Wolembedwa na Mateyo 18:1-35

  • Wamkulu kwambili mu Ufumu wa kumwamba (1-6)

  • Zopunthwitsa (7-11)

  • Fanizo la nkhosa yosocela (12-14)

  • Mmene tingabwezele m’bale wathu (15-20)

  • Fanizo la kapolo wosakhululukila mnzake (21-35)

18  Pa nthawi imeneyo ophunzila a Yesu anabwela kwa iye n’kumufunsa kuti: “Ndani maka-maka wamkulu kwambili mu Ufumu wa kumwamba?”  Pamenepo iye anaitana mwana wamng’ono n’kumuimika pakati pawo,  ndipo anati: “Ndithu nikukuuzani kuti simudzaloŵa mu Ufumu wa kumwamba ngati simutembenuka* n’kukhala ngati ana aang’ono.  Aliyense amene adzadzicepetsa ngati mwana wamng’ono uyu, ndiye wamkulu kwambili mu Ufumu wa kumwamba;  ndipo aliyense wolandila mwana wamng’ono ngati uyu cifukwa ca dzina langa, walandilanso ine.  Koma aliyense wopunthwitsa mmodzi wa ana aang’ono awa amene ali na cikhulupililo mwa ine, cingakhale bwino kwambili kum’mangilila cimwala ca mphelo m’khosi cimene bulu amaguza na kum’miza m’nyanja.  “Tsoka dzikoli cifukwa ca zopunthwitsa zake! N’zoona kuti zopunthwitsa zidzabwela ndithu, koma tsoka kwa munthu wobweletsa copunthwitsaco!  Cotelo, ngati dzanja lako kapena phazi lako limakupunthwitsa, ulidule n’kulitaya. Ni bwino kuti ukapeze moyo ulibe ciwalo cimodzi kapena uli wolemala, kusiyana n’kuti ukaponyedwe m’moto wosatha uli na manja onse aŵili, kapena mapazi onse aŵili.  Komanso ngati diso lako limakupunthwitsa, ulikolowole n’kulitaya. Ni bwino kuti ukapeze moyo uli na diso limodzi, kusiyana n’kuti ukaponyedwe ku Gehena* wa moto uli na maso onse aŵili. 10  Samalani kuti musanyoze mmodzi wa ana aang’ono awa, cifukwa nikukuuzani kuti angelo awo kumwamba, nthawi zonse amayang’ana nkhope ya Atate wanga amene ali kumwamba. 11  —— 12  “Muganiza bwanji? Ngati munthu ali na nkhosa 100, ndipo imodzi mwa nkhosazo yasocela, kodi sangasiye nkhosa 99 zija m’phili n’kupita kukafuna-funa nkhosa imodzi yosocelayo? 13  Ndithu nikukuuzani kuti akaipeza amakondwela nayo kwambili kuposa nkhosa 99 zija zimene sizinasocele. 14  Mofanana na zimenezi, Atate wanga* wa kumwamba safuna kuti ngakhale mmodzi wa ana aang’ono awa awonongeke. 15  “Komanso ngati m’bale wako wakucimwila, pita ukamufotokozele colakwa cake* panokha muli aŵili. Ngati wakumvela ndiye kuti wamubweza m’bale wakoyo. 16  Koma ngati sanakumvele upiteko na munthu mmodzi kapena aŵili kuti nkhani yonse ikatsimikizike pamaso pa* mboni ziŵili kapena zitatu. 17  Ngati iye sanawamvelenso uuze mpingo. Koma ngati mpingo nawonso sanaumvele, kwa iwe akhale ngati munthu wocokela ku mtundu wina komanso wokhometsa misonkho. 18  “Ndithu nikukuuzani kuti zilizonse zimene mudzamanga pano pa dziko lapansi, zidzakhala zitamangidwa kale kumwamba, komanso zilizonse zimene mudzamasula pano pa dziko lapansi, zidzakhala zitamasulidwa kale kumwamba. 19  Komanso ndithu nikukuuzani kuti, ngati aŵili a inu pano padziko lapansi mwagwilizana kuti mupemphe cinacake cofunika, Atate wanga wa kumwamba adzakupatsani cimeneco. 20  Pakuti pomwe aŵili kapena atatu asonkhana m’dzina langa, inenso nimakhala pakati pawo.” 21  Kenako Petulo anabwela kwa Yesu n’kumufunsa kuti: “Ambuye, kodi m’bale wanga anganicimwile kangati ndipo ine n’kumukhululukila? Mpaka maulendo 7 kodi?” 22  Yesu anamuyankha kuti: “Nikukuuza kuti, osati maulendo 7 cabe ayi, koma mpaka maulendo 77. 23  “Ndiye cifukwa cake Ufumu wa kumwamba uli ngati mfumu imene inafuna kuti akapolo ake abweze nkhongole. 24  Atayamba kulandila nkhongolezo, atumiki ake anamubweletsela munthu wina amene anakongola matalente 10,000.* 25  Koma cifukwa cakuti sakanatha kubweza nkhongoleyo, mbuye wake analamula kuti munthuyo agulitsidwe pamodzi na mkazi wake, ana ake na zinthu zake zonse, kuti nkhongoleyo ibwezedwe. 26  Ndiyeno kapoloyo anagwada pansi ndipo anamuŵelamila n’kunena kuti, ‘Conde munilezeleko mtima, nidzakubwezelani zonse.’ 27  Mbuye wakeyo atamva zimenezi anamumvela cifundo, ndipo anamukhululukila nkhongole yake n’kumulola kuti apite. 28  Koma kapoloyo atatuluka, anakumana na kapolo mnzake amene anali na nkhongole yake yokwana madinari 100. Iye anamugwila na kuyamba kumukanyanga pakhosi, n’kumuuza kuti, ‘Nibwezele zonse zimene unakongola.’ 29  Pamenepo kapolo mnzakeyo anagwada pansi n’kuyamba kumucondelela kuti, ‘Conde munilezeleko mtima, nidzakubwezelani.’ 30  Koma sanalole zimenezo, ndipo anapita kukam’mangitsa kuti akakhale ku ndende mpaka atabweza nkhongole yonse. 31  Akapolo anzake ataona zimene zinacitikazo, anamva cisoni kwambili. Ndipo anapita kukafotokozela mbuye wawo zonse zimene zinacitika. 32  Ndiyeno mbuye wake uja anamuitana n’kumuuza kuti: ‘Kapolo woipa iwe! Ine n’nakukhululukila nkhongole yako yonse utanidandaulila. 33  Kodi iwenso sunayenele kumucitila cifundo kapolo mnzako, mmene ine n’nakucitila cifundo?’ 34  Pamenepo mbuye wakeyo anakwiya kwambili, moti anamupeleka kwa woyang’anila ndende kuti amuponye m’ndende mpaka atabweza nkhongole yonse. 35  Atate wanga wa kumwamba adzacitanso nanu cimodzimodzi, ngati aliyense wa inu sakhululukila m’bale wake na mtima wake wonse.”

Mawu a m'Munsi

Kapena kuti, “ngati simusintha.”
Kamasulidwe kena, “Atate wanu.”
Mawu ake enieni, “ukamudzudzule.”
Mawu ake enieni, “ikatsimikizike na pakamwa pa.”
Matalente 10,000 a siliva zinali ndalama zofanana na madinari 60,000,000.