Wolembedwa na Maliko 3:1-35

  • Munthu wa dzanja lopuwala acilitsidwa (1-6)

  • Khamu lalikulu la anthu m’mbali mwa nyanja (7-12)

  • Atumwi 12 (13-19)

  • Kunyoza mzimu woyela (20-30)

  • Mayi a Yesu na abale ake (31-35)

3  Pa nthawi inanso Yesu analoŵa m’sunagoge, ndipo m’sunagogemo munali munthu wina wopuwala* dzanja.  Conco Afarisi anali kumuyang’anitsitsa kuti aone ngati angacilitse munthuyo pa Sabata. Colinga cawo cinali cakuti amuimbe mlandu.  Ndiyeno Yesu anauza munthu wopuwala* dzanjayo kuti: “Nyamuka bwela apa pakati.”  Kenako anawafunsa kuti: “Kodi cololeka n’citi pa Sabata, kucita cabwino kapena coipa? Kupulumutsa moyo kapena kupha?” Koma iwo anangokhala cete.  Yesu anawayang’ana mokwiya ndipo anamva cisoni kwambili poona kuuma mitima kwawo. Kenako anauza munthuyo kuti: “Tambasula dzanja lako.” Iye analitambasuladi, ndipo linakhala bwino.  Zitatelo Afarisiwo anatuluka, ndipo nthawi yomweyo anayamba kukambilana na acipani ca Herode zakuti amuphe.  Koma Yesu anacoka n’kupita ku nyanja pamodzi na ophunzila ake, ndipo khamu lalikulu la anthu ocokela ku Galileya komanso ku Yudeya linamutsatila.  Ngakhalenso anthu ambili ocokela ku Yerusalemu, ku Idumeya, ku tsidya lina la Yorodani komanso kumadela a Turo na Sidoni, anabwela kwa iye atamva zinthu zambili zimene anali kucita.  Ndipo iye anauza ophunzila ake kuti amubweletsele bwato laling’ono loti akwelemo kuti khamulo lisam’panikize. 10  Cifukwa cakuti anacilitsa anthu ambili, onse amene anali na matenda aakulu, anamuunjilila kuti angomukhudza. 11  Ngakhale mizimu yonyansa ikamuona inali kudzigwetsa pansi n’kufuula kuti: “Inu ndinu Mwana wa Mulungu.” 12  Koma mobweleza-bweleza iye anali kuilamula mwamphamvu kuti isamuulule. 13  Yesu anakwela m’phili n’kuitana anthu amene anali kuwafuna, ndipo iwo anapita kwa iye. 14  Ndiyeno anapanga* gulu la anthu 12, amenenso anawacha atumwi. Anthu amenewa anali oti aziyenda naye komanso kuti aziwatuma kukalalikila 15  na kuwapatsa mphamvu zotulutsa ziŵanda. 16  Ndipo pa gulu la anthu 12 amenewo panali Simoni, amene anamupatsanso dzina lakuti Petulo, 17  Yakobo mwana wa Zebedayo na Yohane m’bale wake wa Yakobo (Aŵiliŵa anawapatsanso dzina lakuti Bowanege, kutanthauza “Ana a Bingu”), 18  Andireya, Filipo, Batulomeyo, Mateyo, Thomasi, Yakobo mwana wa Alifeyo, Tadeyo, Simoni Kananiya,* 19  komanso Yudasi Isikariyoti amene pambuyo pake anapeleka Yesu. Ndiyeno iye ataloŵa m’nyumba, 20  khamu la anthu linasonkhananso, moti iwo sanathe ngakhale kudya cakudya. 21  Koma acibale ake atamva nkhaniyi, anapita kukamugwila, cifukwa anali kunena kuti: “Ameneyu wafuntha.” 22  Komanso, alembi amene anacokela ku Yerusalemu anali kunena kuti: “Ali na Belezebule* ndipo amatulutsa ziŵanda na mphamvu za wolamulila ziŵanda.” 23  Conco atawaitana anayamba kulankhula nawo mwa mafanizo kuti: “Kodi Satana angatulutse bwanji Satana? 24  Ngati ufumu wagaŵikana, ufumuwo sukhalitsa; 25  ndipo ngati nyumba yagaŵikana, nyumbayo singalimbe. 26  Mofanana na zimenezi, ngati Satana wadziukila yekha, ndipo wagaŵikana, iye sangakhalitse koma amenewo adzakhala mapeto ake. 27  Kukamba zoona, palibe aliyense angaloŵe m’nyumba ya munthu wamphamvu kuti amubele katundu, asanayambe wam’manga munthu wamphamvuyo. Akamumanga m’pamene angathe kutenga zinthu m’nyumbamo. 28  Ndithu nikukuuzani kuti, ana a anthu adzakhululukidwa zinthu zonse, kaya anacita macimo otani komanso kaya analankhula mawu onyoza otani. 29  Koma aliyense wonyoza mzimu woyela sadzakhululukidwa kwamuyaya.” 30  Iye anakamba izi cifukwa iwo anali kumunena kuti: “Ali na mzimu wonyansa.” 31  Tsopano amayi ake na abale ake anabwela n’kuimilila panja. Kenako anatuma winawake kuti akamuitane. 32  Panali khamu la anthu limene linakhala pansi momuzungulila, ndipo iwo anamuuza kuti: “Mayi anu na abale anu ali panja ndipo akukufunani.” 33  Koma iye anawayankha kuti: “Kodi mayi anga na abale anga ndani?” 34  Ndiyeno anayang’ana anthu amene anakhala pansi momuzungulila aja n’kunena kuti: “Ona! Awa ndiwo amayi anga na abale anga! 35  Aliyense wocita cifunilo ca Mulungu ameneyo ndiye m’bale wanga, mlongo wanga, komanso mayi anga.”

Mawu a m'Munsi

Kapena kuti, “wolemala.”
Kapena kuti, “wolemala.”
Kapena kuti, “anasankha.”
Kapena kuti, “wokangalika.”
Dzina lina la Satana.