KODI ZINANGOCHITIKA ZOKHA?
Luso la Galu Lotha Kununkhiza Zinthu
Ochita kafukufuku amanena kuti galu amatha kugwiritsa ntchito luso lake lomva fungo kuti adziwe msinkhu wa galu mnzake, ngati mnzakeyo ndi wamwamuna kapena wamkazi, kapenanso kuti adziwe mmene galu mnzake akumvera. Galu akhozanso kuphunzitsidwa kuti azitha kuzindikira pamene pali mabomba kapenanso mankhwala osavomerezeka ndi boma. Anthufe nthawi zambiri timadalira maso kuti tifufuze zimene zikuchitika pamalo amene tili, pomwe galu amadalira luso lake lotha kununkhiza. M’mawu ena tingati, galu amaona ndi mphuno.
Taganizirani izi: Galu ali ndi luso lotha kumva fungo mofulumira kwambiri kuposa anthufe. Pakafukufuku yemwe bungwe lina linachita ku United States, linapeza kuti galu akhoza kumva fungo la chinthu ngakhale chitasungunulidwa kwambiri. Zimene ananena pofotokoza mfundoyi ndi zofanana ndi kukwanitsa kuzindikira shuga wosakwana hafu ya sipuni yaing’ono, yemwe wathiridwa m’madzi a mudamu losambiriramo lalikulu ngati hafu ya bwalo lampira.
Kodi n’chiyani chimathandiza galu kuti azitha kumva fungo kwambiri chonchi?
Mphuno ya galu imakhala yonyowa zomwe zimathandiza kuti izikola fungo mosavuta.
Mphuno ya galu inagawidwa mbali ziwiri, ina yothandiza popuma pomwe inayo ndi imene amanunkhizira. Galu akanunkhiza chinthu, mpweya wochokera pa chinthucho umalowera mbali yonunkhizirayo osati yopumira.
Mkati mwa mphuno ya chinthu chilichonse muli kachigawo kamene kamathandiza chinthucho kumva fungo. Mu mphuno ya galu, kachigawoka kamatha kukula mpaka masentimita 130 kapena kuposerapo, pomwe mu mphuno ya munthu kachigawoka kamakhala ka masentimita 5 okha.
Galu akhoza kukhala ndi maselo othandizira kumva fungo ochuluka maulendo 50 kuposa maselo amene anthufe tili nawo.
Zimenezi n’zomwe zimathandiza galu kuti azitha kusiyanitsa fungo la zinthu, moti ngati zinthu zambirimbiri zitasakanizidwa pamodzi, galu amatha kumva fungo la chinthu chilichonse pachokhapachokha. Mwachitsanzo, akatswiri ena amanena kuti, anthufe tikhoza kumva kununkhira kwa supu, koma galu amatha kudziwa kena kalikonse komwe kaikidwa mu supuyo.
Ochita kafukufuku a bungwe la Pine Street Foundation, omwe amafufuza zokhudza matenda a khansa amanena kuti ubongo komanso mphuno za galu zimachita zinthu mogwirizana kwambiri n’kukhala ngati “zipangizo zamakono kwambiri zotha kuzindikira fungo la zinthu zovuta kuzizindikira.” Asayansi akupanga zipangizo zogwira ntchito ngati mphuno za galu zoti zizitha kuzindikira mabomba, katundu wosavomerezeka ndi boma komanso matenda osiyanasiyana, kuphatikizapo khansa.
Kodi inuyo mukuganiza bwanji? Kodi zinangochitika zokha kuti galu akhale ndi luso lotha kununkhiza zinthu chonchi? Kapena pali winawake amene anamulenga ndi luso limeneli?