KUFOTOKOZA MAVESI A M’BAIBULO
Mlaliki 3:11—“Chilichonse Iye Anachipanga Chokongola Ndiponso pa Nthawi Yake”
“Chilichonse iye anachipanga chokongola ndiponso pa nthawi yake. Komanso anapatsa anthu mtima wofuna kukhala ndi moyo mpaka kalekale kuti ntchito imene Mulungu woona wagwira, iwo asaidziwe kuyambira pa chiyambi mpaka pa mapeto.”—Mlaliki 3:11, Baibulo la Dziko Latsopano.
“Chinthu chilichonse anachikongoletsa pa mphindi yake; ndipo waika zamuyaya m’mitima yao ndipo palibe munthu angalondetse ntchito Mulungu wazipanga chiyambire mpaka chitsiriziro.”—Mlaliki 3:11, Buku Lopatulika Ndilo Mau a Mulungu.
Tanthauzo la Mlaliki 3:11
“Chilichonse iye anachipanga chokongola ndiponso pa nthawi yake.” Mawu a Chiheberi omwe anawamasulira kuti “chokongola” angatanthauze zambiri kuposa maonekedwe akunja. Angamasuliridwenso kuti “zoikidwa mwadongosolo,” “zabwino” kapenanso “zoyenera.” (Mlaliki 3:11,) Zinthu zokongola zimene Mulungu analenga zimaphatikizaponso zinthu zonse zimene iye amachita pofuna kukwaniritsa cholinga chake.—Danieli 2:21; 2 Petulo 3:8; Chivumbulutso 4:11.
“Anapatsa anthu mtima wofuna kukhala ndi moyo mpaka kalekale.” Mulungu analenga anthu kuti azikhala ndi moyo kwamuyaya. (Salimo 37:29) Iye anawapatsanso mtima wofuna kukhala ndi moyo mpaka kalekale. Koma banja loyambirira, Adamu ndi Hava, silinamvere Mulungu ndipo zimenezi zinachititsa kuti iwo limodzi ndi ana awo azifa. (Genesis 3:17-19; Aroma 5:12) Ngakhale zili choncho, Mulungu analonjeza kuti ‘adzakhutiritsa zokhumba za chamoyo chilichonse,’ zomwe zikuphatikizapo mtima wofuna kukhala ndi moyo mpaka kalekale. (Salimo 145:16) Baibulo limafotokoza zimene Yehova anachita kuti anthu adzakhalenso ndi mwayi wokhala ndi moyo wosatha.—Aroma 6:23.
“Iwo asaidziwe kuyambira pa chiyambi mpaka pa mapeto.” Nzeru za Mulungu n’zozama kwambiri komanso n’zochuluka ndipo Baibulo limati palibe ‘angatulukire njira zake.’ (Aroma 11:33) Komabe, Mulungu ndi wofunitsitsa kuthandiza anthu amene amafuna kuchita zinthu zomusangalatsa kuti adziwe zolinga zake.—Amosi 3:7.
Nkhani yonse ya pa Mlaliki 3:11
Buku la Mlaliki linalembedwa ndi Mfumu Solomo wa ku Isiraeli wakale, yemwe ndi munthu wodziwika chifukwa cha nzeru zimene Mulungu anamupatsa. Bukuli lili ndi malangizo othandiza munthu kudziwa zinthu zothandiza pa moyo wake ndi zimene zili zopanda phindu. (Mlaliki 1:2, 3; 2:1, 17; 7:1; 12:1, 13) Muchaputala 3, Solomo anafotokoza zina mwa zinthu zosiyanasiyana zimene zimachitika pa moyo wa munthu. (Mlaliki 3:1-8, 10) Mulungu anapereka ufulu woti anthu asankhe zinthu zimene angachite komanso nthawi yomwe angachitire zinthuzo. (Deuteronomo 30:19, 20; Yoswa 24:15) Solomo anafotokozanso kuti anthu angasangalale ndi zotsatira za ntchito yabwino yomwe aigwira mwakhama ngati akuchita zinthu mogwirizana ndi cholinga cha Mulungu komanso ngati amachita zinthu mogwirizana ndi “nthawi yake,” kutanthauza yomwe Mulungu amachitira zinthu. Solomo anati “imeneyi ndi mphatso yochokera kwa Mulungu.”
Onerani vidiyo yaifupiyi kuti mumvetse bwino nkhani ya m’buku la Mlaliki.