Wolembedwa na Mateyo 3:1-17

  • Ulaliki wa Yohane M’batizi (1-12)

  • Ubatizo wa Yesu (13-17)

3  M’masiku amenewo, Yohane M’batizi anapita ku cipululu ca Yudeya, na kuyamba kulalikila.  Anali kulalikila kuti: “Lapani, cifukwa Ufumu wa kumwamba wayandikila.”  Mneneli Yesaya anali kukamba za ameneyu pamene anati: “Winawake akufuula m’cipululu kuti: ‘Konzani njila ya Yehova! Wongolani misewu yake.’”  Yohane anali kuvala covala caubweya wa ngamila na lamba wacikumba m’ciuno mwake. Cakudya cake cinali dzombe na uci.  Pa nthawiyo, anthu a mu Yerusalemu na mu Yudeya yense, komanso a m’madela onse ozungulila Yorodani anali kupita kwa iye.  Iye anali kuwabatiza* mu mtsinje wa Yorodani, ndipo iwo anali kuulula macimo awo poyela.  Yohane ataona kuti Afarisi na Asaduki ambili akubwela ku ubatizowo, anawauza kuti: “Ana a njoka inu, ndani wakucenjezani kuti muthaŵe mkwiyo umene ukubwela?  Conco balani zipatso zoonetsa kulapa.  Musadzinamize n’kumati, ‘Tili na Abulahamu atate wathu.’ Pakuti nikukuuzani kuti Mulungu angathe kusandutsa miyala iyi kukhala ana a Abulahamu. 10  Nkhwangwa yaikidwa kale ku mizu ya mitengo. Cotelo mtengo uliwonse wosabala zipatso zabwino udulidwa na kuponyedwa pa moto. 11  Ine nikukubatizani na madzi cifukwa mwalapa. Koma amene akubwela pambuyo panga ni wamphamvu kuposa ine, ndipo sindine woyenela kumuvula nsapato. Ameneyo adzakubatizani na mzimu woyela komanso moto. 12  Fosholo yake youluzila ili m’manja mwake. Iye adzayeletsa kothelatu malo ake opunthila mbewu. Ndipo tiligu adzamututila m’nkhokwe, koma mankhusu* adzawatentha pamoto wosazimitsika.” 13  Kenako Yesu anacoka ku Galileya n’kupita kwa Yohane ku Yorodani kuti akamubatize. 14  Koma Yohaneyo anayesa kumuletsa, amvekele: “Ndine amene niyenela kubatizidwa na inu, nanga bwanji inu mukubwela kwa ine?” 15  Yesu anamuyankha kuti: “Lola kuti zikhale telo pa nthawi ino, cifukwa kucita zimenezi n’koyenela kwa ife kuti tikwanilitse cilungamo conse.” Atatelo, analeka kumuletsa. 16  Yesu atabatizidwa, nthawi yomweyo anavuuka m’madzimo. Atavuuka, kumwamba kunatseguka, ndipo Yohane anaona mzimu wa Mulungu ukutsika ngati nkhunda kudzatela pa iye. 17  Kumwamba kunamvekanso mawu akuti: “Uyu ndiye mwana wanga wokondeka, amene nimakondwela naye.”

Mawu a m'Munsi

Kapena kuti, “kuwaviika; kuwamiza.”
“Mankhusu” ni makoko amene amacotsa ku mbewu monga mpunga akapuntha, ndipo amatha kuwauluza.