KUFOTOKOZA MAVESI A M’BAIBULO
Aefeso 3:20—“[Mulungu] Amene Angathe Kuchita Zazikulu Kwambiri Kuposa Zonse Zimene Timapempha Kapena Kuganiza”
“Tsopano kwa iye amene angathe kuchita zazikulu kwambiri kuposa zonse zimene timapempha kapena kuganiza, malinga ndi mphamvu yake imene ikugwira ntchito mwa ife, kwa iye kukhale ulemerero.”—Aefeso 3:20, 21, Baibulo la Dziko Latsopano.
“Ndipo kwa Iye amene angathe kuchita koposaposatu zonse zimene tizipempha, kapena tiziganiza, monga mwa mphamvu ya kuchita mwa ife, kwa Iye ukhale ulemerero.”—Aefeso 3:20, 21, Buku Lopatulika Ndilo Mau a Mulungu.
Tanthauzo la Aefeso 3:20
Mtumwi Paulo sankakayikira kuti Mulungu amayankha mapemphero komanso amakwaniritsa zimene analonjeza kwa atumiki ake m’njira imene atumiki akewo sanaiganizirepo. Iye angayankhe anthu ake powachitira zazikulu kuposa zomwe akuyembekezera komanso m’njira zina zambiri.
“Tsopano kwa iye amene angathe . . . malinga ndi mphamvu yake imene ikugwira ntchito mwa ife.” Mawu omwe ali pavesi 21 akuti “iye,” akunena za Yehova Mulungu a ndipo iye angatipatse mphamvu zimene timafunikira kuti tichite zomwe amafuna.—Afilipi 4:13.
Muvesi 20, mtumwi Paulo akufotokoza mmene Yehova amathandizira anthu amene amamulambira. Ponena za mawu amene anamasuliridwa kuti “kwa iye amene angathe,” buku lina limati: “Sikuti vesili limangonena kuti Mulungu angathe kuchita chinachake kapena kuti n’zotheka kuti angachite zinazake koma amatanthauza kuti ali ndi mphamvu zochitira zinthuzo.” Mosiyana ndi anzathu apamtima, nthawi zonse Yehova amachita zonse zofunikira kuti asamalire atumiki ake komanso kuyankha mapemphero awo. Iye yekha ndi amene ali ndi mphamvu zambiri zopanda malire.—Yesaya 40:26.
“[Mulungu] angathe kuchita zazikulu kwambiri kuposa zonse zimene timapempha kapena kuganiza.” Yehova angachitire atumiki ake zambiri kuposa ‘zonse zimene amapempha kapena kuganiza.’ Iye angawathandize m’njira zimene sankaziyembekezera kapena zoposa zimene iwo amaona kuti angawapatse mosaumira.
Mawu akuti “kuposa zonse zimene timapempha kapena kuganiza,” akutithandiza kumvetsa mfundo ina yofunika kwambiri ya muvesili. Polankhula mawu amenewa, mtumwiyu ankafuna kuti Akhristu onse amvetse kuti Mulungu angawathandize m’njira imene sanaiganizirepo n’komwe. Nthawi zina, Akhristu akhoza kumaona kuti mavuto awo ndi aakulu kwambiri moti zingakhale zovuta kuwathetsa. Nthawi zinanso sangadziwe zimene anganene m’pemphero, koma Yehova amadziwa ndipo alibe malire akafuna kupeza njira zothetsera mavuto aliwonse amene atumiki ake angakumane nawo. Pa nthawi yake, iye angathetse mavuto m’njira imene sankaiyembekezera kapena kuiganizira. (Yobu 42:2; Yeremiya 32:17). Panopa, Yehova amawapatsa mphamvu kuti athe kupirira mosangalala mavuto amene akukumana nawo.—Yakobo 1:2, 3.
Nkhani yonse ya pa Aefeso 3:20
Buku la Aefeso ndi kalata imene mtumwi Paulo analembera Akhristu amene ankakhala mumzinda wa Aefeso ku Asia Minor komwe panopa ndi mbali ya dziko la Turkey. M’kalata yake, Paulo analembamo mfundo zimene anatchula popempherera Akhristuwa. (Aefeso 3:14-21) Iye anapemphera kuti Akhristuwo, kuphatikizapo ena onse, ayenera kutsanzira chikondi chimene Khristu anali nacho poyesetsa kuti aziganiza komanso kuchita zinthu ngati mmene Yesu ankachitira. Paulo anamaliza pemphero lake potamanda Mulungu ndipo ananena mawu amene timawapeza pa Aefeso 3:20, 21.
Onerani vidiyo yaifupiyi kuti mumvetse bwino nkhani ya m’buku la Aefeso.
a Yehova ndi dzina la Mulungu. (Salimo 83:18) Werengani nkhani yakuti, “Kodi Yehova Ndi Ndani?”