasonyeza kuti Mulungu ali kumbali ya anthu omwe amamulambira.—Luka 2:27-32; 7:12-16.
c Mawu akuti “Mnazareti” anachokera ku mawu achiheberi akuti neʹtser, omwe amatanthauza “mphukira.”
d Kuti mudziwe zambiri zokhudza maulosi a m’Baibulo kudzafika mu 29 C.E. chaka chomwe Mesiya anafika, werengani nkhani yakuti, “Mmene Ulosi wa Danieli Unasonyezera Nthawi Imene Mesiya Adzafike,” m’buku la kodi Baibulo limaphunzitsa Chiyani, patsamba 197—199. (mu kabuku ka Zimene Baibulo Limaphunzitsa, ndi patsamba 211-212 koma mutu wake ndi wina)
e Ulosi umenewu uli m’buku la Zekariya ngakhale kuti Mateyu amene analemba nawo Baibulo ananena kuti ulosiwu unanenedwa “kudzera mwa mneneri Yeremiya.” (Mateyu 27:9) Zikuoneka kuti nthawi ina m’mbuyomo buku la Yeremiya, linkaikidwa koyambirira m’mabuku omwe ankadziwika kuti “Zolemba za Aneneri.” (Luka 24:44) Choncho n’kutheka kuti Mateyu ananena kuti ulosiwu uli m’buku la “Yeremiya” pofotokoza za mabuku onse a aneneriwo omwe ankaphatikizaponso buku la Zekariya.