Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

KUFOTOKOZA MAVESI A M’BAIBULO

Salimo 37:4​—“Udzikondweretsenso Mwa Yehova”

Salimo 37:4​—“Udzikondweretsenso Mwa Yehova”

 “Komanso sangalala mwa Yehova, ndipo adzakupatsa zokhumba za mtima wako.”​—Salimo 37:4, Baibulo la Dziko Latsopano.

 “Udzikondweretsenso mwa Yehova, ndipo iye adzakupatsa zokhumba mtima wako.”​—Salimo 37:4, Buku Lopatulika Ndilo Mau a Mulungu.

Tanthauzo la Salimo 37:4

 Wolemba masalimo analimbikitsa atumiki a Mulungu kuti azisangalala chifukwa chokhala pa ubwenzi wabwino ndi Mulunguyo. Anthu onse amene ali pa ubwenzi umenewu, amakhala otsimikiza kuti Yehova a Mulungu adzakwaniritsa zinthu zabwino zimene amalakalaka.

 “Sangalala mwa Yehova.” Mawuwa angatanthauzenso kuti “sangalala kwambiri mwa Yehova,” “sangalala potumikira Yehova,” kapena “sangalala ndi zimene Yehova wakulonjeza.” Mwachidule, tiyenera “kumasangalala kwambiri” pamene tikulambira Mulungu woona. (Salimo 37:4, mawu a m’munsi Baibulo la Dziko Latsopano la Chingelezi) N’chifukwa chiyani zili choncho?

 Anthu amene amalambira Yehova amaona zinthu mmene iye amazionera mogwirizana ndi zimene Baibulo limanena. Si kuti iwo amangodziwa Mulungu, koma amaonanso kuti n’zofunika kwambiri kuti azimumvera. Zimenezi zimawathandiza kuti azikhala ndi chikumbumtima chabwino, azisankha bwino zinthu komanso azipewa mavuto ambiri. (Miyambo 3:5, 6) Mwachitsanzo, sapsa mtima kapena kuchita nsanje akamaona kuti anthu adyera komanso opanda chilungamo zinthu zikuwayendera bwino. (Salimo 37:1, 7-9) Anthu a Mulungu amasangalala podziwa kuti posachedwapa iye adzathetsa zopanda chilungamo zonse ndi kupereka mphoto kwa onse omwe amachita zinthu mokhulupirika. (Salimo 37:34) Iwo amasangalalanso podziwa kuti Atate wawo wa kumwamba akusangalala nawo.​—Salimo 5:12; Miyambo 27:11.

 “Adzakupatsa zokhumba za mtima wako.” Mawuwa angamasuliridwenso kuti “adzayankha mapemphero anu” kapena “adzakupatsani zomwe mukufunitsitsa.” Koma sikuti Yehova amayankha pemphero lililonse. Mofanana ndi kholo labwino, iye amadziwa zimene ana ake angafunikiredi. Ndipo zopempha zathu komanso mmene timachitira zinthu pa moyo wathu, ziyenera kukhala zogwirizana ndi chifuniro chake. (Miyambo 28:9; Yakobo 4:3; 1 Yohane 5:14) Zikatero tingakhale otsimikiza kuti “Wakumva pemphero” atiyankha pemphero lathu.​—Salimo 65:2; Mateyu 21:22.

Nkhani yonse ya pa Salimo 37:4

 Salimo 37 linalembedwa ndi Davide yemwe anali Mfumu ya Isiraeli. Iye analemba salimoli potsatira afabeti. b

 Davide anavutika ndi zinthu zambiri zopanda chilungamo. Iye ankasakidwa ndi Mfumu Sauli komanso anthu ena omwe ankafuna kumupha. (2 Samueli 22:1) Komabe, Davide ankadalira Mulungu nthawi zonse. Iye ankadziwa kuti tsiku lina Yehova adzalanga anthu onse oipa. (Salimo 37:10, 11) Ngakhale ataoneka kuti zinthu zikuwayendera bwino ngati “msipu watsopano wobiriwira” n’kupita kwa nthawi iwo sadzapezekaponso.​—Salimo 37:2, 20, 35, 36.

 Salimo 37 limasiyanitsa zimene zimachitikira anthu amene amatsatira malamulo a Mulungu ndi amene samumvera. (Salimo 37:16, 17, 21, 22, 27, 28) Choncho salimoli limatithandiza kuti tikhale anzeru komanso anthu amene Mulungu amasangalala nawo.

 Onerani vidiyo yaifupiyi kuti mumvetse bwino nkhani ya m’buku la Masalimo.

a Dzina lenileni la Mulungu lochokera m’Chiheberi nthawi zambiri m’Chichewa limamasuliridwa kuti Yehova. Kuti mudziwe chifukwa chake Mabaibulo ambiri amagwiritsa ntchito dzina la udindo lakuti Ambuye m’malo mwa dzina lenileni la Mulungu, werengani nkhani yakuti, “Kodi Yehova Ndi Ndani?

b Potsatira njirayi, vesi loyamba kapena gulu loyamba la mavesi limayamba ndi chilembo choyambirira cha afabeti ya Chiheberi ndipo mavesi otsatira amayamba ndi chilembo chachiwiri mpaka kumapeto. Kalembedwe kameneka kayenera kuti kankathandiza anthu kuti azikumbukira salimoli.