Wolembedwa na Mateyo 15:1-39
15 Ndiyeno Afarisi na alembi anabwela kwa Yesu kucokela ku Yerusalemu n’kumufunsa kuti:
2 “N’cifukwa ciyani ophunzila anu amanyozela miyambo ya makolo? Mwa citsanzo, iwo sasamba* m’manja akafuna kudya cakudya.”
3 Powayankha iye anati: “Nanga n’cifukwa ciyani inuyo mumaphwanya malamulo a Mulungu cifukwa ca miyambo yanu?
4 Mwa citsanzo Mulungu anati, ‘Uzilemekeza atate ako na amayi ako,’ komanso anati, ‘Aliyense wonyoza atate ake na amayi ake ayenela kuphedwa.’
5 Koma inu mumati, ‘Aliyense wouza atate ake kapena amayi ake kuti: “Ciliconse cimene nili naco, cimene nikanakuthandizani naco ni mphatso yoyenela kupelekedwa kwa Mulungu,”
6 munthuyo asawalemekeze* n’komwe atate ake.’ Conco mwapangitsa mawu a Mulungu kukhala opanda phindu cifukwa ca miyambo yanu.
7 Onyenga inu, Yesaya analosela molondola za inu pamene anati:
8 ‘Anthu awa amanilemekeza na milomo yawo cabe, koma mitima yawo ili kutali na ine.
9 Iwo amanipembedza pacabe cifukwa amaphunzitsa malamulo a anthu monga ziphunzitso za Mulungu.’”
10 Atakamba zimenezi, anaitana khamu la anthulo kuti libwele pafupi, ndipo anaŵauza kuti: “Mvetselani na kumvetsetsa tanthauzo lake:
11 Coloŵa m’kamwa mwa munthu si cimene cimamudetsa, koma cotuluka m’kamwa mwake n’cimene cimamudetsa.”
12 Ndiyeno ophunzilawo anabwela kwa iye n’kumuuza kuti: “Kodi mudziŵa kuti Afarisi akhumudwa na zimene mwakamba?”
13 Poyankha iye anati: “Mbewu iliyonse imene sinabyalidwe na Atate wanga wa kumwamba idzazulidwa.
14 Alekeni amenewo. Iwo ni atsogoleli akhungu. Cotelo ngati munthu wakhungu akutsogolela wakhungu mnzake, onse aŵili adzagwela m’dzenje.”
15 Petulo anati: “Timasulileni fanizo lija.”
16 Pamenepo Yesu anati: “Kodi inunso simukumvetsa mpaka pano?
17 Kodi simudziŵa kuti ciliconse coloŵa m’kamwa cimapita m’mimba, kenako cimakatayidwa ku cimbudzi?
18 Koma zilizonse zotuluka pakamwa zimacokela mu mtima, ndipo zimenezo n’zimene zimaipitsa munthu.
19 Mwa citsanzo, mumtima mumatuluka maganizo oipa monga: zakupha, zacigololo, zaciwelewele,* zakuba, maumboni onama komanso zonyoza Mulungu.
20 Izi n’zimene zimadetsa munthu. Koma kudya cakudya cosasamba* m’manja sikudetsa munthu.”
21 Atacoka kumeneko, Yesu anapita ku cigawo ca Turo na Sidoni.
22 Ndiyeno mayi wina wa ku Foinike, wocokela m’cigawo cimeneco, anabwela kwa iye n’kufuula kuti: “Ambuye, Mwana wa Davide, nicitileni cifundo. Mwana wanga wamkazi wagwidwa na ciŵanda ndipo akuzunzika koopsa.”
23 Koma Yesu sanamuyankhe ciliconse. Conco, ophunzila ake anapita kwa iye n’kumuuza kuti: “Muuzeni azipita, cifukwa akufuulabe n’kumatilondola.”
24 Poyankha iye anati: “Ine sin’natumidwe kwa wina aliyense koma kwa nkhosa zosocela za mtundu wa Isiraeli.”
25 Koma mayiyo anafika pafupi na Yesu, ndipo anamugwadila n’kunena kuti: “Ambuye, nithandizeni!”
26 Iye anamuyankha kuti: “N’kosayenela kutenga cakudya ca ana n’kuponyela tuagalu.”
27 Mayiyo anati: “N’zoona Ambuye, koma ngakhale tuana twa agalu tumadya nyenyeswa zakugwa pa thebulo la ambuye awo.”
28 Ndiyeno Yesu anamuyankha kuti: “Mayi iwe, cikhulupililo cako n’cacikulu. Zimene wapempha zicitike.” Nthawi yomweyo mwana wake anacila.
29 Yesu atacoka kumeneko, anapita kufupi na nyanja ya Galileya, ndipo anakwela m’phili n’kukhala pansi.
30 Tsopano kunafika khamu lalikulu la anthu limene linamubweletsela anthu olemala, othyoka ziwalo, akhungu, osalankhula, na ena ambili. Iwo anaika anthuwo pafupi na mapazi ake ndipo iye anawacilitsa.
31 Khamulo linadabwa kwambili poona kuti osalankhula akulankhula, othyoka ziwalo akukhala bwino, olemala akuyenda, komanso osaona akuona. Ndipo iwo anatamanda Mulungu wa Isiraeli.
32 Koma Yesu anaitana ophunzila ake n’kuwauza kuti: “Nikuwamvela cifundo anthuwa, cifukwa akhala nane masiku atatu osadya ciliconse. Sinifuna kuwauza kuti azipita na njala cifukwa angakomoke m’njila.”
33 Koma ophunzilawo anati: “Kodi tingapeze kuti cakudya cokwanila khamu lalikulu ngati ili kumalo opanda anthu kuno?”
34 Pamenepo Yesu anawafunsa kuti: “Muli na mitanda ingati ya mkate?” Iwo anati: “Tili nayo 7 na tunsomba toŵelengeka.”
35 Conco, anauza anthuwo kuti akhale pansi.
36 Ndiyeno anatenga mitanda 7 ija na tunsomba tuja n’kuyamika. Kenako ananyema-nyema mikateyo n’kuyamba kupatsa ophunzila ake pamodzi na tunsombato, ndipo iwo anagaŵila khamulo.
37 Onse anadya n’kukhuta, ndipo anatola-tola zotsala zokwana matadza 7 akulu-akulu.
38 Amene anadya anali amuna 4,000, osaŵelengelako akazi komanso ana.
39 Atauza anthuwo kuti azipita, anakwela bwato n’kupita ku cigawo ca Magadani.
Mawu a m'Munsi
^ Kutanthauza kusamba m’manja motsatila mwambo.
^ Kutanthauza kuti, “asawathandize.”
^ M’Cigiriki por nei’a. Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
^ Kutanthauza kusasamba m’manja motsatila mwambo.