Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

KUFOTOKOZA MAVESI A M’BAIBULO

Miyambo 17:17—“Mnzako Amakusonyeza Chikondi Nthawi Zonse”

Miyambo 17:17—“Mnzako Amakusonyeza Chikondi Nthawi Zonse”

“Mnzako weniweni amakusonyeza chikondi nthawi zonse, ndipo ndi mʼbale amene anabadwa kuti akuthandize pakagwa mavuto.”—Miyambo 17:17, Baibulo la Dziko Latsopano.

“Bwenzi limakonda nthawi zonse, ndipo m’bale anabadwira kuti akuthandize pooneka tsoka.”—Miyambo 17:17, Buku Lopatulika Ndilo Mau a Mulungu.

Tanthauzo la Miyambo 17:17

 Anzathu enieni amakhala odalirika. Mofanana ndi anthu obadwira m’banja limodzi, anzathuwa amakhala okhulupirika komanso amatithandiza, makamaka tikakumana ndi mavuto.

 “Mnzako weniweni amakusonyeza chikondi nthawi zonse.” Mawu amenewa angamasuliridwenso kuti “mabwenzi amakondana nthawi zonse.” Mawu a Chiheberi amene anawamasulira kuti “chikondi” palembali, amaphatikizapo zambiri osangoti mmene munthu amamvera mumtima mwake. Amatanthauza chikondi chopanda dyera chimene munthu amasonyeza mnzake kudzera mu zochita. (1 Akorinto 13:4-7) Anthu omwe amakondana chonchi amagwirizanabe pakakhala kusamvetsetsana kapena mavuto ena. Amakhululukirananso ndi mtima wonse. (Miyambo 10:12) Ndiponso sachitirana nsanje wina zikamuyendera bwino. M’malomwake, amasangalala naye.—Aroma 12:15.

 “Mnzako weniweni . . . ndi mʼbale amene anabadwa kuti akuthandize pakagwa mavuto.” Mwambiwu unachokera pa mfundo yoti anthu obadwira m’banja limodzi ndi amene angakhale ogwirizana kwambiri. Choncho tikamachita zonse zomwe tingathe kuti tithandize mnzathu yemwe ali pa mavuto, timachita zinthu ngati mchimwene kapena mchemwali wake weniweni. Kuwonjezera pamenepa, chikondi chimene chimagwirizanitsa anthu oterewa sichichepa kaya akumane ndi vuto lotani. M’malomwake, anthuwa amagwirizanabe chifukwa chokondana komanso kulemekezana kwambiri.

Nkhani yonse ya pa Miyambo 17:17

 M’buku la Miyambo muli nzeru zothandiza kwambiri zomwe zinalembedwa ngati miyambi ifupiifupi imene imathandiza wowerenga kuti aziganiza. Mfumu Solomo ndi imene inalemba mbali yaikulu ya buku la m’Baibuloli. Mfumuyi inalemba motsatira kalembedwe ka ndakatulo za Chiheberi zimene akamazilemba, m’malo mogwiritsa ntchito mawu omveka mofanana, ankalemba mfundo zofanana komanso ankalemba mfundo zosonyeza kusiyanitsa zinthu pofuna kumveketsa bwino mfundo. Lemba la Miyambo 17:17 ndi chitsanzo cha ndakatulo za mfundo zofanana chifukwa mbali yachiwiri ya lembali ikumveketsa mfundo ya mbali yoyambayo. Lemba la Miyambo 18:24 ndi chitsanzo cha kalembedwe kosiyanitsa zinthu. Lembali limati: “Pali anthu ogwirizana amene ndi okonzeka kuchitirana zoipa, koma pali mnzako amene amakhala nawe pafupi nthawi zonse kuposa mʼbale wako.”

 Pamene ankalemba Miyambo 17:17, mwina Solomo ankaganizira za bambo ake, Davide komanso Yonatani mwana wa Mfumu Sauli, omwe ankagwirizana kwambiri. (1 Samueli 13:16; 18:1; 19:1-3; 20:30-34, 41, 42; 23:16-18) Ngakhale kuti Davide sanali mchimwene wake weniweni wa Yonatani, ankagwirizana kwambiri kuposa anthu abanja limodzi. Yonatani anali wokonzeka ngakhale kufa kumene kuti ateteze mnzake wachinyamatayu. a

Mmene Mabaibulo Ena Anamasulilira Lemba la Miyambo 17:17

 “Mnzako amakukonda nthawi zonse, ndipo amakhala m’bale wako ukakhala pa mavuto.”—The Bible in Basic English.

 “Mnzako amakhala mnzako nthawi zonse, iye ndi m’bale amene anabadwa kuti azikuthandiza ukakumana ndi mavuto.”​—The Moffatt Translation of the Bible.

 “Mnzako amasonyeza kuti ndi mnzako nthawi zonse—m’bale wako [wotereyu] anabadwira kuti azikuthandiza pa mavuto.”—The Complete Jewish Study Bible.

 Onerani vidiyo yaifupiyi kuti muone mwachidule zimene zili m’buku la Miyambo.

a Onani nkhani yakuti “Anagwirizana Kwambiri.”