KUFOTOKOZA MAVESI A M’BAIBULO
Mateyu 6:34—“Musadere Nkhawa za Mawa”
“Musamade nkhawa za tsiku lotsatira, chifukwa tsiku lotsatira lidzakhala ndi zodetsa nkhawa zakenso. Zoipa za tsiku lililonse n’zokwanira pa tsikulo.”—Mateyu 6:34, Baibulo la Dziko Latsopano.
“Musadere nkhawa za mawa; pakuti mawa adzadzidera nkhawa iwo okha. Zikwanire tsiku zovuta zake.”—Mateyu 6:34, Buku Lopatulika Ndilo Mau a Mulungu.
Tanthauzo la Mateyu 6:34
Yesu, yemwe ananena mawu amenewa, ankatsimikizira anthu amene ankamumvetsera kuti sayenera kudera nkhawa kwambiri za mavuto a m’tsogolo. M’malomwake, angachite bwino kungoganizira mavuto amene anali nawo pa tsikulo.
Pamenepa si kuti Yesu ankatanthauza kuti kuganizira za mawa kapena kukonzekera za m’tsogolo n’kulakwa. (Miyambo 21:5) Koma ankatilimbikitsa kuti tisamadere nkhawa kwambiri za zinthu zimene mwina zingachitike mawa. Nkhawa imeneyi ingatilepheretse kukhala osangalala komanso kumaliza zimene tikuchita pa nthawiyo. Sitingathetse mavuto a m’tsogolo pomada nawo nkhawa lero. Komanso nthawi zambiri zinthu zimene tikudera nkhawa sizichitika n’komwe kapena sizikhala zoipa kwambiri ngati mmene tikuganizira.
Nkhani Yonse ya Mateyu 6:34
Mawu a Yesuwa ali mu ulaliki wake wa paphiri womwe ndi wotchuka kwambiri ndipo umapezeka pa Mateyu chaputala 5 mpaka 7. Pa ulaliki wakewu, Yesu anafotokoza kuti kuda nkhawa kwambiri sikungachititse kuti moyo wathu ukhale wabwino kapena kuutalikitsa. (Mateyu 6:27) Iye ananenanso kuti ngati tikuika Mulungu pamalo oyamba pa moyo wathu, sitiyenera kudera nkhawa kwambiri za mawa. Mulungu amasamalira maluwa komanso nyama ndipo adzasamaliranso anthu amene amamutumikira.—Mateyu 6:25, 26, 28-33.
Werengani Mateyu Chaputala 6, mawu am’munsi ndi malifalensi ake.