Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

KUFOTOKOZA MAVESI A M’BAIBULO

Afilipi 4:8—“Zinthu zilizonse zoona, . . . pitirizani kuganizira zimenezi”

Afilipi 4:8—“Zinthu zilizonse zoona, . . . pitirizani kuganizira zimenezi”

 “Chomalizira abale, zinthu zilizonse zoona, zilizonse zofunika kwambiri, zilizonse zolungama, zilizonse zoyera, zilizonse zachikondi, zilizonse zoyamikirika, khalidwe labwino lililonse, ndi chilichonse chotamandika, pitirizani kuganizira zimenezi.”—Afilipi 4:8, Baibulo la Dziko Latsopano.

 “Chotsalira, abale, zinthu zilizonse zoona, zilizonse zolemekezeka, zilizonse zolungama, zilizonse zoyera, zilizonse zokongola, zilizonse zimveka zokoma; ngati kuli chokoma mtima china, kapena chitamando china, zilingirireni izi.”—Afilipi 4:8, Buku Lopatulika Ndilo Mau a Mulungu.

Tanthauzo la Afilipi 4:8

 Mulungu amachita chidwi ndi zimene anthufe timaganiza, makamaka chifukwa chakuti zomwe timaganizazo zimakhudza zomwe timachita. (Salimo 19:14; Maliko 7:20-23) N’chifukwa chake anthu omwe amafuna kusangalatsa Mulungu, amapewa zinthu zomwe Mulunguyo amadana nazo. Ndipo m’malomwake amaganizira zinthu zomwe iye amazivomereza.

 Vesili likutchula zinthu zabwino zokwanira 8 zomwe Akhristu ayenera ‘kupitiriza kuziganizira’ kapena kukhala ndi chizolowezi choziganizira.

  •   “Zoona.” Mawuwa akufotokoza za zinthu zoyenera komanso zodalirika. Mwachitsanzo zinthuzi ndi monga mfundo zopezeka m’Mawu a Mulungu Baibulo.—1 Timoteyo 6:20.

  •   “Zofunika kwambiri.” Mawuwa akunena za nkhani zofunika kwambiri, osati zachibwana kapena zopanda pake. Ndipo Akhristu akamaganizira zinthu zimenezi amakhala okonzeka kuchita zinthu zoyenera.—Tito 2:6-8.

  •   “Zolungama.” Mawuwa akuimira zolinga komanso zochita zomwe ndi zogwirizana ndi mfundo za Mulungu zonena za zinthu zoyenera osati pongotengera nzeru za anthu.—Miyambo 3:5, 6; 14:12.

  •   “Zoyera.” Mawuwa akufotokoza za maganizo komanso zolinga zoyenera osati pankhani zokhudza kugonana kokha, komanso m’zinthu zonse.—2 Akorinto 11:3.

  •   “Zachikondi.” Mawuwa akunena zinthu zosangalatsa zomwe zimatilimbikitsa kukonda anzathu m’malo modana nawo, kuwakwiyira kapenanso kukangana nawo.—1 Petulo 4:8.

  •   “Zoyamikirika.” Mawuwa akunena zinthu zomwe zingathandize munthu kukhala ndi mbiri yabwino komanso zomwe anthu omwe amalemekeza Mulungu angazione kuti ndi zoyenera.—Miyambo 22:1.

  •   “Khalidwe labwino.” Mawuwa akunena za makhalidwe abwino ogwirizana ndi mfundo za Mulungu. Makhalidwewa ndi apamwamba kwambiri.—2 Petulo 1:5, 9.

  •   “Chotamandika.” Mawuwa akuimira zinthu zovomerezeka kwa Mulungu. Angaphatikizeponso zochita za Mulungu zomwe anthu amafunika kuziganizira.—Salimo 78:4.

Nkhani yonse ya pa Afilipi 4:8

 Mtumwi Paulo anali pa ukaidi wapanyumba ku Roma pa nthawi imene ankalembera kalata Akhristu a ku Filipi. Komabe, akatswiri othirira ndemanga pa nkhani za m’Baibulo amati kalatayi, ndi “kalata yachisangalalo” chifukwa ili ndi mawu ambiri olimbikitsa komanso achikondi.—Afilipi 1:3, 4, 7, 8, 18; 3:1; 4:1, 4, 10.

 Paulo ankakonda abale ndi alongo ake auzimu omwe ankakhala ku Filipi ndipo ankafuna kuti nawonso azisangalala komanso kukhala ndi mtendere ngati iyeyo. (Afilipi 2:17, 18) N’chifukwa chake m’mawu omaliza a m’kalatayi, analimbikitsa Akhristuwa kuti azikhala osangalala, oganiza bwino, azipemphera nthawi zonse kwa Mulungu ndiponso kuti aziganizira zinthu zomwe zingawathandize kukhala ndi mtendere wamumtima komanso zomwe zingawathandize kukhala pamtendere ndi Mulungu.—Afilipi 4:4-9.

 Onerani vidiyo yaifupiyi kuti mumvetse bwino nkhani ya m’buku la Afilipi.