Wolembedwa na Mateyo 16:1-28

  • Apempha cizindikilo (1-4)

  • Zofufumitsa za Afarisi na Asaduki (5-12)

  • Makiyi a Ufumu (13-20)

    • Mpingo udzamangidwa pa thanthwe (18)

  • Yesu anenelatu za imfa yake (21-23)

  • Zimene ophunzila oona a Yesu amacita (24-28)

16  Kenako Afarisi na Asaduki anafika kwa iye, ndipo pofuna kumuyesa anamupempha kuti awaonetse cizindikilo cocokela kumwamba.  Powayankha iye anati: “Pamene dzuŵa likuloŵa mumati, ‘Maŵa nyengo idzakhala bwino, cifukwa kumwamba kukuoneka psuu.’  Ndipo m’maŵa mumakamba kuti, ‘Lelo kuzizila, ndipo kugwa mvula, cifukwa kumwamba kukuoneka psuu koma kuli mitambo.’ Mumadziŵa kumasulila maonekedwe a kumwamba koma simungathe kumasulila zizindikilo za nthawi ino.  M’badwo woipa komanso wacigololo* ukufunabe cizindikilo, koma sudzapatsidwa cizindikilo ciliconse kupatulapo cizindikilo ca Yona.” Atakamba zimenezi anacokapo n’kuwasiya.  Tsopano ophunzila ake anawolokela ku tsidya lina koma anaiŵala kunyamula mkate.  Yesu anawauza kuti: “Khalani maso ndipo samalani na zofufumitsa za Afarisi na Asaduki.”  Conco anayamba kukambilana kuti: “Sitinanyamule mitanda ya mkate pobwela kuno.”  Yesu anadziŵa zimene anali kukambilana, ndipo anawafunsa kuti: “A cikhulupililo cocepa inu, n’cifukwa ciyani mukukambilana zakuti mulibe mitanda ya mkate?  Kodi simukumvetsetsabe zimene nikutanthauza, kapena simukukumbukila mitanda isanu ya mkate imene anadya anthu 5,000, komanso kuculuka kwa matadza a zotsala zimene munasonkhanitsa? 10  Kapenanso simukukumbukila mitanda ya mkate 7 imene anadya anthu 4,000, komanso kuculuka kwa matadza akulu-akulu a zotsala zimene munasonkhanitsa? 11  Nanga n’cifukwa ciyani simukuzindikila kuti sinikunena za mkate? Koma samalani na zofufumitsa za Afarisi na Asaduki.” 12  Apa lomba ophunzilawo anamvetsa kuti anali kuwauza kuti asamale na ziphunzitso za Afarisi na Asaduki, osati na zofufumitsa za mkate. 13  Yesu atafika m’cigawo ca Kaisareya wa ku Filipi, anafunsa ophunzila ake kuti: “Kodi anthu amati Mwana wa munthu ndani?” 14  Iwo anayankha kuti: “Ena amati ni Yohane M’batizi, ena Eliya, komanso ena amati ni Yeremiya kapena mmodzi wa aneneli.” 15  Iye anawafunsanso kuti: “Nanga inu mumati ndine ndani?” 16  Simoni Petulo anayankha kuti: “Ndinu Khristu Mwana wa Mulungu wamoyo.” 17  Kenako Yesu anamuuza kuti: “Ndiwe wodala Simoni mwana wa Yona, cifukwa si munthu wakuululila zimenezi koma ni Atate wanga wa kumwamba. 18  Komanso nikukuuza kuti: Iwe ndiwe Petulo, ndipo pa thanthwe ili nidzamangapo mpingo wanga. Mageti a Manda* sizidzaugonjetsa. 19  Ine nidzakupatsa makiyi a Ufumu wa kumwamba. Ndipo ciliconse cimene udzamange pano pa dziko lapansi, cidzakhala citamangidwa kale kumwamba. Komanso ciliconse cimene udzamasule pa dziko lapansi, cidzakhala citamasulidwa kale kumwamba.” 20  Ndiyeno analamula ophunzila ake mwamphamvu kuti asauze aliyense kuti iye ni Khristu. 21  Kuyambila nthawi imeneyo, Yesu anayamba kuuza ophunzila ake kuti ayenela kupita ku Yerusalemu. Kumeneko akazunzidwa m’njila zosiyana-siyana na akulu, ansembe aakulu, komanso alembi. Kenako adzaphedwa, ndipo pa tsiku lacitatu adzaukitsidwa. 22  Petulo atamva izi anatengela Yesu pambali n’kuyamba kumudzudzula kuti: “Dzikomeleni mtima Ambuye. Ndipo izi sizidzakucitikilani ayi.” 23  Koma Yesu anatembenuka n’kuuza Petulo kuti: “Pita kumbuyo kwanga Satana! Ndiwe copunthwitsa kwa ine, cifukwa zimene ukuganiza si maganizo a Mulungu koma maganizo a anthu.” 24  Kenako Yesu anauza ophunzila ake kuti: “Ngati munthu afuna kunitsatila adzikane yekha, na kunyamula mtengo wake wozunzikilapo* n’kupitiliza kunitsatila. 25  Pakuti aliyense wofuna kupulumutsa moyo wake adzautaya, koma aliyense wotaya moyo wake cifukwa ca ine adzaupeza. 26  Kunena zoona, kodi pali phindu lanji munthu atapeza zinthu zonse za m’dzikoli koma n’kutaya moyo wake? Kapena munthu angapeleke ciyani cosinthanitsa na moyo wake? 27  Pakuti Mwana wa munthu adzabwela mu ulemelelo wa Atate wake pamodzi na angelo ake, ndipo adzabwezela aliyense malinga na zocita zake. 28  Ndithu nikukuuzani kuti pali ena pano, amene sadzalaŵa imfa ngakhale pang’ono, mpaka coyamba ataona Mwana wa munthu akubwela mu Ufumu wake.”

Mawu a m'Munsi

Kapena kuti, “wosakhulupilika.”
Kapena kuti, “mphamvu za imfa.” Mawu ake enieni, “mageti a Hade.”