Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

KUFOTOKOZA MAVESI A M’BAIBULO

Ekisodo 20:12​—“Uzilemekeza Bambo Ako ndi Mayi Ako”

Ekisodo 20:12​—“Uzilemekeza Bambo Ako ndi Mayi Ako”

 “Uzilemekeza bambo ako ndi mayi ako kuti masiku ako atalike m’dziko limene Yehova Mulungu wako akukupatsa.”​—Ekisodo 20:12, Baibulo la Dziko Latsopano.

 “Uzilemekeza atate wako ndi amako; kuti achuluke masiku ako m’dziko limene Yehova Mulungu wako akupatsa iwe.”​—Ekisodo 20:12, Buku Lopatulika Ndilo Mau a Mulungu.

Tanthauzo la Ekisodo 20:12

 Mulungu analamula Aisiraeli kuti azilemekeza makolo awo. Iye anawalimbikitsanso kutsatira lamuloli powalonjeza zinthu zabwino. Ngakhale kuti Chilamulo cha Mulungu, kapena kuti Chilamulo cha Mose, sichikugwirabe ntchito masiku ano, mfundo za Mulungu sizinasinthe. Mfundo zimene malamulo a m’Chilamulo cha Mulungu amachokera zikugwirabe ntchito ndipo n’zofunika kwa Akhristufe.​—Akolose 3:20.

 Ana, kaya ndi aang’ono kapena aakulu, amalemekeza makolo akamawasonyeza ulemu komanso kuwamvera. (Levitiko 19:3; Miyambo 1:8) Ngakhale ana atakula n’kukhala ndi mabanja awo, amapitirizabe kusonyeza chikondi kwa makolo awo. Mwachitsanzo, amaonetsetsa kuti makolo awo atakalamba akusamaliridwa komanso pakafunika amawapatsa ndalama.​—Mateyu 15:4-6; 1 Timoteyo 5:4, 8.

 Onani kuti ana a Chiisiraeli ankafunika kulemekeza bambo awo komanso mayi awo ndipo ankayenera kuzindikira kuti udindo wa mayi ndi wofunika m’banja. (Miyambo 6:20; 19:26) Ana amasiku ano ayeneranso kuchita zimenezi.

 Koma kuyambira kale, lamulo loti ana azilemekeza makolo awo linali ndi malire. Ana a Chiisiraeli sankayenera kumvera makolo awo kapena munthu wina aliyense ngati powamvera ankafunika kuchita zinthu zimene Mulungu sangasangalale nazo. (Deuteronomo 13:6-8) N’chimodzimodzinso masiku ano. Akhristu ayenera “kumvera Mulungu monga wolamulira, osati anthu.”​—Machitidwe 5:29.

 M’Chilamulo chimene Mulungu anapatsa Aisiraeli, iye analonjeza kuti ana amene amalemekeza makolo awo adzakhala kwa nthawi yaitali m’dziko limene Mulungu anawapatsa. (Deuteronomo 5:16) Sakanapatsidwa chilango chimene ana aakulu omwe ananyalanyaza lamulo la Mulunguli n’kumapandukira makolo awo linapatsidwa. (Deuteronomo 21:18-21) Mfundo zimene malamulowo amachokera sizinasinthe. (Aefeso 6:1-3) Kaya ndife ana kapena achikulire, tonse tiyenera kuyankha mlandu kwa Mlengi wathu. Ndipotu mogwirizana ndi zimene Mulungu analonjeza, ana amene amamumvera komanso kumvera makolo awo adzakhala ndi moyo wautali. Iwo angayembekezere kudzakhala ndi moyo wosatha.​—1 Timoteyo 4:8; 6:18, 19.

Nkhani yonse ya Ekisodo 20:12

 Lamulo la pa Ekisodo 20:12 lili ndi malo apadera pa Malamulo 10, kapena kuti Mawu 10. (Ekisodo 20:1-17) Lili pakati pa magulu awiri a malamulo. Malamulo am’mbuyo mwa lamuloli ndi okhudza zimene Aisiraeli ankafunika kupatsa Mulungu, ngati kumulambira iye yekha. Malamulo apatsogolo pa lamuloli ndi okhudza zimene Aisiraeli ankafunika kuchita ndi anthu anzawo. Mwachitsanzo, pali lamulo loti akhale okhulupirika kwa mwamuna kapena mkazi wawo komanso asabe. Choncho anthu amaona kuti lamulo loti “uzilemekeza bambo ako ndi mayi ako” ndi limene limalumikiza magulu awiri a malamulowa.

Werengani Ekisodo chaputala 20, mawu am’munsi ndi malifalensi ake.