Wolembedwa na Mateyo 13:1-58

  • MAFANIZO ONENA ZA UFUMU (1-52)

    • Wofesa mbewu (1-9)

    • Cifukwa cake Yesu anali kuseŵenzetsa mafanizo (10-17)

    • Kufotokoza tanthauzo la wofesa mbewu (18-23)

    • Tiligu na namsongole (24-30)

    • Kanjele ka mpilu na zofufumitsa (31-33)

    • Kuseŵenzetsa mafanizo kunakwanilitsa ulosi (34, 35)

    • Kufotokoza tanthauzo la tiligu na namsongole (36-43)

    • Cuma cobisika na ngale yamtengo wapatali (44-46)

    • Khoka (47-50)

    • Cuma catsopano komanso cakale (51, 52)

  • Yesu akanidwa kwawo (53-58)

13  Tsiku limenelo Yesu anacoka pa nyumbayo n’kukakhala pansi m’mbali mwa nyanja.  Ndiyeno khamu lalikulu la anthu linasonkhana kwa iye moti anakwela m’bwato n’kukhala pansi, ndipo anthu onsewo anaimilila m’mbali mwa nyanjayo.  Kenako anayamba kuwauza zinthu zambili mwa mafanizo, kuti: “Tamvelani! Munthu wina anapita kukafesa mbewu.  Pamene anali kufesa mbewuzo, zina zinagwela m’mbali mwa msewu, ndipo mbalame zinabwela n’kuzidya.  Zina zinagwela pa miyala pamene panalibe dothi lokwanila, ndipo zinamela mwamsanga cifukwa nthaka inali yosazama.  Koma dzuŵa litatentha zinaŵauka, kenako zinauma cifukwa zinalibe mizu.  Mbewu zina zinagwela pa minga, ndipo mingazo zitakula, zinalepheletsa mbewuzo kukula.  Koma mbewu zina zinagwela pa nthaka yabwino, ndipo zinayamba kubala zipatso, mbewu iyi zipatso 100, ina 60, inanso 30.  Ali na matu amve.” 10  Conco ophunzila ake anabwela na kumufunsa kuti: “N’cifukwa ciyani mumalankhula nawo mwa mafanizo?” 11  Poyankha iye anati: “Inu mwapatsidwa mwayi womvetsa zinsinsi za Ufumu wa kumwamba, koma iwo sanapatsidwe mwayi umenewo. 12  Pakuti aliyense amene ali nazo adzapatsidwa zambili, ndipo adzakhala na zoculuka, koma aliyense amene alibe adzalandidwa ngakhale zimene ali nazo. 13  Ndiye cifukwa cake nimalankhula nawo mwa mafanizo. Pakuti kuona amaona, koma kuona kwawo n’kopanda phindu, ndipo kumva amamva koma kumva kwawo n’kopanda phindu komanso samvetsa tanthauzo lake. 14  Ndipo ulosi wa Yesaya ukukwanilitsidwa pa iwo. Ulosiwo umati: ‘Kumva mudzamva ndithu, koma simudzamvetsa tanthauzo lake. Kuona mudzaona ndithu, koma simudzazindikila zimene mukuona. 15  Pakuti anthu awa aumitsa mitima yawo, ndipo amva na matu awo koma osacitapo kanthu, komanso atseka maso awo. Acita zimenezi kuti asaone na maso awo komanso kuti asamve na matu awo. Zotulukapo zake n’zakuti samvetsa tanthauzo lake m’mitima yawo n’kutembenuka kuti ine niwacilitse.’ 16  “Koma inu ndinu odala cifukwa maso anu amaona, ndipo matu anu amamva. 17  Pakuti ndithu nikukuuzani, kuti aneneli ambili komanso anthu olungama, anali kulakalaka kuona zimene inu mukuona na kumva zimene inu mukumva. 18  “Tsopano mvetselani tanthauzo la fanizo la munthu wofesa mbewu uja. 19  Munthu aliyense akamva mawu a Ufumu koma osamvetsa tanthauzo lake, woipayo amabwela n’kucotsa zimene zafesedwa mu mtima mwake. Izi ndizo mbewu zimene zinagwela m’mbali mwa msewu. 20  Mbewu zogwela pa miyala ni munthu amene amamva mawu, n’kuwalandila mwacimwemwe nthawi yomweyo. 21  Ngakhale n’conco, mawuwo sazika mizu mwa iye,* koma amapitiliza kwa kanthawi. Ndipo mazunzo kapena cisautso cikabwela cifukwa ca mawuwo, amapunthwa nthawi yomweyo. 22  Mbewu zogwela pa minga ni munthu amene amamva mawu, koma nkhawa za nthawi ino* komanso cinyengo camphamvu ca cuma, zimalepheletsa mbewuzo kukula, ndipo sizibala zipatso. 23  Koma mbewu zogwela pa nthaka yabwino ni munthu amene amamva mawu na kumvetsa tanthauzo lake, amene amabaladi zipatso, uyu zipatso 100, wina 60, komanso wina 30.” 24  Iye anawauzanso fanizo lina. Anati: “Ufumu wa kumwamba uli ngati munthu amene anafesa mbewu yabwino m’munda wake. 25  Anthu ali m’tulo, mdani wake anabwela n’kufesa namsongole m’munda wa tiliguwo, kenako anapita. 26  Mmelawo utakula na kutulutsa ngalangala, nayenso namsongole anaonekela. 27  Conco akapolo a mwinimunda uja anabwela n’kumufunsa kuti, ‘Ambuye, sipaja munafesa mbewu yabwino m’munda mwanu? Nanga namsongole wacokela kuti?’ 28  Poyankha iye anawauza kuti, ‘Munthu wina wodana nane ndiye anacita zimenezi.’ Akapolowo anamufunsa kuti, ‘Ndiye kodi tipite tikamuzule namsongoleyo?’ 29  Iye anawayankha kuti, ‘Ayi, kuopela kuti pozula namsongoleyo, mungazulile pamodzi na tiligu. 30  Zilekeni zikulile pamodzi mpaka nthawi yokolola, ndipo m’nyengo yokolola nidzauza okololawo kuti: Coyamba sonkhanitsani namsongole n’kumumanga mitolo-mitolo kuti akatenthedwe, kenako sonkhanitsani tiligu n’kumuika mu nkhokwe yanga.’” 31  Iye anawauzanso fanizo lina kuti: “Ufumu wa kumwamba uli ngati kanjele ka mpilu kamene munthu anatenga n’kukabyala m’munda wake. 32  Kanjele kameneka nikakang’ono kwambili pa mbewu zonse. Koma kamakula kuposa mbewu zonse za kudimba n’kukhala mtengo, moti mbalame za mumlengalenga zimapeza malo okhala m’nthambi zake.” 33  Anawauzanso fanizo lina kuti: “Ufumu wa kumwamba uli ngati zofufumitsa zimene mayi wina anatenga n’kuzisakaniza na ufa wokwana mbale zitatu zikulu-zikulu zopimila, ndipo mtanda wonsewo unafufuma.” 34  Yesu analankhula zinthu zonsezi na khamulo mwa mafanizo. Ndithudi sanalankhule nawo popanda fanizo, 35  kuti mawu amene ananenedwa kudzela mwa mneneli akwanilitsidwe, akuti: “Nidzatsegula pakamwa panga na kunena mafanizo. Nidzalengeza zinthu zimene zakhala zobisika kucokela pa ciyambi.”* 36  Ndiyeno atauza khamu la anthulo kuti lizipita analoŵa m’nyumba. Ophunzila ake anabwela kwa iye n’kunena kuti: “Tifotokozeleni tanthauzo la fanizo lija la namsongole m’munda.” 37  Iye anawayankha kuti: “Wofesa mbewu yabwino ni Mwana wa munthu; 38  ndipo mundawo ni dzikoli. Mbewu yabwino ni ana a Ufumu, koma namsongole ni ana a woipayo, 39  ndipo mdani amene anafesa namsongoleyo ni Mdyelekezi. Nthawi yokolola ndiyo cimalizilo ca nthawi ino,* ndipo okololawo ni angelo. 40  Conco monga mmene namsongole amamusonkhanitsila pamodzi na kumutentha pamoto, ni mmenenso zidzakhalila pa cimalizilo ca nthawi ino.* 41  Mwana wa munthu adzatumiza angelo ake amene adzacotsa mu Ufumu wake zinthu zonse zopunthwitsa kuphatikizapo anthu osamvela malamulo, 42  ndipo adzawaponya mu ng’anjo ya moto. Kumeneko azikalila na kukukuta mano. 43  Pa nthawiyo olungama adzawala kwambili ngati dzuŵa mu Ufumu wa Atate wawo. Ali na matu amve. 44  “Ufumu wa kumwamba uli ngati cuma cobisika m’munda, cimene munthu wina anapeza n’kucibisa. Ndipo cifukwa ca cimwemwe cimene anali naco, anapita kukagulitsa zinthu zonse zimene anali nazo n’kukagula mundawo. 45  “Komanso Ufumu wa kumwamba uli ngati wamalonda woyenda-yenda amene anali kufuna-funa ngale zabwino. 46  Atapeza ngale imodzi yamtengo wapatali anapita, ndipo mwamsanga anagulitsa zinthu zonse zimene anali nazo n’kukagula ngaleyo. 47  “Ndiponso Ufumu wa kumwamba uli ngati khoka lalikulu limene linaponyedwa m’nyanja, ndipo linasonkhanitsa nsomba za mitundu-mitundu. 48  Litadzala analikokela ku mtunda, ndipo atakhala pansi anasonkhanitsa nsomba zabwino n’kuziika m’madengu, koma zoipa anazitaya. 49  Ni mmenenso zidzakhalila pa mapeto a nthawi ino.* Angelo adzapita n’kukacotsa oipa pakati pa olungama, 50  ndipo adzawaponya mu ng’anjo ya moto. Kumeneko azikalila na kukukuta mano. 51  “Kodi mwamvetsa tanthauzo la zinthu zonsezi?” Iwo anamuyankha kuti: “Inde.” 52  Ndiyeno anawauza kuti: “Poti zili telo, mphunzitsi aliyense wa anthu amene waphunzitsidwa za Ufumu wa kumwamba, ali ngati mwininyumba, amene amatulutsa zinthu zatsopano komanso zakale mosungila cuma cake.” 53  Yesu atatsiliza kuwauza mafanizo amenewa anacoka kumeneko. 54  Atafika m’dela la kwawo anayamba kuphunzitsa anthu m’sunagoge wawo, moti anthuwo anadabwa kwambili ndipo anati: “Kodi munthu ameneyu anazitenga kuti nzelu na nchito zamphamvu zimenezi? 55  Kodi ameneyu si mwana wa kalipentala uja? Kodi mayi ake si Mariya, ndipo abale ake si Yakobo, Yosefe, Simoni na Yudasi? 56  Komanso alongo ake onse sitili nawo konkuno? Nanga zonsezi anazitenga kuti?” 57  Conco anayamba kupunthwa cifukwa ca iye. Koma Yesu anawauza kuti: “Mneneli salemekezedwa kwawo kapena panyumba pake, koma kwina.” 58  Cotelo sanacite nchito zambili zamphamvu kumeneko cifukwa ca kusoŵa cikhulupililo kwawo.

Mawu a m'Munsi

Kapena kuti, “mawuwo samufika pa mtima.”
Kamasulidwe kena, “kucokela pa kukhazikitsidwa kwa dziko.”