Wolembedwa na Maliko 7:1-37

  • Kuvumbula miyambo ya anthu (1-13)

  • Zodetsa munthu zimacokela mu mtima (14-23)

  • Cikhulupililo ca mayi wacisirofoinike (24-30)

  • Munthu wogontha acilitsidwa (31-37)

7  Tsopano Afarisi na alembi ena amene anacokela ku Yerusalemu anasonkhana kwa Yesu.  Ndipo iwo anaona ena mwa ophunzila ake akudya cakudya na manja odetsedwa, kapena kuti cosasamba m’manja.*  (Pakuti Afarisi na Ayuda onse sakudya cakudya asanasambe m’manja kufika mu kakonyokonyo.* Iwo amacita izi potsatila mwambo wa makolo awo akale.  Ndipo akacoka ku msika, sakudya cakudya asanasambe. Palinso miyambo ina yambili imene iwo analandila ndipo amaitsatila, monga mwambo woviika makapu m’madzi, mitsuko, na ziwiya zakopa.)  Conco Afarisi na alembiwo anamufunsa kuti: “N’cifukwa ciyani ophunzila anu sasunga miyambo ya makolo akale, koma amadya cakudya na manja odetsedwa?”  Iye anawauza kuti: “Yesaya analosela molondola za onyenga inu pamene analemba kuti, ‘Anthu awa amanilemekeza na milomo yawo cabe, koma mitima yawo ili kutali na ine.  Iwo amanipembedza pacabe cifukwa amaphunzitsa malamulo a anthu monga ziphunzitso za Mulungu.’  Mumanyalanyaza malamulo a Mulungu n’kumamatila miyambo ya anthu.”  Kuwonjezela apo, iye anawauza kuti: “Mocenjela mumakankhila pambali malamulo a Mulungu kuti musunge miyambo yanu. 10  Mwa citsanzo, Mose anati, ‘Uzilemekeza atate ako na amayi ako,’ komanso anati, ‘Aliyense wonyoza atate ake kapena amayi ake ayenela kuphedwa.’ 11  Koma inu mumati, ‘Ngati munthu wauza atate ake kapena amayi ake kuti: “Ciliconse cimene nili naco, cimene nikanakuthandizani naco, ni Khobani (kutanthauza mphatso yoyenela kupelekedwa kwa Mulungu),”’ 12  simumulola kucitila atate ake kapena amayi ake ciliconse. 13  Mwa kutelo, mwapangitsa mawu a Mulungu kukhala opanda phindu cifukwa ca miyambo yanu imene munaipeleka kwa anthu. Ndipo mumacita zinthu zambili zotelezi.” 14  Conco ataitananso gulu la anthuwo anawauza kuti: “Nimvetseleni nonsenu, ndipo mumvetsetse tanthauzo lake. 15  Palibe ciliconse cocokela kunja kwa munthu cimene cikaloŵa m’thupi lake cingamudetse. Koma zinthu zimene zimatuluka mwa munthu n’zimene zimamudetsa.” 16 * —— 17  Ndiyeno ataloŵa m’nyumba inayake kutali na gulu la anthulo, ophunzila ake anayamba kumufunsa za fanizo lija. 18  Conco anawafunsa kuti: “Kodi inunso simukumvetsa ngati anthu aja? Kodi simukudziŵa kuti palibe ciliconse cocokela kunja kwa munthu cimene cikaloŵa m’thupi mwake cingamudetse? 19  Pakuti siciloŵa mu mtima mwake koma m’mimba, ndipo cimakatuluka ku cimbudzi.” Mwa kukamba zimenezi, Yesu anagamula kuti zakudya zonse n’zoyela. 20  Anakambanso kuti: “Cotuluka mwa munthu n’cimene cimamudetsa. 21  Pakuti mkati, mumtima mwa anthu ni mmene mumatuluka maganizo oipa monga: zaciwelewele,* zakuba, zakupha anthu, 22  zacigololo, dyela, kucita zoipa, cinyengo, khalidwe lotayilila,* diso lakaduka, manyozo, kudzikuza, na kucita zinthu mopanda nzelu. 23  Zinthu zoipa zonsezi zimacokela mumtima mwa munthu ndipo zimamudetsa.” 24  Iye anacoka kumeneko n’kupita kumadela a Turo na Sidoni. Ali kumeneko, analoŵa m’nyumba inayake, ndipo sanafune kuti munthu aliyense adziŵe kuti ali kumeneko. Koma anthu anadziŵabe. 25  Nthawi yomweyo mayi wina amene mwana wake wamng’ono wamkazi anagwidwa na mzimu wonyansa anamva za iye, ndipo anabwela n’kugwada kumapazi ake. 26  Mayiyu anali Mgiriki wacisirofoinike.* Iye anapempha Yesu mobweleza-bweleza kuti atulutse ciŵanda mwa mwana wakeyo. 27  Koma Yesu anamuuza kuti: “Ana ayenela kukhuta coyamba, cifukwa n’kosayenela kutenga cakudya ca ana n’kuponyela tuagalu.” 28  Koma mayiyo anayankha kuti: “N’zoona mbuyanga, koma ngakhale tuagalu tumene tuli pansi pa thebulo tumadya nyenyeswa za anawo.” 29  Pamenepo Yesu anauza mayiyo kuti: “Cifukwa ca zimene wakambazi, pita. Ciŵanda cija catuluka mwa mwana wako.” 30  Conco mayiyo anapita ku nyumba kwake, ndipo anapeza mwana wamng’ono uja ali gone pabedi ciŵanda cija citatuluka. 31  Pamene Yesu anali kubwelela kucokela ku dela la Turo kupita ku Nyanja ya Galileya anapitila m’dela la Sidoni komanso m’cigawo ca Dekapoli.* 32  Kumeneko, anthu anamubweletsela munthu wogontha komanso wosalankhula, ndipo anamucondelela kuti aike dzanja lake pa iye. 33  Ndiyeno anatengela munthuyo pambali capatali na gulu la anthulo. Kenako anapisa zala zake m’matu a munthuyo, ndipo atalavula mata anakhudza lilime la munthuyo. 34  Ndiyeno atayang’ana kumwamba, anafuza mwamphamvu n’kunena kuti: “Efata,” kutanthauza, “Tseguka.” 35  Atakamba izi, makutu ake anatseguka ndipo vuto lake losalankhula linatha, moti anayamba kulankhula bwino-bwino. 36  Ndiyeno anawalamula kuti asauze aliyense zimene zinacitikazo. Koma amati akawalamula mwamphamvu, m’pamenenso anthuwo anali kufalitsa kwambili nkhaniyo. 37  Inde, iwo anazizwa kosaneneka, amvekele: “Wacita zonse bwino-bwino. Akucititsa ngakhale ogontha kumva, na osalankhula kulankhula!”

Mawu a m'Munsi

Kutanthauza, kusayeletsedwa motsatila mwambo.
Ena amati, “kasukusuku.”
Mawu a pa vesiyi amapezeka m’ma Baibo ena, koma sapezeka m’mipukutu yosiyana-siyana yodalilika yamakedzana ya Cigiriki.
Mu Cigiriki ni por·nei′a. Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Kapena kuti, “khalidwe lopanda manyazi.” Mu Cigiriki a·sel′gei·a.
Cioneka kuti mayiyu anabadwila ku Foinike.
Kapena kuti, “Cigawo ca Mizinda 10.”