Wolembedwa na Mateyo 27:1-66
27 Kutaca m’maŵa, ansembe aakulu onse na akulu anakambilana na kugwilizana zakuti amuphe Yesu.
2 Atam’manga, anapita kukam’peleka kwa bwanamkubwa Pilato.
3 Ndiyeno Yudasi womupeleka uja ataona kuti Yesu waweluzidwa kuti aphedwe, anadzimvela cisoni kwambili, ndipo anapita kukabweza ndalama 30 zasiliva zija kwa ansembe aakulu komanso akulu.
4 Iye anati: “N’nacimwa cifukwa copeleka munthu wosalakwa.” Iwo anamuyankha kuti: “Izo n’zako!* Ife sizitikhudza!”
5 Conco iye anangoponya ndalama zasiliva zija m’kacisi n’kucoka. Kenako anapita kukadzimangilila.
6 Koma ansembe aakuluwo anatenga ndalama zasiliva zija n’kunena kuti: “Si kololeka kuika ndalamazi mosungila cuma copatulika, cifukwa ni malipilo a magazi.”
7 Pambuyo pokambilana, iwo anatenga ndalamazo na kukagulila munda wa woumba mbiya kuti ukhale manda a alendo.
8 Conco, munda umenewo wakhala ukuchedwa Munda wa Magazi mpaka lelo.
9 Izi zinakwanilitsa mawu amene ananenedwa kupitila mwa mneneli Yeremiya akuti: “Ndipo iwo anatenga ndalama 30 zasiliva, mtengo umene iwo anaika pa munthuyo, malipilo amene ena mwa ana a Isiraeli anagwilizana kugulila munthuyo.
10 Ndipo ndalamazo anagulila munda wa woumba mbiya, malinga na zimene Yehova ananilamula.”
11 Tsopano Yesu anaimilila pamaso pa bwanamkubwa, ndipo bwanamkubwayo anamufunsa kuti: “Kodi ndiwe Mfumu ya Ayuda?” Yesu anayankha kuti: “Mwanena nokha zimenezi.”
12 Koma pamene ansembe aakulu na akulu anali kumuneneza, iye sanayankhe ciliconse.
13 Ndiyeno Pilato anamufunsa kuti: “Kodi sukumva zonsezi zimene akukuneneza?”
14 Koma Yesu sanamuyankhe ciliconse. Anangokhala duu, moti bwanamkubwayo anadabwa kwambili.
15 Pa cikondwelelo ciliconse, bwanamkubwayo anali na cizoloŵezi comasulila anthu mkaidi mmodzi amene iwo afuna.
16 Pa nthawiyi anali kusunga mkaidi wina woopsa kwambili, dzina lake Baraba.
17 Cotelo iwo atasonkhana pamodzi, Pilato anawafunsa kuti: “Kodi mufuna nikumasulileni ndani, Baraba kapena Yesu, amene anthu amamucha Khristu?”
18 Pakuti Pilato anali kudziŵa kuti iwo anamupeleka cifukwa ca kaduka.
19 Komanso atakhala pa mpando woweluzila milandu, mkazi wake anamutumizila uthenga wakuti: “Nkhani ya munthu wolungamayu isakukhudzeni, cifukwa navutika kwambili m’maloto lelo kaamba ka munthu ameneyu.”
20 Koma ansembe aakulu komanso akulu analimbikitsa khamu la anthulo kupempha kuti Baraba amasulidwe ndipo Yesu aphedwe.
21 Conco, bwanamkubwa uja anawafunsa kuti: “Kodi mufuna nikumasulileni ndani pa aŵiliwa?” Iwo anayankha kuti: “Baraba!”
22 Pilato anawafunsanso kuti: “Nanga nicite naye ciyani Yesu, amene anthu amamucha kuti Khristu?” Anthu onsewo anayankha kuti: “Apacikidwe!”*
23 Iye anati: “Cifukwa ciyani? Walakwanji?” Koma m’pamene anthuwo anafuula mwamphamvu kuti: “Apacikidwe ndithu!”
24 Pilato ataona kuti sizikuthandiza, koma cipolowe cifuna kuyamba, anatenga madzi na kusamba m’manja khamulo likuona n’kunena kuti: “Nilibe mlandu wa magazi a munthu uyu. Zonse zili kwa inu.”
25 Pamenepo anthu onsewo anayankha kuti: “Magazi ake akhale pa ife komanso pa ana athu!”
26 Basi Pilato anawamasulila Baraba, koma analamula kuti Yesu akwapulidwe. Kenako anamupeleka kuti akaphedwe pa mtengo.
27 Ndiyeno asilikali a bwanamkubwa anatenga Yesu n’kupita naye ku nyumba kwa bwanamkubwayo, ndipo anasonkhanitsa asilikali onse n’kumuzungulila.
28 Ndiyeno anamuvula zovala n’kumuveka cinsalu cofiila kwambili.
29 Kenako analuka cisoti cacifumu caminga n’kumuveka kumutu, komanso anam’patsa bango m’dzanja lake lamanja. Ndipo anamugwadila n’kuyamba kukamba momunyodola kuti: “Moni,* inu Mfumu ya Ayuda!”
30 Iwo anamuthila mata. Kenako anatenga bangolo n’kuyamba kumumenya nalo pamutu.
31 Pambuyo, pomucita zacipongwezo, anamuvula cinsalu cija n’kumuveka zovala zake zakunja, ndipo anapita naye kukam’khomelela pa mtengo.
32 Pamene anali kupita, anakumana na munthu wina wa ku Kurene, dzina lake Simoni. Iwo analamula munthuyo kuti anyamule mtengo wozunzikilapo* wa Yesu.
33 Ndipo atafika pa malo ochedwa Gologota, kutanthauza Malo a Cigoba,
34 anamupatsa vinyo wosakaniza na ndulu* kuti amwe. Koma ataulaŵa, anakana kumwa.
35 Iwo atamukhomelela pa mtengo, anagaŵana zovala zake zakunja mwa kucita maele,
36 ndipo anakhala pansi pomwepo n’kumamulonda.
37 Komanso pamwamba pa mutu wake anakhomapo cikwangwani coonetsa mlandu umene anamuimba. Analembapo kuti: “Uyu ni Yesu Mfumu ya Ayuda.”
38 Ndiyeno acifwamba aŵili anapacikidwa pafupi naye, mmodzi ku dzanja lake lamanja, wina kumanzele kwake.
39 Ndipo anthu opita m’njila anali kumunena monyoza n’kumapukusa mitu yawo.
40 Iwo anali kunena kuti: “Iwe amene unali kunena kuti ukhoza kugwetsa kacisi n’kumumanga m’masiku atatu cabe, dzipulumutse! Ngati ndiwedi mwana wa Mulungu, tsika pa mtengo wozunzikilapowo!”*
41 Nawonso ansembe aakulu pamodzi na alembi komanso akulu anayamba kumunyodola n’kumanena kuti:
42 “Anali kupulumutsa ena, koma cam’kanga kuti adzipulumutse yekha. Ngati iye ni Mfumu ya Aisiraeli atsike pa mtengo wozunzikilapowo* tione, ndipo tidzam’khulupilila.
43 Iye amakhulupilila Mulungu. Amupulumutse tione ngati afuna kum’thandiza, cifukwa anali kunena kuti, ‘Ndine Mwana wa Mulungu.’”
44 Nawonso acifwamba amene anapacikidwa pa mitengo pafupi naye anali kumunyoza.
45 Kuyambila ca m’ma 12 koloko masana,* m’dziko lonselo munacita mdima mpaka ca m’ma 3 koloko masana.*
46 Ca m’ma 3 koloko momwemo, Yesu anafuula mokweza kuti: “Eli, Eli, lama sabakitani?” kutanthauza kuti, “Mulungu wanga, Mulungu wanga, n’cifukwa ciyani mwanilekelela?”
47 Atamva zimenezi, ena mwa amene anaimilila pamenepo anayamba kunena kuti: “Munthu uyu akuitana Eliya.”
48 Nthawi yomweyo mmodzi wa iwo anathamanga kukatenga cinkhupule n’kuciviika mu vinyo wowawasa. Kenako anaciika ku bango na kum’patsa kuti amwe.
49 Koma enawo ananena kuti: “Mulekeni! Tione ngati Eliyayo abwela kudzam’pulumutsa.”
50 Yesu anafuulanso mokweza, kenako anatsilizika.*
51 Nthawi yomweyo, cinsalu cochinga ca m’nyumba yopatulika cinang’ambika pakati, kucokela pamwamba mpaka pansi, ndipo dziko linagwedezeka komanso matanthwe anang’ambika.
52 Manda* anatseguka, moti mitembo yambili ya anthu oyela amene anaikidwa mmenemo, inaponyedwa kunja,
53 ndipo inaonekela kwa anthu ambili. (Yesu ataukitsidwa, anthu amene anali kubwela kucokela ku mandawo analoŵa mu mzinda woyela).
54 Koma kapitawo wa asilikali, na aja amene anali naye polonda Yesu, ataona civomezico na zimene zinali kucitika, anacita mantha kwambili ndipo anati: “Ameneyu analidi Mwana wa Mulungu.”
55 Komanso azimayi ambili anali kumeneko, ndipo anali kuona capatali. Iwo anali atatsatila Yesu pamene iye anali kucoka ku Galileya kuti azim’tumikila.
56 Ena mwa iwo anali Mariya Mmagadala, Mariya mayi wa Yakobo na Yose, komanso mayi wa Yakobo na Yohane.*
57 Ndiyeno madzulo, kunabwela munthu wina wacuma wa ku Arimateya, dzina lake Yosefe. Nayenso anali atakhala wophunzila wa Yesu.
58 Iye anapita kwa Pilato kukapempha mtembo wa Yesu. Pilato analamula kuti amupatse mtembowo.
59 Yosefe anatenga mtembowo n’kuukulunga m’nsalu yoyela komanso yabwino kwambili,
60 ndipo anapita kukauika m’manda* ake atsopano, amene anali atagoba m’thanthwe. Kenako anatseka pa khomo la mandawo* mwa kugubuduzilapo cimwala cacikulu. Pambuyo pake anacoka.
61 Koma Mariya Mmagadala na Mariya wina uja anakhalabe komweko. Iwo anakhala pansi pafupi na mandawo.
62 Tsiku lotsatila, pambuyo pa tsiku la Cikonzekelo, ansembe aakulu komanso Afarisi anasonkhana pamodzi pamaso pa Pilato
63 na kunena kuti: “Bwana, tikumbukila kuti munthu wonyenga uja akali moyo ananena kuti, ‘Pambuyo pa masiku atatu, nidzauka.’
64 Conco lamulani kuti pamandapo pakhale citetezo cokhwima kufikila tsiku lacitatu, kuti ophunzila ake asapite kukamuba n’kumauza anthu kuti, ‘Anauka kwa akufa!’ Ngati izi zingacitike, ndiye kuti cinyengo cothelaci cidzakhala coipa kwambili kuposa coyamba cija.”
65 Pilato anawauza kuti: “Tengani asilikali olonda. Pitani mukakhwimitse citetezo mmene mudziŵila.”
66 Conco iwo anapita kukakhwimitsa citetezo pamandapo mwa kumata pa khomo la mandawo, pomwe panali potseka na cimwala na kuikapo asilikali olonda.
Mawu a m'Munsi
^ Kapena kuti, “Ilo ni vuto lako.”
^ Kapena kuti, “akaphedwe pa mtengo!”
^ Kapena kuti, “Mutamandike.”
^ Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
^ Apa, mawu akuti “ndulu” angatanthauze zinazake zamadzimadzi zoŵaŵa.
^ Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
^ Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
^ Mawu ake enieni, “ola la 6.”
^ Mawu ake enieni, “ola la 9.”
^ Kapena kuti, “anapeleka mzimu wake.”
^ Kapena kuti, “manda acikumbutso.”
^ Mawu ake enieni, “mayi wa ana a Zebedayo.”
^ Kapena kuti, “m’manda acikumbutso.”
^ Kapena kuti, “manda acikumbutsowo.”