KODI ZINANGOCHITIKA ZOKHA?
Zonanda za Nsomba Yangati Mlamba
Kwa nthawi yaitali, asayansi akhala akuchita chidwi ndi zinthu zinazake zonanda zomwe nsomba zinazake zimatulutsa (m’Chingelezi nsombazi zimatchedwa hagfish). Koma kodi n’chifukwa chiyani akufunitsitsa kudziwa zambiri zokhudza zinthu zonandazi? Akatswiri amanena kuti zinthuzi ndi zodabwitsa chifukwa “ndi zofewa kwambiri komanso zimatamuka kwambiri.”
Taganizirani izi: Nsomba zomwe zimatulutsa zonandazi ndi zooneka ngati mlamba ndipo zimakhala pansi pa nyanja zikuluzikulu. Nsombazi zikazindikira kuti kukubwera adani, zimayamba kutulutsa zinthu zonandazi zomwe zimapangidwa ndi mapuloteni ataliatali kwambiri. Mapuloteniwa amagwirana n’kuchititsa kuti madzi omwe azungulira anande. Zinthu zonandazi zimachititsa kuti chimene chinkafuna kudya nsombayi chiyambe kubanika n’kuilavula ndipo chimathawa nthawi yomweyo.
Kunena zoona, zinthu zimenezi ndi zochititsa chidwi kwambiri. Mapuloteni omwe amapanga zinthuzi amakhala aang’ono kwambiri moti kuphatikiza pamodzi timaulusi ta mapuloteni okwana 100 akhoza kumaoneka ngati tsitsi la munthu kunenepa kwake. Komatu kaulusi kalikonse kamakhala kamphamvu maulendo 10 kuposa ulusi wolimba kwambiri womwe anthu amapangira zovala. Nsomba zija zikalavulira zinthu zonandazi m’madzi, zimakhala ngati sefa ndipo zimatha kuimitsa madzi amphamvu kwambiri mwina maulendo 26,000 kuposa kulemera kwake. Chodabwitsa n’choti pafupifupi 100 peresenti ya zinthu zimenezi imakhalanso madzi.
Asayansi akhala akulephera kupanga zinthu zofanana nazo. Munthu wina yemwe amachita kafukufuku wa zinthu zonandazi anati: “Zinthu zimenezi zimapangidwa mwachilengedwe koma ndi zogometsa kwambiri.” Asayansi akuyesayesa kupanga timaulusi topangidwa ndi mapuloteni pogwiritsa ntchito mabakiteriya. Cholinga chawo ndi choti azidzagwiritsa ntchito ulusiwu popanga zinthu zopepuka kwambiri, zosang’ambika chisawawa, zotamuka kwambiri komanso zosaononga chilengedwe. Ngati atakwaniritsa kuchita zimenezi, akhoza kumapanga ulusi wolimba kwambiri womwe ungamagwiritsidwe ntchito popanga nsalu komanso zinthu zina zogwiritsa ntchito kuchipatala. Ndipo ulusi umenewu ukhoza kumadzagwiritsidwa ntchito zinanso zambirimbiri.
Kodi inuyo mukuganiza bwanji? Kodi zinangochitika zokha kuti nsombazi zizitulutsa zinthu zodabwitsazi? Kapena pali winawake amene anazilenga?