Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

KUFOTOKOZA MAVESI A M’BAIBULO

Yesaya 42:8—“Ine ndine AMBUYE”

Yesaya 42:8—“Ine ndine AMBUYE”

“Ine ndine Yehova. Dzina langa ndi limeneli. Ndipo sindipereka ulemu wanga kwa wina aliyense. Kapena kupereka ulemerero wanga kwa zifaniziro zogoba.”—Yesaya 42:8, Baibulo la Dziko Latsopano.

“Ine ndine AMBUYE. Dzina langa ndi limeneli. Ndipo sindipereka ulemu wanga kwa wina aliyense. Kapena kupereka ulemerero wanga kwa zifaniziro zogoba.”—Yesaya 42:8, King James Version.

Tanthauzo la Yesaya 42:8

Palembali, Mulungu akutiuza dzina lake ndipo akunena kuti sapereka ulemu kapena ulemerero wake kwa mafano.

Mulungu anadzipatsa yekha dzina limeneli lomwe kawirikawiri limamasuliridwa kuti “Yehova” m’Chichewa. a (Ekisodo 3:14, 15) Ngakhale kuti dzinali limapezeka maulendo pafupifupi 7,000 m’Chipangano Chatsopano (Malemba a Chiheberi ndi Chiaramu), omasulira ambiri ankachotsa dzinali n’kuikapo dzina la udindo lakuti “AMBUYE” (m’zilembo zazikulu). Chitsanzo ndi lemba la Salimo 110:1, limene limalosera za Yehova ndi Yesu. M’Baibulo la King James Version, analemba kuti: “AMBUYE [Yehova ] anati kwa Mbuye wanga [Yesu].” (Machitidwe 2:34-36) Mu Baibulo la Dziko Latsopano munthu sangasokonezeke ndi “Ambuye” awiri chifukwa anabwezeretsa dzina la Mulungu pamalo ake oyenera. Limanena kuti: “Yehova anauza Ambuye wanga kuti: ‘Khala kudzanja langa lamanja.kufikira nditaika adani ako monga chopondapo mapazi ako.’”

Akatswiri ambiri amakhulupirira kuti dzina la Mulunguli limatanthauza kuti “Amachititsa Zinthu Kuchitika.” Mulungu woona yekha ndi amene angakhale ndi dzina limeneli. Tikutero chifukwa iye yekha ndi amene angadzichititse kukhala chilichonse chimene chikufunika, kapena kuchititsa zinthu zimene analenga kukhala chilichonse chimene chikufunika, kuti akwaniritse cholinga chake.

Yehova ndi Mlengi wathu komanso ndi Mulungu woona yekha choncho ndi wofunika tizidzipereka kwa iye. Sitiyenera kulambira aliyense kapena chilichonse kuphatikizapo mafano kapena zifaniziro.—Ekisodo 20:2-6; 34:14; 1 Yohane 5:21.

Nkhani Yonse ya pa Yesaya 42:8

Kumayambiriro kwa Yesaya chaputala 42, Yehova ananeneratu za ntchito ya mtumiki ‘amene wamusankha.’ Ananena kuti mtumikiyo adzabweretsa “chilungamo kwa anthu amitundu ina.” (Yesaya 42:1) Pofotokoza za lonjezoli, Mulungu anati: “Ndikukuuzani zinthu zatsopano. Zisanayambe kuonekera ndimakuuzani.” (Yesaya 42:9) Ulosi wonena za mtumiki wosankhidwa ndi Mulungu unayamba kuonekera patapita zaka zambiri pamene Mesiya kapena kuti Khristu anafika n’kuyamba utumiki wake padzikoli.—Mateyu 3:16, 17; 12:15-21.

Lemba la Yesaya 42:8 M’Mabaibulo Ena

“Ine ndine Yehova dzina langa ndi lomweli; ndipo ulemerero wanga Ine sindidzapereka kwa wina .”—Buku Lopatulika Ndilo Mawu a Mulungu.

“Ndine Yahve; nali dzina langa, ndipo sindidzapatsa munthu aliyense ulemu wanga; sindidzaninkha mafano ulemu wanga.”—Malembo Oyera.

a M’Chiheberi, dzina la Mulungu limalembedwa ndi zilembo zitatu zomwe nthawi zambiri zimaimiridwa ndi “YHWH.” Omasulira ena amalemba dzina la Mulungu kuti “Yahweh.” Kuti mumve zambiri onani zakumapeto A4 pamutu wakuti “Dzina la Mulungu M’malemba Achiheberi” m’Baibulo la Dziko Latsopano.