Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

KUFOTOKOZA MAVESI A M’BAIBULO

Miyambo 3:5, 6​—“Usamadalire Luso Lako Lomvetsa Zinthu”

Miyambo 3:5, 6​—“Usamadalire Luso Lako Lomvetsa Zinthu”

 “Uzikhulupirira Yehova ndi mtima wako wonse, ndipo usamadalire luso lako lomvetsa zinthu. Uzimukumbukira mʼnjira zako zonse, ndipo iye adzawongola njira zako.”​—Miyambo 3:5, 6, Baibulo la Dziko Latsopano.

 “Khulupirira AMBUYE ndi mtima wako wonse ndipo usamadalire luso lako lomvetsa zinthu, uzimugonjera pa zilizonse zimene umachita, ndipo iye adzawongola njira zako.”—Miyambo 3:5, 6, New International Version.

Tanthauzo la Miyambo 3:5, 6

 Tizidalira malangizo ochokera kwa Yehova a Mulungu m’malo modzidalira tikafuna kusankha zochita pa nkhani zofunika kwambiri.

 “Uzikhulupirira Yehova ndi mtima wako wonse.” Timasonyeza kuti timadalira Mulungu tikamachita zinthu mogwirizana ndi mfundo zake. Timafunika kumakhulupirira Mulungu ndi mtima wathu wonse. Nthawi zambiri Baibulo likamanena za mtima, limanena zokhudza mmene munthuwe ulili mumtima mwako, zomwe zikuphatikizapo mmene umamvera, zolinga zako, maganizo ako komanso mmene umaonera zinthu. Choncho, kukhulupirira Mulungu ndi mtima wathu wonse kumaphatikizapo zinthu zambiri osangoti mmene timamvera. Ndi zimene timasankha chifukwa chokhulupirira kwambiri kuti Mlengi wathu amadziwa zinthu zomwe ndi zothandiza kwambiri kwa ife.—Aroma 12:1.

 “Usamadalire luso lako lomvetsa zinthu.” Popeza si ife angwiro, timafunika kudalira Mulungu osati luso lathu la kuganiza. Tikamadzidalira kapena kumangochita zinthu chifukwa cha mmene tikumvera, tikhoza kusankha zinthu zomwe poyamba zingaoneke zabwino koma zotsatira zake zingakhale zoipa. (Miyambo 14:12; Yeremiya 17:9) Nzeru za Mulungu ndi zapamwamba kwambiri kuposa zathu. (Yesaya 55:8, 9) Tikamatsogoleredwa ndi maganizo ake, zinthu zimatiyendera bwino.—Salimo 1:1-3; Miyambo 2:6-9; 16:20.

 “Uzimukumbukira mʼnjira zako zonse.” Timafunika kuyendera maganizo a Mulungu pa zinthu zofunika kwambiri pa moyo wathu komanso tikamasankha zochita pa nkhani zikuluzikulu. Timachita zimenezi tikamapemphera kwa iye kuti azititsogolera ndiponso tikamatsatira zimene amatiuza m’Mawu ake, Baibulo.—Salimo 25:4; 2 Timoteyo 3:16, 17.

 “Iye adzawongola njira zako.” Mulungu amawongola njira zathu potithandiza kuti tizitsatira mfundo zake zolungama pa moyo wathu. (Miyambo 11:5) Zimenezi zimatithandiza kuti tisamakumane ndi mavuto opeweka ndipo timakhala moyo wosangalala kwambiri.​—Salimo 19:7, 8; Yesaya 48:17, 18.

Nkhani yonse ya pa Miyambo 3:5, 6

 Buku la m’Baibulo la Miyambo lili ndi mfundo zotithandiza kukhala ndi moyo wosangalala, womwenso umasangalatsa Mulungu. Machaputala 9 oyambirira, analembedwa ngati kuti bambo akupereka malangizo kwa mwana wake wamwamuna wokondedwa. Chaputala 3 chimafotokoza madalitso amene anthu amapeza chifukwa chokonda komanso kugwiritsa ntchito nzeru za Mlengi wathu.—Miyambo 3:13-26.

a Yehova ndi dzina lenileni la Mulungu.—Salimo 83:18.