Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

KUFOTOKOZA MAVESI A M’BAIBULO

Miyambo 16:3—“Pereka Zochita Zako kwa AMBUYE”

Miyambo 16:3—“Pereka Zochita Zako kwa AMBUYE”

 “Zochita zako zonse uzisiye mʼmanja mwa Yehova, ndipo mapulani ako adzayenda bwino.”—Miyambo 16:3, Baibulo la Dziko Latsopano.

 “Pereka zochita zako kwa AMBUYE, ndipo zolingalira zako zidzakhazikika.”—Miyambo 16:3, New International Version.

Tanthauzo la Miyambo 16:3

 Mwambi umenewu umatsimikizira anthu omwe amalambira Mulungu woona kuti mapulani awo adzayenda bwino ngati angamadalire Mulunguyo komanso kutsatira malangizo ake.

 “Zochita zako zonse uzisiye mʼmanja mwa Yehova.” Anthu omwe amalambira Yehova a amatsatira malangizo ake modzichepetsa asanasankhe zochita. (Yakobo 1:5) N’chifukwa chiyani amatero? Chifukwa chimodzi n’chakuti nthawi zambiri anthufe sitingathe kudziwa kapena kulamulira zochitika pa moyo wathu. (Mlaliki 9:11; Yakobo 4:13-15) Komanso timasowa nzeru zoyendetsera mapulani athuwo. Pa zifukwa zimenezi anthu ambiri amaona kuti ndi nzeru kusiya m’manja mwa Mulungu zochita zawo. Iwo amachita zimenezi popemphera kwa iye kuti awatsogolere komanso kuchita zinthu mogwirizana ndi chifuniro chake monga mmene Baibulo, lomwe ndi Mawu ake, limanenera.—Miyambo 3:5, 6; 2 Timoteyo 3:16, 17.

 Mawu akuti “pereka zochita zako kwa AMBUYE” b m’chilankhulo choyambirira amatanthauza “kupereka ntchito zako kwa AMBUYE.” Malinga ndi buku lina, mawuwa amanena za “munthu yemwe amachotsa katundu pamsana pake n’kumuika pamsana pa munthu wina wamphamvu kuposa iyeyo amenenso angakwanitse kunyamula katunduyo.” Anthu odzichepetsa amadalira Mulungu ndipo samakayikira kuti awathandiza.—Salimo 37:5; 55:22.

 Mawu akuti “zochita zako zonse” sakutanthauza kuti Mulungu adzavomereza kapena kudalitsa mapulani alionse amene anthu angakhale nawo. Kuti Mulungu azitidalitsa, mapulani athu ayenera kukhala ogwirizana ndi zimene iye amafuna komanso mfundo zake. (Salimo 127:1; 1 Yohane 5:14) Mulungu samadalitsa anthu osamvera. Zoona zake n’zakuti, “amasokoneza mapulani a anthu oipa.” (Salimo 146:9) Koma amathandiza anthu amene amasonyeza kuti ndi odzichepetsa pomvera mfundo zomwe iye anakhazikitsa zimene zimapezeka m’Baibulo.—Salimo 37:23.

 “Ndipo mapulani ako adzayenda bwino.” Mabaibulo ena anamasulira mawu amenewa kuti “mapulani ako adzakhazikika.” M’Malemba a Chiheberi kapena kuti Chipangano Chakale, mawu omwe m’Chingelezi anamasuliridwa kuti “adzakhazikika” amafotokoza za kuyala maziko ndipo nthawi zambiri amanena za kukhazikika kwa ntchito zimene Mulungu analenga. (Miyambo 3:19; Yeremiya 10:12) Mofanana ndi zimenezi, Mulungu amakhazikitsa mapulani a anthu amene iye amawaona kuti akuchita zinthu mwachilungamo, amawateteza komanso amawathandiza kuti akhazikike ndiponso azikhala ndi moyo wosangalala.​—Salimo 20:4; Miyambo 12:3.

Nkhani yonse ya pa Miyambo 16:3

 Mwambi umenewu unalembedwa ndi Mfumu Solomo yemwe analemba miyambi yambiri ya m’buku la Miyambo. Iye anakwanitsa kunena miyambi masauzande ambiri chifukwa choti anali ndi nzeru zochokera kwa Mulungu.—1 Mafumu 4:29, 32; 10:23, 24.

 M’chaputala 16, Solomo anayamba ndi kutamanda nzeru za Mulungu komanso anasonyeza kuti Mulungu amadana ndi anthu onyada. (Miyambo 16:1-5) Kenako chaputalachi chimathandiza wowerenga kuti aone mfundo yaikulu yomwe ndi yofunika kwambiri komanso uthenga waukulu wa buku la Miyambo wakuti: Anthu angakhaledi ndi nzeru zenizeni komanso zinthu zingawayendere bwino pokhapokha ngati ali odzichepetsa n’kumalola kuti Mulungu aziwatsogolera pa moyo wawo. (Miyambo 16:3, 6-8, 18-23) Mfundo ya choonadi imeneyi inatchulidwa mobwerezabwereza m’Baibulo.—Salimo 1:1-3; Yesaya 26:3; Yeremiya 17:7, 8; 1 Yohane 3:22.

 Onerani vidiyo yaifupi iyi kuti muone mfundo zazikulu za buku la Miyambo.

a Yehova ndi dzina lenileni la Mulungu. (Salimo 83:18) Werengani nkhani yakuti, “Kodi Yehova Ndi Ndani?

b Mawu oyamba a m’Baibulo lotchedwa New International Version Study Bible amanena kuti Baibuloli linagwiritsa ntchito mawu akuti “AMBUYE” (m’zilembo zazikulu) m’malo amene pali dzina la Mulungu. Mabaibulo enanso anachita zimenezi. Kuti mudziwe chifukwa chake izi zingasokoneze owerenga, onani nkhani yakuti, “Yesaya 42:8​—‘Ine ndine AMBUYE.’