Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

KUFOTOKOZA MAVESI A M’BAIBULO

Yoswa 1:9​—“Ukhale Wolimba Mtima Ndipo Uchite Zinthu Mwamphamvu”

Yoswa 1:9​—“Ukhale Wolimba Mtima Ndipo Uchite Zinthu Mwamphamvu”

 “Monga ndakulamula kale, ukhale wolimba mtima ndipo uchite zinthu mwamphamvu. Usachite mantha kapena kuopa, pakuti Yehova Mulungu wako ali nawe kulikonse kumene upiteko.”​—Yoswa 1:9, Baibulo la Dziko Latsopano.

 “Kodi sindinakulamulira iwe? Khala wamphamvu, nulimbike mtima, usaope, kapena kutenga nkhawa, pakuti Yehova Mulungu wako ali ndi iwe kuli konse umukako.”​—Yoswa 1:9, Buku Lopatulika Ndilo Mau a Mulungu.

Tanthauzo la Yoswa 1:9

 Yehova a Mulungu ananena mawuwa potsimikizira Yoswa, yemwe ankamulambira mokhulupirika, kuti angakhale ‘wolimba mtima n’kumachita zinthu mwamphamvu’ ngakhale atakumana ndi mavuto aakulu kwambiri. Ngati Yoswa akanamvera malamulo a Mulungu, sakanayenera kuopa zam’tsogolo chifukwa Mulungu akanakhala ngati ali pafupi naye pomuthandiza kuti zinthu zizimuyendera bwino. Yehova analidi ndi Yoswa chifukwa ankamupatsa malangizo komanso kumuthandiza kuti agonjetse adani ake.

 N’chiyani chikanathandiza Yoswa kuti akhale ‘wolimba mtima n’kumachita zinthu mwamphamvu’? Iye akanalimbikitsidwa komanso kupatsidwa mphamvu ndi Malemba ochokera kwa Yehova omwe analipo pa nthawiyo. Malembawa anaphatikizapo ‘malamulo onse amene mtumiki wa Yehova Mose analamula’ Yoswa. b (Yoswa 1:7) Yehova anauza Yoswa kuti ‘asinkhesinkhe malamulowo usana ndi usiku.’ (Yoswa 1:8) Kuwerenga ndi kusinkhasinkha Malembawo kunalimbitsa maganizo komanso mtima wa Yoswa kuti azichita zinthu zimene Mulungu amafuna. Kenako Yoswa ankafunika kuchita zimene ankaphunzira m’Mawu a Mulunguwo, kapena kuti ‘kuonetsetsa kuti akutsatira zonse zolembedwamo.’ Ngati akanachita zimenezi, akanachita zinthu mwanzeru komanso zinthu zikanamuyendera bwino. Ndipo izi n’zimene zinachitikadi. Ngakhale kuti ankakumana ndi mavuto, Yoswa anali ndi moyo wabwino komanso wosangalala potumikira Yehova mokhulupirika.​—Yoswa 23:14; 24:15.

 Mawu amene Yehova anauza Yoswa amatilimbikitsabe masiku ano. Amasonyeza kuti Yehova amaganizira anthu amene amamulambira, makamaka pamene akukumana ndi mavuto. Ndipo amafuna kuti zinthu ziziwayendera bwino ngati mmene zinalili ndi Yoswa. Mofanana ndi Yoswa, iwonso angakhale ‘olimba mtima n’kumachita zinthu mwamphamvu.’ Angatero akamawerenga ndi kusinkhasinkha Mawu a Mulungu komanso kuchita zinthu mogwirizana ndi malangizo ake.

Nkhani yonse ya Yoswa 1:9

 Mose atamwalira, Yehova anauza Yoswa kuti azitsogolera Aisiraeli. (Yoswa 1:1, 2) Pa nthawi imeneyo n’kuti Aisiraeli atatsala pang’ono kulowa m’Dziko Lolonjezedwa, kapena kuti dziko la Kanani. Koma kunali adani amphamvu. Mwachitsanzo, Yoswa ankafunika kumenyana nkhondo ndi Akanani, omwe anali anthu oipa kwambiri. c (Deuteronomo 9:5; 20:17, 18) Akanani analiponso ambiri ndipo anali ndi zida zambiri zankhondo poyerekezera ndi Aisiraeli. (Yoswa 9:1, 2; 17:18) Koma Yoswa ankatsatira malangizo a Yehova molimba mtima. Ndipotu Mulungu analidi ndi Yoswa chifukwa Aisiraeli anagonjetsa ambiri mwa adani awo m’zaka 6 zokha.​—Yoswa 21:43, 44.

a Dzina lakuti Yehova linamasuliridwa kuchokera ku dzina la Mulungu m’Chiheberi, lomwe limalembedwa ndi zilembo 4 za Chiheberi zakuti יהוה (kapena kuti YHWH). M’Mabaibulo ena dzinali linamasuliridwa kuti “Ambuye” m’vesi limeneli. Kuti mudziwe zambiri zokhudza Yehova komanso chifukwa chake Mabaibulo ena sagwiritsa ntchito dzinali, onani nkhani yakuti “Kodi Yehova Ndi Ndani?

b Malemba amene Yoswa anali nawo komanso amene tonse tili nawo masiku ano m’Baibulo, ayenera kuti anaphatikizapo mabuku 5 amene Mose analemba (Genesis, Ekisodo, Levitiko, Numeri ndi Deuteronomo), buku la Yobu komanso Salimo limodzi kapena awiri.

c Kuti mudziwe chifukwa chake nkhondo ngati zimenezi zinali zofunika, onani nkhani yakuti “N’chifukwa Chiyani Mulungu Anawononga Akanani?” mu Nsanja ya Olonda ya January 1, 2010.