Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

KUFOTOKOZA MAVESI A M’BAIBULO

Aroma 5:8​​—“Pamene Tinali Ochimwa, Khristu Anatifera”

Aroma 5:8​​—“Pamene Tinali Ochimwa, Khristu Anatifera”

 “Mulungu akuonetsa chikondi chake kwa ife, moti pamene tinali ochimwa, Khristu anatifera.”​—Aroma 5:8, Baibulo la Dziko Latsopano.

 “Mulungu atsimikiza kwa ife chikondi chake cha mwini yekha m’menemo, kuti pokhala ife chikhalire ochimwa, Khristu adatifera ife.”​—Aroma 5:8, Buku Lopatulika Ndilo Mau a Mulungu.

Tanthauzo la Aroma 5:8

 Yehova a Mulungu anasonyeza chikondi chosaneneka pamene analola kuti Mwana wake Yesu Khristu afe chifukwa cha anthu ochimwa. (Yohane 3:16) Nthawi zambiri, maganizo ndi zochita za anthu ochimwafe zimakhala zosiyana ndi mfundo zachilungamo za Mulungu. (Akolose 1:21, 22) Koma Mulungu anakonza zoti tigwirizanenso naye “kudzera mu imfa ya Mwana wake.” (Aroma 5:10) Zimenezi zinatitsegulira mwayi woti tikhalenso pa ubwenzi ndi Mulungu komanso tidzapeze moyo wosatha.​—Aroma 5:11; 1 Yohane 4:9, 10.

Nkhani yonse ya Aroma 5:8

 Mtumwi Paulo analemba mawuwa kwa Akhristu a ku Roma. Munkhani imene ili mu chaputala 5 cha buku la Aroma, Paulo anafotokoza chifukwa chake Akhristu ayenera kukhala osangalala komanso osakayikira chiyembekezo chawo. (Aroma 5:1, 2) “Chiyembekezocho sichitikhumudwitsa” chifukwa chakuti chinakhalapo chifukwa cha chikondi chachikulu cha Mulungu chomwe anachisonyeza kudzera mwa Yesu. (Aroma 5:5, 6) Yesu anakhalabe wokhulupirika kwa Mulungu popanda kulakwitsa chilichonse ndipo izi n’zimene Adamu analephera kuchita. (Aroma 5:19) Kusamvera kwa Adamu kunabweretsa uchimo ndi imfa kwa ana ake onse. (Aroma 5:12) Koma kumvera kwa Yesu ndiponso nsembe imene anapereka zinathandiza kuti anthu omvera akhale ndi chiyembekezo cha moyo wosatha.​—Aroma 5:21.

a Yehova ndi dzina lenileni la Mulungu lopezeka m’Baibulo.​—Salimo 83:18.