KUFOTOKOZA MAVESI A M’BAIBULO
Afilipi 4:13—“Ndimatha Kuchita Zonse Kudzera mwa Khristu”
“Pa zinthu zonse, ndimapeza mphamvu kuchokera kwa iye amene amandipatsa mphamvu.”—Afilipi 4:13, Baibulo la Dziko Latsopano.
“Ndimatha kuchita zonse kudzera mwa Khristu yemwe amandipatsa mphamvu.”—Afilipi 4:13, New King James Version.
Tanthauzo la Afilipi 4:13
Mawu amenewa, omwe analembedwa ndi mtumwi Paulo, amatsimikizira onse amene amalambira Mulungu kuti adzalandira mphamvu zowathandiza kuchita zimene Mulungu amafuna.
Mabaibulo ena amanena kuti Khristu ndi amene ankamupatsa Paulo mphamvu. Koma mawu oti “Khristu” sapezeka m’vesili m’makope akale kwambiri a Chigiriki. N’chifukwa chake Mabaibulo ambiri atsopano amagwiritsa ntchito mawu monga akuti “iye amene amandipatsa mphamvu” (Baibulo la Dziko Latsopano) kapena akuti “Iye amene andilimbitsa” (Malembo Oyera). Ndiye kodi Paulo ankanena za ndani m’vesili?
Mavesi ena a m’kalata imene Paulo analembera Afilipiyi amasonyeza kuti Paulo ankanena za Mulungu. (Afilipi 4:6, 7, 10) Chakumayambiriro kwa kalatayi, iye anati: “Mulungu . . . amalimbitsa zolakalaka zanu kuti muchite zinthu zonse zimene iye amakonda.” (Afilipi 2:13) Komanso pa 2 Akorinto 4:7, Paulo analemba kuti ndi Mulungu amene ankamupatsa mphamvu kuti achite utumiki wake. (Yerekezerani ndi 2 Timoteyo 1:8.) Choncho pali zifukwa zomveka zonena kuti Paulo ankanena za Mulungu polemba kuti “iye amene amandipatsa mphamvu.”
Kodi Paulo ankatanthauza chiyani ponena kuti ankapeza mphamvu “pa zinthu zonse”? Zikuoneka kuti ankanena za zinthu zosiyanasiyana zimene ankakumana nazo pogwira ntchito ya Mulungu. Kaya anali ndi zinthu zambiri kapena zochepa, ankadalira Mulungu kuti azimuthandiza. Paulo anaphunzira kukhala wokhutira ndi zimene anali nazo mosatengera mmene zinalili pa moyo wake.—2 Akorinto 11:23-27; Afilipi 4:11.
Mawu a Paulowa angalimbikitse anthu a Mulungu masiku ano. Mulungu adzawapatsa mphamvu zowathandiza kupirira mavuto komanso kuchita zimene iye amafuna. Mulungu angawapatse mphamvu pogwiritsa ntchito mzimu wake woyera, kapena kuti mphamvu yake yogwira ntchito, komanso pogwiritsa ntchito Akhristu anzawo ndiponso Mawu ake, Baibulo.—Luka 11:13; Machitidwe 14:21, 22; Aheberi 4:12.
Nkhani yonse ya Afilipi 4:13
Mawu amenewa ali m’mawu omaliza a kalata imene Paulo analembera Akhristu a ku Filipi. Iye analemba kalatayi cha m’ma 60 kapena 61 C.E. pa nthawi yoyamba imene anali m’ndende ku Roma. Kwa nthawi ndithu, Akhristu a ku Filipi sankakwanitsa kuthandiza mtumwi Paulo kuti azipeza zofunika pa moyo. Koma pa nthawi imene analemba kalatayi, anali atayamba kumutumizira mphatso za zinthu zimene ankafunikira.—Afilipi 4:10, 14.
Paulo anayamikira kwambiri Akhristu a ku Filipi chifukwa chomupatsa zinthu mowolowa manja ndipo anawatsimikizira kuti anali ndi zinthu zonse zofunika. (Afilipi 4:18) Iye anapezeraponso mwayi wowauza mfundo yofunika pa moyo wa Akhristu yakuti: Akhristu onse, kaya ndi olemera kapena osauka, angakhale okhutira ndi zimene ali nazo ngati amadalira Mulungu kuti aziwathandiza.—Afilipi 4:12.