Wolembedwa na Mateyo 28:1-20
28 Pambuyo pa tsiku la Sabata, m’matandakuca pa tsiku loyamba la mlunguwo, Mariya Mmagadala na Mariya wina uja anapita kukaona mandawo.
2 Ndipo panali patacitika civomezi camphamvu, cifukwa mngelo wa Yehova anali atatsika kumwamba na kubwela kudzagubuduzila kumbali cimwalaco n’kukhalapo.
3 Maonekedwe ake anali owala ngati mphenzi, ndipo zovala zake zinali zoyela mbee!
4 Cifukwa coopa mngeloyo, alondawo ananjenjemela, ndipo anauma gwa ngati akufa!
5 Koma mngeloyo anauza azimayi aja kuti: “Musacite mantha cifukwa nidziŵa kuti mukufuna Yesu, amene anamuphela pa mtengo.
6 Iye sali kuno cifukwa wauka kwa akufa, monga ananenela. Bwelani muone pamene panali mtembo wake.
7 Ndiyeno pitani mwamsanga mukauze ophunzila ake kuti iye wauka kwa akufa, ndipo watsogola kupita ku Galileya. Mukamuona kumeneko. Musaiŵale zimene nakuuzani.”
8 Nthawi yomweyo, azimayiwo anacoka pa mandapo ali na mantha komanso cisangalalo cosaneneka. Ndipo anathamanga kukauza ophunzila ake zimenezi.
9 Mwadzidzidzi Yesu anakumana nawo n’kunena kuti, “Moni azimayi!” Iwo anafika pafupi na iye. Ndiyeno anagwada na kugwila mapazi ake n’kumuŵelamila.
10 Kenako Yesu anawauza kuti: “Musacite mantha! Pitani mukauze abale anga kuti apite ku Galileya, ndipo akaniona kumeneko.”
11 Ali m’njila, ena mwa asilikali olonda aja anapita mu mzinda kukafotokozela ansembe aakulu zonse zimene zinacitika.
12 Ansembe aakuluwo anakumana pamodzi na akulu n’kukambilana nkhaniyo. Kenako anapeleka ndalama zambili zasiliva kwa asilikaliwo
13 n’kuwauza kuti: “Muzinena kuti, ‘Ophunzila ake anabwela usiku n’kuba mtembo wake ife tili mtulo.’
14 Ndipo bwanamkubwa akamva za nkhaniyi, tikamba naye.* Inu musade nkhawa.”
15 Conco, anatenga ndalama zasilivazo n’kucita mmene anawalangizila, ndipo nkhaniyi yakhala yofala pakati pa Ayuda mpaka lelo.
16 Koma ophunzila 11 aja anapita ku Galileya, ku phili, kumene Yesu anawauza kuti akakumane.
17 Atamuona, anamugwadila, koma ena anakayikila ngati analidi Yesu.
18 Yesu anafika pafupi n’kuwauza kuti: “Ulamulilo wonse wapelekedwa kwa ine, kumwamba na padziko lapansi.
19 Conco pitani mukapange anthu a mitundu yonse kuti akhale ophunzila. Muziwabatiza m’dzina la Atate, la Mwana, komanso la mzimu woyela,
20 na kuwaphunzitsa kusunga zinthu zonse zimene n’nakulamulani. Ndipo dziŵani kuti ine nili nanu pamodzi masiku onse mpaka cimalizilo ca nthawi ino.”*