KUFOTOKOZA MAVESI A M’BAIBULO
Yesaya 41:10—“Usachite Mantha, Pakuti Ndili Nawe”
“Usachite mantha, pakuti ndili nawe. Usayang’ane uku ndi uku mwamantha, pakuti ine ndine Mulungu wako. Ndikulimbitsa. Ndithu ndikuthandiza. Ndikugwira mwamphamvu ndi dzanja langa lamanja lachilungamo.”—Yesaya 41:10, Baibulo la Dziko Latsopano.
“Usaope, pakuti Ine ndili pamodzi ndi iwe; usaopsedwe, pakuti Ine ndine Mulungu wako; ndidzakulimbitsa; inde, ndidzakuthangata; inde ndidzakuchirikiza ndi dzanja langa lamanja la chilungamo.”—Yesaya 41:10, Buku Lopatulika Ndilo Mau a Mulungu.
Tanthauzo la Yesaya 41:10
Yehova a Mulungu anatsimikizira anthu amene amamulambira mokhulupirika kuti adzawathandiza ngakhale atakumana ndi mavuto aakulu kwambiri.
“Ndili nawe.” Yehova anauza anthu omulambira kuti sayenera kuopa chifukwa sali okha. Popeza Yehova amaona zimene anthuwo akupirira komanso amamva mapemphero awo, zili ngati iye ali pamodzi nawo.—Salimo 34:15; 1 Petulo 3:12.
“Ine ndine Mulungu wako.” Yehova anakhazikitsa mtima pansi anthu omulambira powakumbutsa kuti iye amaonabe kuti ndi Mulungu wawo ndipo iwo ndi anthu ake. Sayenera kukayikira kuti iye adzawathandiza zivute zitani.—Salimo 118:6; Aroma 8:32; Aheberi 13:6.
“Ndikulimbitsa. Ndithu ndikuthandiza. Ndikugwira mwamphamvu ndi dzanja langa lamanja lachilungamo.” Yehova anagwiritsa ntchito mfundo zitatu pofuna kutsindika mfundo imodzi yakuti iye sangalephere ngakhale pang’ono kuthandiza anthu ake. Anagwiritsa ntchito mawu ophiphiritsa posonyeza zimene amachita anthu ake akafunika kuthandizidwa. Munthu akagwa, Mulungu angamupatse dzanja lake lamanja kuti amudzutse.—Yesaya 41:13.
Njira yaikulu imene Mulungu amalimbitsira komanso kuthandiza anthu ake ndi kugwiritsa ntchito Mawu ake, Baibulo. (Yoswa 1:8; Aheberi 4:12) Mwachitsanzo, m’Baibulo muli malangizo anzeru othandiza anthu amene akukumana ndi mavuto monga umphawi, matenda kapena kuferedwa. (Miyambo 2:6, 7) Mulungu angagwiritsenso ntchito mzimu wake woyera, kapena kuti mphamvu yake yogwira ntchito, kuti azipatsa anthu ake mphamvu zopirira mavuto awo.—Yesaya 40:29; Luka 11:13.
Nkhani Yonse ya Yesaya 41:10
Mawuwa analimbikitsa Ayuda okhulupirika omwe anadzatengedwa kupita ku ukapolo ku Babulo. Yehova ananeneratu kuti chakumapeto kwa ukapolowo, kudzakhala malipoti okhudza mdani amene akubwera kudzawononga mitundu yowazungulira komanso kuopseza Babulo. (Yesaya 41:2-4; 44:1-4) Ababulo ndi mitundu yoyandikana nayo idzachita mantha kwambiri ndi malipotiwa koma Ayuda sadzayenera kuda nkhawa chifukwa Yehova adzawateteza. Iye anawatsimikizira zimenezi katatu powauza kuti: “Usachite mantha”—Yesaya 41:5, 6, 10, 13, 14.
N’zoona kuti poyamba Yehova Mulungu ananena mawuwa kuti alimbikitse Ayuda okhulupirika omwe anadzapita ku ukapolo ku Babulo. Koma anachititsa kuti mawu a Yesaya 41:10 asungidwe m’Baibulo n’cholinga choti azilimbikitsa anthu ake onse. (Yesaya 40:8; Aroma 15:4) Iye amathandiza anthu ake masiku ano mofanana ndi mmene ankachitira m’mbuyomu.
Werengani Yesaya chaputala 41, mawu am’munsi ndi malifalensi ake.
a Yehova ndi dzina la Mulungu.—Salimo 83:18.