Wolembedwa na Mateyo 25:1-46

  • CIZINDIKILO CA KUKHALAPO KWA KHRISTU (1-46)

    • Fanizo la anamwali 10 (1-13)

    • Fanizo la matalente (14-30)

    • Nkhosa na mbuzi (31-46)

25  “Ufumu wa kumwamba uli ngati anamwali 10 amene anatenga nyale zawo n’kupita kukakumana na mkwati.  Anamwali asanu anali opusa, ndipo asanu enawo anali ocenjela.*  Opusawo anatenga nyale zawo, koma sanatenge mafuta owonjezela,  Koma ocenjelawo anatenga mafuta owonjezela m’mabotolo awo pamodzi na nyale zawo.  Popeza kuti mkwatiyo anacedwa, onse anayamba kukusila mpaka anagona.  Pakati pa usiku, kunamveka mawu ofuula akuti: ‘Mkwati uja wafika! Pitani mukamucingamile.’  Nthawi yomweyo anamwali onsewo anauka n’kuyamba kukonza nyale zawo.  Anamwali opusa aja anapempha ocenjelawo kuti, ‘Tipatsen’koni mafuta anu, cifukwa nyale zathu zatsala pang’ono kuzima.’  Koma ocenjelawo anayankha kuti: ‘Ayi, tikagaŵana mwina satikwanila tonse. Conco pitani kwa ogulitsa mukagule anu.’ 10  Pamene anali kupita kukagula mafutawo mkwati anafika. Ndipo anamwali amene anali okonzekawo analoŵa naye m’nyumba imene munali phwando la ukwati, ndipo citseko cinatsekedwa. 11  Pambuyo pake, anamwali ena aja nawonso anafika n’kunena kuti, ‘Ambuye, Ambuye, titsegulileni!’ 12  Poyankha iye anati, ‘Kukamba zoona, sinikudziŵani.’ 13  “Conco, khalanibe maso, cifukwa simudziŵa tsiku kapena ola lake. 14  “Pakuti zili ngati munthu amene anatsala pang’ono kupita ku dziko lina. Iye anaitana akapolo ake n’kuwasungiza cuma cake. 15  Kapolo woyamba anamupatsa matalente asanu,* waciŵili matalente aŵili, wacitatu talente imodzi. Aliyense anamupatsa malinga na luso lake. Kenako munthuyo anapita ku dziko lina. 16  Nthawi yomweyo amene analandila matalente asanu uja anapita kukacita nawo malonda, ndipo anapindula matalente enanso asanu. 17  Nayenso uja amene analandila matalente aŵili, anapindula enanso aŵili. 18  Koma amene analandila talente imodzi uja anapita kukakumba pansi, n’kubisa ndalama* ya mbuye wakeyo. 19  “Patapita nthawi yaitali mbuye wa akapolowo anabwela kuti aone zimene anacita na ndalamazo. 20  Conco, amene analandila matalente asanu uja, anabwela na matalente enanso asanu, n’kunena kuti, ‘Ambuye, munanisungiza matalente asanu. Koma onani napindula enanso asanu.’ 21  Mbuye wakeyo anamuuza kuti: ‘Wacita bwino, ndiwe kapolo wabwino komanso wokhulupilika! Wakhulupilika pa zinthu zocepa. Nidzakuika kuti uziyang’anila zinthu zambili. Sangalala pamodzi nane mbuye wako.’ 22  Kenako amene analandila matalente aŵili uja anabwela n’kunena kuti, ‘Ambuye, munanisungiza matalente aŵili, koma onani, napindula enanso aŵili.’ 23  Mbuye wakeyo anamuuza kuti: ‘Wacita bwino, ndiwe kapolo wabwino komanso wokhulupilika! Wakhulupilika pa zinthu zocepa. Nidzakuika kuti uziyang’anila zinthu zambili. Sangalala pamodzi nane mbuye wako.’ 24  “Pamapeto pake, kapolo amene analandila talente imodzi uja anabwela n’kunena kuti: ‘Ambuye, n’nali kudziŵa kuti ndinu munthu wovuta. Mumakolola kumene simunafese, na kututa tiligu kumene simunapepete. 25  Conco n’nacita mantha, ndipo n’napita kukabisa pansi talente ija. Aneni, tengani ndalama yanu.’ 26  Poyankha mbuye wakeyo anamuuza kuti: ‘Kapolo woipa komanso waulesi iwe, wati unali kudziŵa kuti nimakolola kumene sin’nafese, komanso nimatuta tiligu kumene sin’napepete? 27  Ndiye ukanacita bwino kusungiza ndalama yangayi kwa osunga ndalama.* Ndipo ine n’tafika, nikanailandila pamodzi na ciwongoladzanja cake. 28  “‘Cotelo mulandeni talenteyo, ndipo mupatse amene ali na matalente 10. 29  Pakuti aliyense amene ali nazo adzapatsidwa zambili, ndipo adzakhala na zoculuka. Koma amene alibe adzalandidwa ngakhale zimene ali nazo. 30  M’ponyeni kunja ku mdima kapolo wacabe-cabe ameneyu. Kumeneko azikalila na kukukuta mano.’ 31  “Mwana wa munthu akadzabwela mu ulemelelo wake, pamodzi na angelo onse, adzakhala pa mpando wake wacifumu waulemelelo. 32  Mitundu yonse ya anthu idzasonkhanitsidwa pamaso pake. Ndipo iye adzalekanitsa anthu mmene m’busa amalekanitsila nkhosa na mbuzi. 33  Ndipo adzaika nkhosa ku dzanja lake lamanja, koma mbuzi adzaziika kumanzele kwake. 34  “Ndiyeno Mfumu idzauza okhala ku dzanja lake lamanja kuti: ‘Bwelani inu amene mwadalitsidwa na Atate wanga. Loŵani mu Ufumu umene unakonzedwela inu kucokela pa kukhazikitsidwa kwa dziko. 35  Pakuti nitamva njala munanipatsa cakudya. Nitamva ludzu munanipatsa madzi. Ndipo pamene n’nali mlendo munanilandila bwino. 36  N’nali wamalisece* koma inu munaniveka. N’tadwala munanisamalila. N’nali m’ndende ndipo inu munabwela kudzaniona.’ 37  Ndiyeno olungamawo adzamuyankha kuti: ‘Ambuye, kodi ni liti pomwe tinakuonani muli na njala ife n’kukupatsani cakudya, kapena muli na ludzu ife n’kukupatsani madzi? 38  Ni liti pomwe tinakuonani muli mlendo, ife n’kukulandilani bwino, kapena muli wamalisece ife n’kukuvekani? 39  Ni liti pomwe munali kudwala kapena pomwe munali m’ndende, ife n’kubwela kudzakuonani?’ 40  Poyankha Mfumuyo idzawauza kuti, ‘Ndithu nikukuuzani kuti, ciliconse cimene munacitila mmodzi wa abale anga aang’ono awa, munacitila ine amene.’ 41  “Ndiyeno adzauza aja okhala ku dzanja lake lamanzele kuti: ‘Cokani pamaso panga inu otembeleledwa. Pitani ku moto wosatha umene anausonkhela Mdyelekezi na ziŵanda zake. 42  Pakuti n’tamva njala simunanipatse cakudya, ndipo n’tamva ludzu simunanipatse madzi. 43  N’nali mlendo koma simunanilandile bwino. N’nali wamalisece koma simunaniveke. N’nali kudwala komanso n’nali m’ndende koma simunanisamalile.’ 44  Pamenepo iwonso adzayankha kuti: ‘Ambuye, ni liti pomwe tinakuonani muli anjala kapena aludzu, kapena muli mlendo kapena muli wamalisece, kapena mukudwala kapenanso muli m’ndende, koma ife osakutumikilani?’ 45  Poyankha Mfumuyo idzawauza kuti: ‘Ndithu nikukuuzani kuti, ciliconse cimene simunacitile mmodzi wa aang’ono awa, simunacitile ine amene.’ 46  Amenewa adzawonongedwa kothelatu,* koma olungama adzalandila moyo wosatha.”

Mawu a m'Munsi

Kapena kuti, “anzelu.”
Talente ya Agiriki inali yolemela makilogilamu 20.4.
Mawu ake enieni, “siliva.”
Mawu ake enieni, “siliva.”
Kapena kuti, “wosavala mokwanila.”
Mawu ake enieni, “adzadulidwa; adzasadzidwa.”