Wolembedwa na Maliko 2:1-28
2 Koma patapita masiku angapo, iye analoŵanso mu mzinda wa Kaperenao, ndipo anthu anamva kuti ali kunyumba.
2 Conco, anthu ambili anasonkhana m’nyumbamo, moti munalibiletu malo ngakhale pafupi na khomo. Kenako iye anayamba kuwauza uthenga wabwino.
3 Ndiyeno anthu anamubweletsela munthu wofa ziwalo, atanyamulidwa na amuna anayi.
4 Koma iwo sanakwanitse kufikitsa munthuyo pomwe panali Yesu cifukwa ca kuculuka kwa anthu. Conco, anakasula mtenje pamwamba pa malo pomwe panali Yesu, n’kupanga cibowo. Kenako analoŵetselapo macila amene panagona munthu wofa ziwalo uja.
5 Yesu ataona cikhulupililo cawo, anauza wofa ziwaloyo kuti: “Mwanawe, macimo ako akhululukidwa.”
6 Ena mwa alembi anali khale pomwepo, ndipo mu mtima anali kunena kuti:
7 “N’cifukwa ciyani munthu uyu akulankhula conci? Akunyoza Mulungu. Ndani wina angakhululukile munthu macimo kupatulapo Mulungu?”
8 Koma mwa mzimu wake, nthawi yomweyo Yesu anazindikila zimene iwo anali kuganiza m’mitima yawo. Conco anawafunsa kuti: “N’cifukwa ciyani mukuganiza zimenezi m’mitima yanu?
9 Kodi capafupi n’citi, kuuza munthu wofa ziwaloyu kuti, ‘Macimo ako akhululukidwa,’ kapena kukamba kuti, ‘Nyamuka, tenga macila ako uyambe kuyenda’?
10 Koma kuti mudziŵe kuti Mwana wa munthu ali na mphamvu zokhululukila anthu macimo pa dziko lapansi—” Iye anauza wofa ziwaloyo kuti:
11 “Nikukuuza kuti, Nyamuka, nyamula macila akowa, pita ku nyumba kwanu.”
12 Pamenepo munthuyo ananyamuka, ndipo nthawi yomweyo ananyamula macila ake n’kuyamba kuyenda onse akuona. Conco anthu onsewo anadabwa kwambili, ndipo anatamanda Mulungu n’kumati: “Zotelezi sitinazionepo.”
13 Kenako iye anapitanso m’mbali mwa nyanja, ndipo khamu lonse la anthu linali kupitabe kwa iye. Ndiyeno anayamba kuwaphunzitsa.
14 Pamene iye anali kudutsa, anaona Levi mwana wa Alifeyo atakhala pansi mu ofesi yokhomelamo misonkho. Ndipo anamuuza kuti: “Khala wotsatila wanga.” Nthawi yomweyo iye ananyamuka na kumutsatila.
15 Patapita nthawi, Yesu anali kudya m’nyumba ya Levi, ndipo okhometsa misonkho ambili komanso ocimwa anali kudya naye pamodzi na ophunzila ake, cifukwa ambili mwa iwo anali kumutsatila.
16 Koma alembi a Afarisi ataona kuti iye akudya na anthu ocimwa komanso okhometsa misonkho, anayamba kufunsa ophunzila ake kuti: “Kodi munthu ameneyu amadya na okhometsa misonkho komanso ocimwa?”
17 Yesu atamva zimenezi anawauza kuti: “Anthu olimba safunikila dokotala, koma odwala ndiwo amamufunikila. Ine n’nabwela kudzaitana anthu ocimwa, osati olungama.”
18 Ophunzila a Yohane komanso Afarisi anali kusala kudya. Conco iwo anabwela kwa Yesu n’kumufunsa kuti: “N’cifukwa ciyani ife ophunzila a Yohane komanso ophunzila a Afarisi timasala kudya, koma ophunzila anu sasala kudya?”
19 Yesu anawayankha kuti: “Mkwati akakhala pamodzi na anzake, anzakewo sasala kudya, amatelo kodi? Pa nthawi yonse imene mkwatiyo ali nawo limodzi, iwo sangasale kudya.
20 Koma masiku adzafika pamene mkwatiyo adzacotsedwa pakati pawo, ndipo pa tsikulo adzasala kudya.
21 Palibe munthu amene amasokelela cigamba ca nsalu yatsopano pa covala cakunja cakale. Akatelo, cigamba catsopanoco cimaguza covala cakaleco, ndipo pong’ambikapo pamakula kwambili.
22 Komanso palibe amene amathila vinyo watsopano m’matumba acikumba akale. Akatelo matumba a vinyowo amaphulika, ndipo vinyoyo amatayika, matumbawo n’kuwonongeka. Koma vinyo watsopano amamuthila m’matumba acikumba atsopano.”
23 Pamene iye anali kudutsa m’minda ya tiligu pa Sabata, ophunzila ake anayamba kuthyola ngala za tiligu pamene anali kuyenda.
24 Conco Afarisi anamufunsa kuti: “Onani! N’cifukwa ciyani akucita zosaloleka pa Sabata?”
25 Koma iye anawayankha kuti: “Kodi simunaŵelengepo zimene Davide anacita cakudya citamuthela, komanso pamene iye na amuna amene anali naye anamva njala?
26 Nkhani yokamba za Abiyatara wansembe wamkulu, imakamba kuti Davide analoŵa m’nyumba ya Mulungu n’kudya mkate wa cionetselo, ndipo mitanda ina ya mkatewo anapatsako ena mwa amuna amene anali naye. Koma mwalamulo, palibe amene anali kuloledwa kudya mkatewo kupatulapo ansembe.”
27 Kenako Yesu anawauza kuti: “Sabata linakhalapo cifukwa ca munthu, osati munthu kukhalapo cifukwa ca Sabata.
28 Conco Mwana wa munthu ndiye Mbuye wa Sabata.”