Wolembedwa na Mateyo 23:1-39

  • Musamatengele alembi na Afarisi (1-12)

  • Tsoka kwa alembi na Afarisi (13-36)

  • Yesu alilila Yerusalemu (37-39)

23  Tsopano Yesu analankhula na khamu la anthulo komanso ophunzila ake kuti:  “Alembi na Afarisi adzikhazika okha pa mpando wa Mose.  Conco, muzicita na kutsatila zonse zimene amakuuzani, koma musamatengele zimene iwo amacita, cifukwa amangonena koma sacita zimene amanenazo.  Iwo amamanga katundu wolema n’kumuika pa mapewa a anthu, koma iwowo safuna kumukankhako ngakhale na cala cawo.  Zonse zimene iwo amacita, amazicita kuti anthu awaone. Pakuti amakulitsa tumapukusi twa malemba tumene amavala monga zithumwa, ndiponso amatalikitsa ulusi wopota wa m’mbali mwa zovala zawo.  Iwo amakonda malo olemekezeka kwambili pa cakudya ca madzulo, komanso amakonda kukhala pa mipando ya kutsogolo* m’masunagoge.  Amakondanso kupatsidwa moni m’misika, komanso kuti anthu aziwachula kuti Mphunzitsi.*  Koma inu musamachedwe aphunzitsi, cifukwa Mphunzitsi wanu ni mmodzi, ndipo nonsenu ndinu abale.  Komanso musamachule aliyense kuti atate wanu pa dziko pano, cifukwa Atate wanu ni mmodzi, wa kumwamba Yekhayo. 10  Musamachedwenso atsogoleli, cifukwa Mtsogoleli wanu ni mmodzi, Khristu. 11  Koma wamkulu pakati panu akhale mtumiki wanu. 12  Aliyense wodzikweza adzatsitsidwa, ndipo aliyense wodzicepetsa adzakwezedwa. 13  “Tsoka inu alembi na Afarisi, onyenga inu! Cifukwa mumatsekela anthu khomo loloŵela mu Ufumu wa kumwamba. Pakuti inuyo simuloŵamo, ndiponso amene afuna kuloŵamo mumawaletsa. 14  —— 15  “Tsoka inu alembi na Afarisi, onyenga inu! Cifukwa mumayenda mitunda itali-itali pa nyanja komanso pa mtunda kuti mukatembenule munthu mmodzi. Ndipo munthuyo akatembenuka mumamupangitsa kukhala woyenelela kuponyedwa mu Gehena* kuwilikiza kaŵili kuposa inu. 16  “Tsoka inu atsogoleli akhungu amene mumati, ‘Ngati munthu walumbila kuti, “Pali kacisi,” zilibe kanthu. Koma ngati walumbila kuti, “Pali golide wa m’kacisi,” ayenela kukwanilitsa lumbilo lake.’ 17  Opusa komanso akhungu inu! Kodi cofunika kwambili n’ciyani, golide kapena kacisi amene wayeletsa golideyo? 18  Ndiponso mumati, ‘Ngati munthu walumbila kuti, “Pali guwa la nsembe,” zilibe kanthu. Koma ngati walumbila kuti, “Pali nsembe yomwe ili paguwapo,” ayenela kukwanilitsa lumbilo lake.’ 19  Akhungu inu! Kodi cofunika kwambili n’ciyani, nsembe kapena guwa la nsembe lomwe layeletsa nsembeyo? 20  Conco, aliyense wolumbila kuti, “Pali guwa la nsembe,” akulumbila pali guwalo komanso zonse zimene zili pomwepo. 21  Ndipo aliyense wolumbila kuti, “Pali kacisi,” akulumbila pali kacisiyo komanso pali Iye wokhala mmenemo. 22  Komanso aliyense wolumbila kuti, “Pali kumwamba,” akulumbila pali mpando wacifumu wa Mulungu ndiponso pali Iye wokhala pa mpandowo. 23  “Tsoka inu alembi na Afarisi, onyenga inu! Cifukwa mumapeleka cakhumi ca minti, dilili, na kumini,* koma mumanyalanyaza zinthu zofunika kwambili za m’Cilamulo, monga cilungamo, cifundo, na kukhulupilika. Kupeleka zinthu zimenezi n’kofunika, koma simuyenela kunyalanyaza zinthu zinazo. 24  Atsogoleli akhungu inu, amene mumasefa zakumwa zanu kuti mucotsemo kanyelele, koma mumameza ngamila! 25  “Tsoka inu alembi na Afarisi, onyenga inu! Cifukwa muli ngati kapu na mbale imene yayeletsedwa kunja, koma mkati mwake muli zonyansa. Mumtima mwanu ni modzala dyela* komanso kusadziletsa. 26  Mfarisi wakhungu iwe, coyamba yeletsa mkati mwa kapu na mbale kuti kunja kwakenso kukhale koyela. 27  “Tsoka inu alembi na Afarisi, onyenga inu! Cifukwa muli ngati manda opaka laimu, amene amaoneka okongola kunja koma mkati mwake ni modzala na mafupa a anthu akufa komanso zonyansa za mtundu uliwonse. 28  Ni mmenenso inu mulili. Pamaso pa anthu mumaoneka olungama, koma mumtima mwanu nimodzala cinyengo na kusamvela malamulo. 29  “Tsoka inu alembi na Afarisi, onyenga inu! Cifukwa mumamanga manda a aneneli na kukongoletsa manda* a anthu olungama. 30  Ndipo mumanena kuti, ‘Tikanakhalako m’masiku a makolo athu, sitikanatengako mbali pokhetsa magazi a aneneli.’ 31  Cotelo, mukudzicitila umboni wakuti ndinu ana a anthu amene anapha aneneliwo. 32  Conco, tsilizitsani nchito imene makolo anu anaiyamba. 33  “Njoka inu! ana a mphili, mudzathaŵa bwanji cilango ca Gehena?* 34  Pa cifukwa cimeneci, nikukutumizilani aneneli, anthu anzelu komanso aphunzitsi. Ena mudzawapha na kuwapacika pa mtengo. Ndipo ena mudzawakwapula m’masunagoge anu na kuwazunza mu mzinda na mzinda, 35  kuti magazi onse a anthu olungama amene anakhetsedwa pa dziko lapansi akhale pa inu. Kuyambila magazi a munthu wolungama Abele mpaka magazi a Zekariya mwana wa Barakiya, amene munamuphela pakati pa nyumba yopatulika na guwa la nsembe. 36  Ndithu nikukuuzani kuti zinthu zonsezi zidzaugwela m’badwo uwu. 37  “Yerusalemu, Yerusalemu, iwe wakupha aneneli komanso woponya miyala anthu otumidwa kwa iwe. Mobweleza-bweleza n’nafuna kusonkhanitsa pamodzi ana ako, monga mmene nkhuku imasonkhanitsila anapiye ake m’mapiko ake! Koma inu simunafune zimenezo. 38  Lomba mvelani! Mulungu wakusiyilani nyumba yanu.* 39  Pakuti nikukuuzani kuti kuyambila tsopano simudzanionanso, mpaka pamene mudzati, ‘Wodalitsika ni iye wobwela m’dzina la Yehova!’”

Mawu a m'Munsi

Kapena kuti, “yabwino kwambili.”
Kapena kuti, “Rabi.” M’Ciheberi, Rabi ni dzina laulemu la mphunzitsi waciyuda.
Minti, dilili, na kumini ni tomela tokometsela cakudya tumene anthu amalima.
Kapena kuti, “khalidwe lolanda zinthu.”
Kapena kuti, “manda acikumbutso.”
Kamasulidwe kena, “Nyumba yanu yasiidwa kwa inu ili bwinja.”