Wolembedwa na Mateyo 19:1-30

  • Ukwati na cisudzulo (1-9)

  • Mphatso ya umbeta (10-12)

  • Yesu adalitsa ana (13-15)

  • Funso la mnyamata wacuma (16-24)

  • Kudzimana cifukwa ca Ufumu (25-30)

19  Yesu atatsiliza kulankhula zimenezi, anacoka ku Galileya n’kupita ku madela a kumalile kwa Yudeya, ku tsidya la Yorodani.  Khamu lalikulu la anthu linamutsatila, ndipo iye anawacilitsa kumeneko.  Ndiyeno Afarisi anabwela kwa iye, ndipo pofuna kumuyesa anamufunsa kuti: “Kodi n’kololeka mwamuna kusudzula mkazi wake pa cifukwa ciliconse?”  Yesu anayankha kuti: “Kodi simunaŵelenge kuti amene analenga anthu paciyambi anawalenga mwamuna na mkazi,  n’kunena kuti: ‘Pa cifukwa cimeneci, mwamuna adzasiya atate ake na amayi ake, n’kudziphatika kwa mkazi wake, ndipo aŵiliwo adzakhala thupi limodzi?  Conco iwo salinso aŵili koma thupi limodzi. Cotelo cimene Mulungu wacimanga pamodzi munthu asacilekanitse.”  Iwo anamufunsa kuti: “Nanga n’cifukwa ciyani Mose analamula kuti mwamuna azipeleka cikalata ca cisudzulo kwa mkazi wake n’kumuleka?”  Iye anawauza kuti: “Mose anakulolani kusudzula akazi anu cifukwa ca unkhutukumve wanu. Koma sizinali conco kucokela pa ciyambi.  Ine nikukuuzani kuti aliyense wosudzula mkazi wake, osati pa cifukwa ca ciwelewele,* n’kukwatila mkazi wina, wacita cigololo.” 10  Ndiyeno ophunzila ake anati: “Ngati umu ni mmene zilili pakati pa mwamuna na mkazi wake, cili bwino kusakwatila.” 11  Iye anawauza kuti: “Si anthu onse amene angathe kucita zimenezi, koma okhawo amene ali na mphatsoyo. 12  Pakuti ena sakwatila cifukwa anabadwa telo, ndipo ena sakwatila cifukwa anacita kufulidwa. Koma ena anasankha kukhala osakwatila cifukwa ca Ufumu wa kumwamba. Amene angathe kutelo acite zimenezi.” 13  Kenako anthu anamubweletsela ana aang’ono kuti awaike manja na kuwapemphelela, koma ophunzila ake anawadzudzula. 14  Komabe Yesu anawauza kuti: “Alekeni anawo abwele kwa ine musawaletse, cifukwa Ufumu wa kumwamba ni wa anthu ngati amenewa.” 15  Ndipo ataika manja ake pa iwo anacoka kumeneko. 16  Tsopano munthu wina anapita kwa iye n’kumufunsa kuti: “Mphunzitsi, n’ciyani cabwino cimene niyenela kucita kuti nikapeze moyo wosatha?” 17  Yesu anamuyankha kuti: “N’cifukwa ciyani ukunifunsa za cimene cili cabwino? Pali mmodzi yekhayo wabwino. Koma ngati ufuna kukapeza moyo wosatha, uzitsatila malamulo a Mulungu nthawi zonse.” 18  Iye anamufunsa kuti: “Malamulo ati?” Yesu anati: “Usaphe munthu, usacite cigololo, usabe, usapeleke umboni wonama, 19  uzilemekeza atate ako na amayi ako, komanso uzikonda mnzako mmene umadzikondela wekha.” 20  Mnyamatayo anayankha kuti: “Nakhala nikutsatila malamulo onsewa, nanga n’ciyaninso cina cimene nikupeleŵela?” 21  Yesu anamuuza kuti: “Ngati ufuna kukhala wangwilo,* pita ukagulitse zinthu zako ndipo ndalama zake ukapatse osauka. Ukatelo udzakhala na cuma kumwamba. Kenako ubwele udzakhale wotsatila wanga.” 22  Mnyamatayo atamva zimenezi, anacoka ali wacisoni cifukwa anali na katundu wambili. 23  Pamenepo Yesu anauza ophunzila ake kuti: “Ndithu nikukuuzani kuti cidzakhala covuta munthu wolemela kuloŵa mu Ufumu wa kumwamba. 24  Komanso nikukuuzani kuti n’cosavuta ngamila kuloŵa pa diso la singano, kusiyana n’kuti munthu wolemela akaloŵe mu Ufumu wa Mulungu.” 25  Ophunzilawo atamva zimenezi anadabwa kwambili, ndipo anati: “Ndiye pali amene angapulumuke ngati?” 26  Yesu anawayang’anitsitsa n’kuwauza kuti: “Kwa anthu izi n’zosathekadi, koma kwa Mulungu zonse n’zotheka.” 27  Ndiyeno Petulo poyankha anati: “Taonani! Ife tasiya zinthu zathu zonse n’kukutsatilani, kodi tidzapeza ciyani?” 28  Yesu anawauza kuti: “Ndithu nikukuuzani kuti pa nthawi ya kulenganso zinthu, pamene Mwana wa munthu adzakhala pa mpando wake wacifumu waulemelelo, inu amene mwanitsatila mudzakhala pa mipando 12 yacifumu, n’kumaweluza mafuko 12 a Isiraeli. 29  Ndipo aliyense amene wasiya nyumba, abale, alongo, atate, amayi, ana, kapena minda cifukwa ca dzina langa, adzalandila zoculuka kuwilikiza maulendo 100, komanso adzapeza moyo wosatha. 30  “Koma ambili amene ni oyamba adzakhala othela, ndipo othela adzakhala oyamba.

Mawu a m'Munsi

M’Cigiriki por nei’a. Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Kapena kuti “wokwanila.”