Wolembedwa na Maliko 4:1-41

  • MAFANIZO ONENA ZA UFUMU (1-34)

    • Wofesa mbewu (1-9)

    • Cifukwa cake Yesu anaseŵenzetsa mafanizo (10-12)

    • Kufotokoza tanthauzo la fanizo la wofesa mbewu (13-20)

    • Nyale saibwinikila na thadza (21-23)

    • Muyeso umene mukupimila ena (24, 25)

    • Wofesa mbewu amene amagona (26-29)

    • Kanjele ka mpilu (30-32)

    • Kuseŵenzetsa mafanizo (33, 34)

  • Yesu aleketsa cimphepo camkuntho (35-41)

4  Yesu anayambanso kuphunzitsa m’mbali mwa nyanja, ndipo cikhamu ca anthu cinasonkhana pafupi na iye. Conco iye anakwela m’bwato n’kukhala m’bwatomo capatali pang’ono na anthuwo. Koma khamu lonse la anthulo linali m’mbali mwa nyanjayo.  Iye anayamba kuwaphunzitsa zinthu zambili mwa mafanizo, ndipo powaphunzitsa anawauza kuti:  “Tamvelani! Munthu wina anapita kukafesa mbewu.  Pamene anali kufesa mbewuzo, zina zinagwela m’mbali mwa msewu, ndipo mbalame zinabwela n’kuzidya.  Zina zinagwela pa miyala pomwe panalibe dothi lokwanila, ndipo zinamela mwamsanga cifukwa nthaka inali yosazama.  Koma dzuŵa litatentha zinaŵauka, ndipo zinafota cifukwa zinalibe mizu.  Mbewu zina zinagwela pa minga, ndipo mingazo zitakula zinalepheletsa mbewuzo kukula moti sizinabale cipatso ciliconse.  Koma mbewu zina zinagwela pa nthaka yabwino, ndipo zitamela n’kukula, zinayamba kubala zipatso. Mbewu zina zinabala zipatso 30, zina 60, ndipo zina 100.”  Kenako anawonjezela kuti: “Amene ali na matu akumva, amve.” 10  Tsopano pamene Yesu anali payekha, anthu amene anali naye komanso atumwi 12 aja anayamba kumufunsa za mafanizowo. 11  Iye anawauza kuti: “Inu mwapatsidwa mwayi womvetsa cinsinsi copatulika ca Ufumu wa Mulungu. Koma kwa aja amene ali kunja zinthu zonse zimakambidwa mwa mafanizo, 12  kuti kuyang’ana aziyang’ana ndithu, koma osaona. Kumva azimva ndithu koma osamvetsa tanthauzo lake, komanso kuti asatembenuke n’kukhululukidwa.” 13  Anawauzanso kuti: “Ngati fanizoli simukulimvetsa, ndiye kodi mudzamvetsa bwanji mafanizo ena onse? 14  “Wofesa amafesa mawu. 15  Cotelo mbewu zimene zimagwela m’mbali mwa msewu ni mawu amene amafesedwa mwa anthu omwe amati akangomva mawuwo, Satana amabwela n’kucotsa mawu amene afesedwa mwa iwo. 16  Mofananamo, mbewu zimene zafesedwa pa miyala ni mawu amene amafesedwa mwa anthu amene akangomva mawuwo amawalandila mwacimwemwe. 17  Ngakhale n’telo, mawuwo sazika mizu mwa iwo. Koma anthuwo amapitiliza kwa kanthawi. Ndiyeno cisautso kapena mazunzo akangobwela cifukwa ca mawuwo, iwo amapunthwa. 18  Palinso mbewu zina zimene zimafesedwa pa minga. Mbewu zimenezi ni anthu amene amamva mawu, 19  koma nkhawa za nthawi ino* na cinyengo camphamvu ca cuma komanso kulakalaka zinthu zina zonse, zimaloŵa m’mitima yawo na kulepheletsa mawuwo kukula ndipo sabala zipatso. 20  Cothela, mbewu zimene zinafesedwa pa nthaka yabwino ni anthu amene amamva mawu na kuwalandila bwino, ndipo amabala zipatso wina 30, wina 60, ndiponso wina 100.” 21  Iye anawauzanso kuti: “Nyale saibwinikila na thadza* kapena kuiika kunsi kwa bedi, amatelo kodi? Kodi saiika pa coikapo nyale? 22  Pakuti palibe cobisika cimene sicidzaululika. Ndipo palibe cobisidwa mosamala kwambili cimene sicidzaonekela poyela. 23  Amene ali na matu akumva, amve.” 24  Anawauzanso kuti: “Mvetselani mosamala zimene mukumva. Muyeso umene mukupimila ena inunso adzakupimilani womwewo. Inde adzakuwonjezelani zoculuka. 25  Pakuti aliyense amene ali nazo adzapatsidwa zoculuka, koma aliyense amene alibe adzalandidwa ngakhale zimene ali nazo.” 26  Iye anapitiliza kukamba kuti: “Ufumu wa Mulungu uli monga mmene munthu amamwazila mbewu pa nthaka. 27  Iye amagona usiku ndipo kukaca amauka. Mbewuzo zimamela na kukula, koma iye sadziŵa mmene izi zimacitikila. 28  Pang’ono-pang’ono, nthakayo payokha imabala zipatso. Umene umayamba ni mmela, kenako ngala, pothela pake maso okhwima m’ngalamo. 29  Koma mbewuzo zikangoti zaca, iye amazimweta na cikwakwa cifukwa nthawi yokolola yakwana.” 30  Ndiyeno anapitiliza kuwauza kuti: “Kodi Ufumu wa Mulungu tingauyelekezele na ciyani, kapena tingaufotokoze na fanizo lotani? 31  Uli ngati kanjele ka mpilu kamene pa nthawi yofesa kamakhala kakang’ono kwambili kuposa njele zonse pa dziko lapansi. 32  Koma kakafesedwa kamamela na kukula kwambili kuposa mbewu zina zonse za kudimba. Ndipo kamapanga nthambi zikulu-zikulu, moti mbalame za mumlengalenga zimapeza malo okhala mu mthunzi wake.” 33  Iye analankhula nawo mogwilitsa nchito mafanizo ambili otelo malinga na zimene akanakwanitsa kumvetsa. 34  Ndithudi, sanalankhule nawo popanda fanizo, koma kumbali iye anali kuwafotokozela zinthu zonse ophunzila ake. 35  Tsiku limenelo madzulo, iye anauza ophunzila ake kuti: “Tiyeni tiwolokele ku tsidya lina la nyanja.” 36  Conco atauza khamu la anthulo kuti lizipita, ophunzilawo anamutenga n’kupita naye m’bwato, mmene analilimo. Pafupi na bwatolo, panalinso mabwato ena. 37  Ndiyeno kunayamba cimphepo camphamvu camkuntho, ndipo mafunde anali kuwomba bwatolo moti linatsala pang’ono kumila. 38  Koma iye anali gone kumbuyo m’bwatomo atasamila pilo. Conco anamuutsa na kumufunsa kuti: “Mphunzitsi, kodi sizikukukhudzani kuti tikufa?” 39  Pamenepo ananyamuka na kudzudzula mphepoyo, n’kuuza nyanjayo kuti: “Cete! Khala bata!” Mphepoyo inaleka, ndipo panakhala bata lalikulu. 40  Ndiyeno iye anawafunsa kuti: “N’cifukwa ciyani mukucita mantha conci? Kodi mulibiletu cikhulupililo mpaka pano?” 41  Koma iwo anacita mantha kwambili, ndipo anayamba kufunsana, amvekele: “Kodi ameneyu ndani makamaka? Ngakhale mphepo na nyanja zikumumvela!”

Mawu a m'Munsi

Kapena kuti, “thadza lopimila.”