Wolembedwa na Mateyo 2:1-23

  • Okhulupilila nyenyezi apita kukaona Yesu (1-12)

  • Athaŵila ku Iguputo (13-15)

  • Herode akupha ana aamuna (16-18)

  • Abwelela ku Nazareti (19-23)

2  Yesu atabadwa ku Betelehemu wa ku Yudeya m’masiku a Herode mfumu, okhulupilila nyenyezi ocokela Kum’maŵa anabwela ku Yerusalemu.  Iwo anati: “Kodi mfumu ya Ayuda imene yabadwa ili kuti? Cifukwa tinaona nyenyezi yake pamene tinali Kum’maŵa, ndipo tabwela kuti tiiŵelamile.”  Mfumu Herode itamva zimenezi inavutika maganizo pamodzi na onse okhala mu Yerusalemu.  Kenako Herode anasonkhanitsa ansembe aakulu onse na alembi a anthu, n’kuwafunsa za kumene Khristu* adzabadwila.  Iwo anamuyankha kuti: “Ku Betelehemu wa Yudeya, pakuti izi n’zimene zinalembedwa kudzela mwa mneneli kuti:  ‘Ndipo iwe Betelehemu wa m’dziko la Yuda, sindiwe mzinda waung’ono kwambili pakati pa olamulila a Yuda, cifukwa mwa iwe mudzatuluka wolamulila amene adzaŵeta anthu anga Aisiraeli.’”  Ndiyeno Herode anaitanitsa okhulupilila nyenyezi aja mwamseli, na kuwafunsa mosamala kuti adziŵe nthawi yeniyeni imene nyenyeziyo inaonekela.  Powatumiza ku Betelehemu, iye anawauza kuti: “Pitani mukamufunefune mosamala mwanayo, ndipo mukakamupeza mudzabwelenso kudzaniuza, kuti inenso nikapite kukamuŵelamila.”  Atamva zimene mfumuyo inakamba, ananyamuka n’kumapita. Atanyamuka, nyenyezi ija imene anaiona ali Kum’maŵa inaonekelanso. Ndipo inayamba kuyenda kutsogolo kwawo mpaka inakaima pamwamba pa nyumba imene munali mwanayo. 10  Ataona kuti nyenyeziyo yaima anakondwela kwambili. 11  Pamene analoŵa m’nyumbamo, anamuona mwanayo ali na mayi ake Mariya, ndipo anagwada pansi na kumuŵelamila. Anamasulanso cuma cawo n’kumupatsa mphatso mwanayo. Anamupatsa golide, lubani na mule. 12  Koma popeza anacenjezedwa na Mulungu m’maloto kuti asabwelele kwa Herode, iwo anadzela njila ina pobwelela ku dziko lawo. 13  Iwo atacoka, mngelo wa Yehova anaonekela kwa Yosefe m’maloto n’kumuuza kuti: “Nyamuka, tenga mwanayu pamodzi na mayi ake uthaŵile ku Iguputo. Ukakhale kumeneko mpaka n’dzakuuze zocita, cifukwa Herode posacedwa adzayamba kufuna-funa mwanayu kuti amuphe.” 14  Conco Yosefe anauka usiku womwewo n’kutenga mwanayo na mayi ake kupita ku Iguputo. 15  Anakhalabe kumeneko mpaka pamene Herode anamwalila. Izi zinakwanilitsa mawu amene Yehova anakamba mwa mneneli wake, akuti: “N’naitana mwana wanga kuti atuluke mu Iguputo.” 16  Herode atazindikila kuti okhulupilila nyenyezi aja am’pusitsa, anakwiya koopsa. Conco anatumiza anthu kuti akaphe ana onse aamuna ku Betelehemu na m’madela onse ozungulila, kuyambila a zaka ziŵili kubwela pansi mogwilizana na nthawi imene okhulupilila nyenyezi aja anamuuza. 17  Izi zinakwanilitsa mawu amene ananenedwa kudzela mwa mneneli Yeremiya akuti: 18  “Mawu olila mokweza anamveka ku Rama. Anali Rakele kulila ana ake, ndipo sanafune kutonthozedwa cifukwa anawo kunalibenso.” 19  Herode atamwalila, mngelo wa Yehova anaonekela kwa Yosefe ku Iguputo 20  ndipo anati: “Nyamuka, tenga mwanayu pamodzi na mayi ake, ubwelele ku dziko la Isiraeli, cifukwa amene anali kufuna-funa moyo wa mwanayu anafa.” 21  Conco ananyamuka na kutenga mwanayo pamodzi na mayi ake, n’kupita ku dziko la Isiraeli. 22  Koma atamva kuti Arikelao ndiye akulamulila ku Yudeya, m’malo mwa Herode tate wake, anaopa kupita kumeneko. Kuwonjezela apo, atacenjezedwa na Mulungu kupitila m’maloto, anacoka n’kupita ku dela la Galileya. 23  Ndipo anapita kukakhala mu mzinda wa Nazareti. Izi zinakwanilitsa mawu amene ananenedwa kudzela mwa aneneli, akuti: “Iye adzachedwa Mnazareti.”*

Mawu a m'Munsi

Kapena kuti, “Mesiya; Wodzozedwa.”
Cioneka kuti dzinali linacokela ku liwu la Ciheberi lotanthauza kuti “mphukila.”